Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kutumikira Yehova ‘M’masiku Oipa’

Pitirizani Kutumikira Yehova ‘M’masiku Oipa’

M’BALE wina dzina lake Ernst * ali ndi zaka za m’ma 70 ndipo anadandaula kuti: “Thupi langa likufookafookabe.” Mwina nanunso muli ndi vuto lomweli. Ngati ndinu wachikulire ndipo mukuona kuti mukufooka ndiye kuti mungamvetse bwino mavuto otchulidwa pa Mlaliki chaputala 12. Paja vesi 1 imanena kuti masiku a ukalamba ndi “masiku oipa.” Koma sikuti zinthu zaipiratu. N’zotheka kutumikirabe Yehova mosangalala.

MUZILIMBITSABE CHIKHULUPIRIRO CHANU

Dziwani kuti atumiki akale a Yehova ankakumananso ndi mavuto a ukalamba ngati anu. Mwachitsanzo, Isaki, Yakobo ndiponso Ahiya anasiya kuona. (Gen. 27:1; 48:10; 1 Maf. 14:4) Sara anaona kuti ‘watheratu.’ (Gen. 18:11, 12) Mfumu Davide ankangokhalira kuzizidwa. (1 Maf. 1:1) Munthu wina wachuma dzina lake Barizilai anasiya kumva kukoma kwa chakudya kapena nyimbo. (2 Sam. 19:32-35) Abulahamu anavutika kwambiri mkazi wake atamwalira. Nayenso Naomi anakumana ndi vuto lomweli mwamuna wake atamwalira.—Gen. 23:1, 2; Rute 1:3, 12.

N’chiyani chinawathandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kutumikira Yehova mosangalala? Abulahamu anali wachikulire koma ankakhulupirirabe malonjezo a Mulungu “ndipo chikhulupiriro chakecho chinamulimbitsa.” (Aroma 4:19, 20) Nafenso timafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Chikhulupiriro chimenechi sichidalira msinkhu wathu, luso lathu kapena mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Mwachitsanzo, pamene Yakobo anasiya kuona, kuyenda ndiponso anali wofooka ankakhulupirirabe malonjezo a Mulungu. (Gen. 48:1-4, 10; Aheb. 11:21) Mlongo wina wazaka 93 dzina lake Ines ali ndi matenda amene amamuchititsa kufooka kwambiri koma anati: “Tsiku lililonse ndimaona kuti Yehova akundidalitsa. Ndimaganizira kwambiri za Paradaiso ndipo izi zimandithandiza kukhala wosangalala.” Mlongoyu ndi chitsanzo chabwino kwambiri.

Kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kupezeka pa misonkhano kungatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Mneneri Danieli atakalamba ankapemphera katatu pa tsiku ndiponso kuphunzira Mawu a Mulungu. (Dan. 6:10; 9:2) Pamene Anna anali wachikulire ndiponso wamasiye, “sanali kusowa pakachisi.” (Luka 2:36, 37) Ngati mungakwanitse, mungachite bwino kufika pa misonkhano ndiponso kuyankha. Izi zidzakulimbikitsani ndiponso kulimbikitsa Akhristu anzanu. Dziwani kuti Yehova amasangalala kwambiri ndi mapemphero anu ngakhale kuti simungachite zambiri pomutumikira.—Miy. 15:8.

Muzilimbikitsana ndi anzanu

Achikulire ambiri amalakalaka kuwerenga ndiponso kufika pa misonkhano. Koma mwina zimawavuta ndipo nthawi zina sizitheka n’komwe. Ngati zili choncho, ndi bwino kuti azingochita zimene angakwanitse. Achikulire ambiri amene sakwanitsa kufika ku misonkhano amamvetsera kudzera pafoni. Mlongo wina wazaka 79 dzina lake Inge amavutika kuona. Koma m’bale wina amamusindikizira zinthu za zilembo zazikulu kuti azigwiritsa ntchito pokonzekera misonkhano.

N’kutheka kuti achikulire ambiri amakhala ndi nthawi yambiri kusiyana ndi anthu ena. Ngati zili choncho ndi inuyo, mungachite bwino kugwiritsa ntchito nthawiyi pomvetsera zinthu zojambulidwa monga Baibulo, mabuku, nkhani kapena masewero. Mungachitenso bwino kuimbira foni Akhristu anzanu kuti ‘muzilimbikitsana.’—Aroma 1:11, 12.

MUZICHITA ZIMENE MUNGATHE POTUMIKIRA YEHOVA

Muzilalikira

Mlongo wina wazaka zoposa 80 dzina lake Christa anati: “Ukamalephera kuchita zimene unkakwanitsa kale zimapweteka kwambiri.” Ndiyeno n’chiyani chingathandize achikulirewa kukhala osangalala? M’bale wina wazaka 75 dzina lake Peter anati: “Muyenera kuganizira zimene mungakwanitse kuchita osati zimene mukulephera.”

Yesetsani kuganizira zinthu zina zimene mungachite kuti mulalikire. Mwachitsanzo, mlongo wina wazaka zoposa 80 dzina lake Heidi, sangathe kulalikira kunyumba ndi nyumba. Koma iye anaphunzira kugwiritsa ntchito kompyuta. Anachita izi kuti azilalikira pogwiritsa ntchito makalata. Achikulire ena amapita kumene kuli anthu ambiri ndipo amakhala pampando n’kumalalikira anthu odutsa. Mukhozanso kulalikira anthu okhala nawo pafupi kapena amene amabwera kudzakuonani.

Muzilandira bwino anthu

Mfumu Davide atakalamba anachita zimene akanatha potumikira Yehova. Iye anapereka ndalama zambiri zothandiza kuti kachisi amangidwe. (1 Mbiri 28:11–29:5) Yesetsani kudziwa zimene zikuchitika m’gulu la Yehova n’kuona zomwe mungachite pothandiza. Mwachitsanzo, mukhoza kuthandiza apainiya kapena ofalitsa ena akhama mumpingo wanu. Mungawauze mawu olimbikitsa, kuwapatsa kamphatso kapena kachakudya. Mungachitenso bwino kupempherera achinyamata, mabanja, atumiki a nthawi zonse, anthu odwala ndiponso amene ali ndi maudindo m’gulu la Yehova.

Inuyo ndiponso zimene mumachita potumikira Mulungu ndi zamtengo wapatali. Yehova sadzakusiyani kapena kukutayani. (Sal. 71:9) Iye amakukondani ndipo amaona kuti ndinu ofunika kwambiri. Musaiwale kuti posachedwapa mavuto a ukalamba adzatha. Tonsefe tidzakhala anthu angwiro komanso amphamvu n’kumatumikira Yehova mpaka muyaya.

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.