Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mdyerekezi Ndi Munthu Weniweni?

Kodi Mdyerekezi Ndi Munthu Weniweni?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mdyerekezi Ndi Munthu Weniweni?

Inde, Satana Mdyerekezi ndi munthu weniweni chifukwa ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Koma anthu amene amatsutsa Baibulo amakana zimenezi. Iwo amati Satana ndi maganizo oipa chabe amene amakhala mumtima mwa munthu.

Kodi tiyenera kudabwa chifukwa cha maganizo osiyanasiyana amene anthu ali nawo pankhani yakuti Satana ndi ndani? Ayi. Mwachitsanzo, chigawenga chingasokoneze umboni wa zoipa zimene chachita n’cholinga chakuti chisagwidwe komanso kuti chipitirize kuchita zakezo. N’chimodzimodzinso Satana. Iye ndi chigawenga choopsa chimene chikuchita zinthu mobisa polimbikitsa makhalidwe oipa. Yesu ananena momveka bwino kuti Satana ndi amene akuchititsa kuti zinthu ziipe padziko pano. Iye ananena kuti Satana ndi “wolamulira wa dzikoli.”​—Yohane 12:31.

Kodi Mdyerekezi anachokera kuti? Poyamba iye anali mngelo wangwiro kumwamba. Koma kenako anagalukira Mulungu n’kukhala Mdyerekezi pofuna kuti anthu azimulambira m’malo molambira Mulungu. Baibulo limanena zimene Satana ndi Yesu anakambirana, ndipo zimenezi zinasonyeza kuti Mdyerekezi anali ndi zolinga zadyera. Satana anayesetsa kunyengerera Yesu kuti ‘agwade pansi ndi kumulambira.’​—Mateyo 4:8, 9.

Komanso, buku la Yobu limasonyeza kuti pokambirana ndi Mulungu, Satana anasonyeza zolinga zake zoipa. Iye amachita zonse zimene angathe kuti anthu asiye kulambira Mulungu.​—Yobu 1:13-19; 2:7, 8.

Ganizirani izi: Ngati Satana anakambirana ndi Yehova Mulungu ndiponso Yesu Khristu, kodi n’zoona kuti Satana ndi maganizo oipa chabe amene amakhala mu mtima mwa munthu? Ndithudi, palibe choipa chilichonse mwa Mulungu kapena mwa Mwana wake. Choncho, n’zoonekeratu kuti Satana ndi munthu weniweni, mngelo woipa amene salemekeza Yehova ndiponso Yesu.

Komanso, makhalidwe oipa a anthu, ndi umboni wakuti Mdyerekezi ndi munthu weniweni. Mwachitsanzo, mayiko ambiri amasunga chakudya mpaka kumaola pamene anthu awo akufa ndi njala. Ndipo mayiko ena amasunga zida zoopsa zankhondo zomwe angawonongere anthu ambiri. Ndiponso mayiko amawononga zinthu zachilengedwe zomwe zili padzikoli. Komatu anthu ambiri sadziwa yemwe akulimbikitsa makhalidwe oipa ndiponso owononga moyo amenewa. N’chifukwa chiyani?

Baibulo limanena kuti Satana “wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira.” (2 Akorinto 4:4) Pofuna kukopa komanso kupusitsa anthu, Satana amagwiritsa ntchito gulu lake losaoneka ndi maso. Iye ndi “wolamulira ziwanda.” (Mateyo 12:24) Mtsogoleri wa gulu la zigawenga akhoza kumatsogolera gulu lakelo popanda kudzionetsera kwa anthu onse a m’gululo. Satana nayenso amagwiritsa ntchito gulu lake la angelo oipa kutsogolera anthu ambiri amene sadziwa n’komwe kuti akulamulidwa ndi iye.

Tili ndi mwayi chifukwa Baibulo limaulula za Mdyerekezi ndi gulu lake. Choncho, tingathe kudziteteza kwa Mdyerekezi. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Gonjerani Mulungu; koma tsutsani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani.”​—Yakobe 4:7.