Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Woweruza Wachilungamo

Woweruza Wachilungamo

Yandikirani Mulungu

Woweruza Wachilungamo

Numeri 20:2-13

ANTHU omwe ali ndi udindo woweruza milandu, nthawi zina amaweruza mokondera kapena amapereka chilango chokhwima kwambiri chosagwirizana ndi mlandu umene munthu wapalamula. Koma Yehova Mulungu ndi wosiyana kwambiri ndi oweruza amenewa chifukwa iye “amakonda chilungamo.” (Salmo 37:28, NW) Komabe, salekerera anthu ochita zoipa ngakhale kuti iye ndi woleza mtima. Nthawi zonse amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Taonani zimene iye anachita Aisiraeli atayamba kukangana ndiponso kuukira Mose, monga mmene buku la Numeri chaputala 20 limasonyezera.

Atatsala pang’ono kutuluka m’chipululu, Aisiraeli anayamba kusowa madzi. * Anthuwa anayamba kukangana ndi Mose ndiponso Aroni n’kumati: “Mwalowa nawo bwanji msonkhano wa Yehova m’chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?” (Vesi 4) Iwo anadandaula kuti chipululucho chinali “malo oipa,” ndipo munalibe “mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza.” Komatu zipatso zimenezi ndi zimene azondi a achiisiraeli anabweretsa kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa, zaka zingapo m’mbuyomo. Anadandaulanso kuti m’chipululumo munalibe “madzi akumwa.” (Vesi 5; Numeri 13:23) Pamenepa kwenikweni iwo ankaimba mlandu Mose ndi Aroni chifukwa chowalowetsa m’chipululumo, mmene munalibe zipatso zangati zimene zinali m’dziko limene makolo awo, omwenso ankadandaula, anakana kulowamo.

Komabe Yehova sananyalanyaze anthuwo ngakhale kuti ankang’ung’udza. M’malo mwake, iye anauza Mose kuti achite zinthu zitatu izi: Atenge ndodo yake, asonkhanitse anthu ndiponso ‘anene ndi thanthwe pamaso pawo, kuti liwapatse madzi.’ (Vesi 8) Mose anamvera malangizo awiri oyambirirawo koma analephera kumvera lachitatulo. M’malo molankhula ndi thanthwelo mwa chikhulupiriro, iye analankhula ndi anthuwo mopsa mtima kuti: “Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m’thanthwe umu?” (Vesi 10; Salmo 106:32, 33) Kenako Mose anamenya thanthwelo kawiri “ndipo madzi anatulukamo ochuluka.”​—Vesi 11.

Pamenepa, Mose ndi Aroni anachita tchimo lalikulu kwambiri. Mulungu anawauza kuti “munapikisana ndi mawu anga.” (Numeri 20:24) Potsutsana ndi malangizo a Mulungu, Mose ndi Aroni ndi amene anasonyeza kuti akupikisana ndi Mulungu. Choncho, Mulungu anapereka chiweruzo mosapita m’mbali kuti Mose ndi Aroni sakalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Kodi tinganene kuti pamenepa Mulungu sanaweruze bwino? Ayi, anaweruza bwino. Tikutero pazifukwa zotsatirazi.

Choyamba, Mulungu sanalangize Mose kuti alankhule ndi anthu kapena kuti auze anthuwo kuti akupikisana ndi Yehova. Chachiwiri, Mose ndi Aroni analephera kupereka ulemerero kwa Mulungu. N’chifukwa chake Mulungu anawauza kuti: “Simunasonyeze . . . kundilemekeza.” (Vesi 12, NW) Ponena kuti “tikutulutsireni madzi,” Mose ankatanthauza kuti iye ndi Aroni, ndi amene angapatse anthuwo madzi, osati Mulungu. Chachitatu, chilango chimene Mulungu anawapatsa chinali chogwirizana ndi zilango zina zimene iye anaperekapo m’mbuyomo. Zimenezi zisanachitike, Mulungu sanalole kuti anthu amene sanamvere malamulo ake alowe m’dziko la Kanani, choncho iye anachitanso chimodzimodzi ndi Mose ndi Aroni. (Numeri 14:22, 23) Chachinayi, Mose ndi Aroni anali atsogoleri a mtundu wa Isiraeli. Choncho, anthu onse amene ali ndi udindo, akalakwitsa chinachake, Mulungu amawaimba mlandu waukulu.​—Luka 12:48.

Yehova amaonetsetsa kuti nthawi zonse chilungamo chachitika. Chifukwa choti iye amakonda chilungamo, sangaweruze mlandu mokondera. Motero, tiyenera kukhulupirira ndiponso kulemekeza Woweruza wathu ameneyu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Atayenda ulendo wochokera ku Iguputo, Aisiraeli anali okonzeka kulowa m’dziko la Kanani, limene Mulungu analonjeza Abulahamu. Koma azondi 10 atabweretsa lipoti loipa, anthuwo anayamba kung’ung’udza pom’dandaula Mose. Choncho, Yehova ananena kuti Aisiraeli akhale m’chipululumo kwa zaka 40 n’cholinga choti anthu onse ong’ung’udzawo afere m’chipululumo.