Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Tsopano Ndili pa Mtendere ndi Mulungu Komanso Amayi Anga

Tsopano Ndili pa Mtendere ndi Mulungu Komanso Amayi Anga

TSIKU lina, mayi anga ananena kuti: “N’chifukwa chiyani ukukana kulambira makolo athu akale? Kodi sukudziwa kuti iwowo ndi amene anakupatsa moyo? Zoona sukufuna kuyamikira zimene anakuchitirazi? Ukamakana kuwalambira ndiye kuti ukutanthauza kuti zimene timapangazi ndi zopanda nzeru. Ukuganiza kuti ndi bwino kusiya kuchita zimene makolo athu onse akhala akuchita?” Kenako mayi angawa anayamba kulira.

Aka kanali koyamba kuti mayi andilankhule chonchi. Nthawi zonse ndinkawamvera koma pa tsikuli sindikanatha kutsatira malangizo awowa chifukwa ndinkafuna kusangalatsa Yehova. Zinali zovuta kwambiri, koma Yehova anandithandiza. Miyezi ingapo izi zisanachitike, a Mboni ena anafunsa mayi anga ngati angakonde kuphunzira Baibulo. Mayi sankafuna kuphunzira koma poopa kuwakhumudwitsa anandiuza ineyo kuti ndiziphunzira nawo.

NDINASANKHA KUTI NDIYAMBE KUTUMIKIRA YEHOVA

Anthu ambiri ku Japan ndi achipembedzo chachibuda. Banja lathu linalinso m’chipembedzo chomwechi. Koma nditangophunzira ndi Mboni za Yehova kwa miyezi iwiri yokha, ndinadziwa kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona. Nditaphunzira kuti Mulungu ndi Atate wathu wakumwamba, ndinkafunitsitsa kuti ndimudziwe bwino. Poyamba, ndinkakonda kukambirana ndi mayi zimene ndaphunzira. Kenako ndinayamba kupita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu Lamlungu lililonse. Ndiyeno nditaphunzira zambiri m’Baibulo, ndinauza mayi anga kuti sindizichitanso nawo miyambo yachibuda. Koma mayi anakwiya kwambiri ndipo anati: “Munthu akasiya kulemekeza makolo akale amachititsa manyazi banja lake.” Anandiuza kuti ndisiye kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana. Ndinadabwa kwambiri chifukwa sindinayembekezere kuti anganene zimenezi. Nawonso bambo anagwirizana ndi maganizo a mayiwa.

Ndinaphunzira m’chaputala 6 cha Aefeso kuti Yehova amafuna kuti ndizimvera makolo anga. Poyamba, ndinaganiza kuti ndikawamvera mwina nawonso ayamba kundimvetsa ndipo izi zithandiza kuti tizikhala mwamtendere. Komanso pa nthawiyi n’kuti nditatsala pang’ono kulemba mayeso a ku sekondale, ndipo ndinkafunika kukonzekera. Choncho ndinauza makolo anga kuti ndisiya kuphunzira komanso kusonkhana kwa miyezi itatu. Ndipo ndinamulonjeza Yehova kuti miyezi itatuyo ikangotha, ndiyambiranso kusonkhana.

Koma patapita nthawi ndinaona kuti sindinasankhe bwino. Nditangosiya kuphunzira ndiponso kusonkhana, ubwenzi wanga ndi Yehova unayamba kusokonekera. Komanso m’malo moyamba kundimvetsa, makolo anga anayamba kuchita zinthu zoti ndisiyiretu kutumikira Yehova.

YEHOVA ANANDITHANDIZA PAMENE MAKOLO ANGA ANKANDITSUTSA

Ku Nyumba ya Ufumu ndinakumana ndi anthu ambiri amenenso ankatsutsidwa ndi achibale awo. Anthuwa anandilimbikitsa n’kundiuza kuti Yehova andipatsa mphamvu. (Mat. 10:34-37) Anandiuza kuti ndikapitiriza kutumikira Yehova, mwina ndingathandize anthu a m’banja lathu kuti nawonso ayambe kumutumikira. Choncho ndinkapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima ndipo izi zinandithandiza kuti ndizimudalira kwambiri.

Makolo anga ankachita zinthu zosiyanasiyana pofuna kundifooketsa. Mayi ankayesetsa kukambirana nane komanso kundichonderera kuti ndisiye kutumikira Yehova. Nthawi zambiri akamalankhula, ndinkangokhala chete chifukwa ndikayankha tinkapsetsana mitima. Panopa ndikuona kuti ndinkalephera kumvetsa maganizo awo ndipo izi zinkachititsa kuti tizikangana kwambiri. Mayi ndi bambo anayambanso kundipatsa ntchito zambiri zapakhomo n’cholinga choti ndisamapeze nthawi yokasonkhana. Komanso nthawi zina ndikachoka, ankanditsekera panja kapena kundimana chakudya.

Mayi anapemphanso anthu ena kuti awathandize. Mwachitsanzo, anapempha aphunzitsi anga kuti akambirane nane koma aphunzitsiwo anakana kulowerera nkhani zathu. Mayi anapitanso nane kwa bwana wa kuntchito kwawo n’cholinga choti akandiuze kuti zipembedzo zonse n’zosathandiza. Ankaimbiranso foni achibale osiyanasiyana ndipo ankawapempha akulira kuti awathandize. Izi zinkandikhumudwitsa kwambiri. Koma akulu anandiuza kuti ndisamadandaule nazo kwambiri chifukwa mosadziwa, mayi akuthandiza anthu ambiri kudziwa za Yehova.

Vuto linanso linali loti, makolo anga ankafuna kuti ndipite kuyunivesite n’cholinga choti ndidzapeze ntchito yabwino. Sitikanatha kukambirana nkhaniyi popanda kukangana, choncho ndinawalembera makalata angapo owafotokozera zolinga zanga. Bambo ataona kuti sindikufuna kupita kuyunivesite anakwiya n’kunena kuti: “Ngati ukuona kuti ungapeze ntchito, uipeze pofika mawa apo ayi uchoke pakhomo pano.” Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Tsiku lotsatira ndili mu utumiki, alongo awiri anandiuza kuti andilemba ntchito yophunzitsa ana awo. Izi sizinasangalatse bambo ndipo anasiya kundilankhula komanso ankandipewa. Mayi ankakonda kunena kuti, ‘Bola utakhala chigawenga kusiyana n’kukhala wa Mboni.’

Yehova anandithandiza kudziwa zoyenera kuchita komanso kuti ndiyambe kuona zinthu moyenera

Nthawi zina ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma Yehova akusangalaladi ndi zimene ndikuchitazi?’ Ndinkapemphera kwambiri ndiponso kuphunzira za chikondi cha Yehova m’Baibulo. Izi zinachititsa kuti ndisamadandaule kwambiri ndi zimene makolo anga ankachita komanso kuti ndizindikire kuti ankachita zimenezi chifukwa chondikonda. Yehova anandithandiza kudziwa zoyenera kuchita komanso kuti ndiyambe kuona zinthu moyenera. Ndinkalowa mu utumiki pafupipafupi ndipo ndinayamba kukonda kwambiri kulalikira. Kenako ndinaganiza zoyamba upainiya.

NDINAYAMBA UPAINIYA

Alongo ena atadziwa kuti ndikufuna kuyamba upainiya, anandiuza kuti ndidikire kaye mpaka makolo anga atasiya kunditsutsa kwambiri. Ndinapempha Yehova kuti andipatse nzeru, ndinafufuza za nkhaniyi komanso ndinafunsa abale ndi alongo ena. Ndinaganiziranso zifukwa zimene ndinkafunira kuchita upainiya. Ndinaona kuti cholinga changa ndi kusangalatsa Yehova. Ndinaonanso kuti ngakhale nditadikira, panalibe umboni woti makolo anga adzasintha.

Choncho kutatsala chaka chimodzi kuti ndimalize sekondale, ndinayamba upainiya. Patapita nthawi, ndinkafuna kusamukira kudera lomwe kukufunika ofalitsa ambiri. Koma makolo anga sankafuna kuti ndichoke pakhomo. Choncho ndinadikira mpaka nditakwanitsa zaka 20. Kenako, pofuna kuti mayi asakhumudwe kwambiri, ndinapempha abale ku ofesi ya nthambi kuti anditumize kuchigawo cha kum’mwera kwa Japan kumene kunali achibale athu.

Ananditumizadi kumeneko ndipo ndinayamba kuphunzira ndi anthu ambiri. Ndinasangalala kwambiri kuona ena mwa anthuwa akubatizidwa. Kenako ndinayamba kuphunzira Chingelezi n’cholinga choti ndichite zambiri potumikira Yehova. Mu mpingo wathu munali abale awiri omwe anali apainiya apadera ndipo wina dzina lake anali Atsushi. Anali akhama ndipo ankakonda kuthandiza anthu. Izi zinapangitsa kuti ndikhale ndi cholinga chochita upainiya wapadera. Pa nthawiyi, mayi anadwala kwambiri kawiri konse ndipo ndinkapita kukawasamalira. Sanayembekezere kuti ndingachite zimenezi ndipo anasintha moti sankanditsutsanso kwambiri ngati poyamba.

YEHOVA WANDIDALITSA KWAMBIRI

Patapita zaka 7, ndinalandira kalata yochokera kwa Atsushi. Iye anandifunsa ngati ndingavomere kukhala naye pa chibwenzi. Kunena zoona ndinali ndisanaganizirepo zimenezi ndipo sindinkadziwa kuti ankandifuna. Komabe patatha mwezi, ndinamuyankha n’kumuuza kuti tingopitiriza kulemberana makalata kuti tidziwane bwino. Titalemberana makalata kwa kanthawi, tinaona kuti tinali ndi zolinga zofanana. Tonse tinali okonzeka kuchita utumiki wa nthawi zonse, kulikonse kumene angatitumize. Patapita nthawi tinakwatirana. Ndinasangalala kwambiri kuti mayi, bambo komanso achibale ena anabwera ku ukwati wathu.

Nepal

Tinkachita upainiya wokhazikika koma pasanapite nthawi, Atsushi anapemphedwa kuti akhale woyang’anira dera wogwirizira. Ndiyeno tinayamba upainiya wapadera ndipo kenako tinauzidwa kuti tikagwire ntchito yoyang’anira dera. Apanso tinaona kuti Yehova watidalitsa. Titachezera mipingo yonse m’deralo kamodzi, tinalandira foni yochokera kunthambi. Anatifunsa ngati tingavomere kukagwira ntchito yoyang’anira dera ku Nepal.

Ndaphunzira zambiri zokhudza Yehova chifukwa chotumikira m’mayiko osiyanasiyana

Ndinada nkhawa kuti mwina makolo anga sangasangalale akamva kuti atitumiza kutali chonchi. Koma nditawaimbira foni n’kuwadziwitsa, bambo anayankha kuti: “Kumene mukupitako n’kwabwino kwambiri.” Mnzawo wina anali atangowapatsa buku lofotokoza za ku Nepal ndipo ankafuna atapitako kukaona malo.

Tinkasangalala kwambiri kutumikira ndi abale athu a ku Nepal. Kenako Yehova anatidalitsanso pamene tinauzidwa kuti tizichezera mipingo ina ya ku Bangladesh. Ngakhale kuti dzikoli lili kufupi ndi ku Nepal, anthu ake ndi osiyana. Zikhalidwe ndiponso miyambo yawo ndi zosiyananso kwambiri. Choncho tikakhala mu utumiki, tinkakumana ndi anthu osiyanasiyana. Titatumikira zaka 5, tinauzidwa kuti tibwerere ku Japan ndipo n’kumene tikugwira ntchito yoyang’anira dera panopa.

Ndaphunzira zambiri zokhudza Yehova chifukwa chotumikira ku Japan, ku Nepal ndiponso ku Bangladesh. N’zoona kuti mayikowa ndi osiyana kwambiri ndipo munthu aliyense ndi wosiyananso ndi mnzake. Koma ndaona kuti Yehova amaganizira munthu aliyense payekha, amamuthandiza komanso amamudalitsa.

Ndaonanso kuti Yehova wandidalitsa pondithandiza kuti ndimudziwe, pondipatsa mwamuna wabwino komanso pondipatsa zochita. Wakhala akunditsogoleranso kuti ndizisankha bwino zinthu pa moyo wanga. Panopa ndili pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu ndiponso ndimagwirizana ndi achibale anga. Yehova wandithandizanso kuti ndiyambe kugwirizananso ndi mayi. Ndikusangalala kwambiri kuti tsopano ndili pa mtendere ndi Mulungu komanso mayi anga.

Timasangalala kwambiri kugwira ntchito yoyang’anira dera