Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi likasa la chipangano linapita kuti?

Likasa la chipangano linali chizindikiro chosonyeza kuti Mulungu anali ndi Aisiraeli. (Eksodo 25:22) Likasali linali bokosi lopatulika, ndipo linapangidwa ndi matabwa kenako n’kulikuta ndi golide ndipo Mose anaikamo miyala iwiri yomwe panalembedwa Chilamulo. Panthawi imene Aisiraeli anali m’chipululu, likasali linkasungidwa ku Malo Opatulikitsa a chihema chokomanako. (Eksodo 26:33) Patapita nthawi, likasali analiika ku Malo Opatulikitsa m’kachisi wa Solomo.​—1 Mafumu 6:19.

Likasali linatchulidwa komaliza pa lemba la 2 Mbiri 35:3, pomwe Mfumu Yosiya analibwezeretsa m’kachisi m’chaka cha 642 B.C.E. N’kutheka kuti Mfumu Manase, yemwe anali wampatuko ndipo ankalamulira Ayuda Yosiya asanakhale mfumu, ndi amene anachotsa likasali m’kachisimo, n’kuikamo fano. Kapena likasali linachotsedwa m’kachisimo kuti lisawonongeke pomwe mfumu Yosiya ankakonzanso kachisiyo. (2 Mbiri 33:1, 2, 7; 34:1, 8-11) Koma kenako kumene kunapita likasali sikukudziwika chifukwa silinatchulidwe pa m’ndandanda wa zinthu zimene Ababulo anatenga atawononga mzinda wa Yerusalemu, m’chaka cha 607 B.C.E.​—2 Mafumu 25:13-17.

Baibulo silinena kuti likasali anakaliikanso ku Malo Opatulikitsa a kachisi amene Zerubabele anamanga ndipo zikuoneka kuti sipanapangidwenso likasa lina lolowa m’malo.​—Ezara 1:7-11.

Kodi m’Baibulo, ndani amene anali ndi dzina loti Yakobe?

Panali anthu anayi omwe ankatchedwa ndi dzinali ndipo n’zosavuta kuti munthu asokonezeke. * Yakobe wina anali bambo ake a mtumwi Yudasi (osati Yudasi Isikarioti), ndipo Baibulo silinena chilichonse chokhudza Yakobe ameneyu.​—Luka 6:16; Machitidwe 1:13.

Ndiyeno pali Yakobe, mwana wa Zebedayo. Yakobe ameneyu anali m’bale wake wa Yohane ndipo onsewa anali atumwi a Yesu. (Mateyo 10:2) Zikuoneka kuti mayi ake anali Salome yemwe anali mchemwali wa mayi ake a Yesu. (Yerekezerani Mateyo 27:55, 56 ndi Maliko 15:40, 41 ndiponso Yohane 19:25.) Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Yakobe ameneyu anali msuweni wake wa Yesu. Iye komanso mchimwene wake anali asodzi ndipo ankagwira ntchito limodzi ndi Petulo ndiponso Andireya.​—Maliko 1:16-19; Luka 5:7-10.

Komanso panali Yakobe wina, mwana wa Alifeyo, yemwe analinso mtumwi wa Yesu. (Maliko 3:16-18) Pa lemba la Maliko 15:40, iye amatchedwa kuti, “Yakobe Wamng’ono.” N’kutheka kuti iye ankatchedwa “Wamng’ono” chifukwa choti anali wamfupi kapenanso wamg’ono pomuyerekezera ndi Yakobe, mwana wa Zebedayo.

Panalinso Yakobe womaliza, yemwe anali mwana wa Yosefe ndi Mariya, mchimwene wake wa Yuda ndiponso Yesu. (Maliko 6:3; Agalatiya 1:19) Panthawi ya utumiki wa Yesu, Yakobe ameneyu sanakhale wophunzira wake. (Mateyo 12:46-50; Yohane 7:5) Komabe, pa Pentekosite mu 33 C.E., Yakobe pamodzi ndi mayi ake komanso azibale ake, anapemphera limodzi ndi atumwi m’chipinda cha m’mwamba ku Yerusalemu. (Machitidwe 1:13, 14) Kenako, Yakobe anadzakhala munthu wodalirika kwambiri mu mpingo wa ku Yerusalemu komanso analemba buku la m’Baibulo lomwe lili ndi dzina lake.​—Machitidwe 12:17; Yakobe 1:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 M’Chichewa, dzina lakuti Yakobe ndi lofanana ndi lakuti Yakobo. Mawu akuti “Abulahamu, Isake ndi Yakobo” amapezeka nthawi zambiri m’Baibulo. Ndipo lemba la Mateyo 1:16, limatchula za Yakobo, yemwe “anabala Yosefe, mwamuna wake wa Mariya.”