Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anawononga Akanani?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anawononga Akanani?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anawononga Akanani?

“Muwawononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga YEHOVA MULUNGU wanu anakulamulirani.”​—DEUTERONOMO 20:17.

“Khalani mwamtendere ndi anthu onse.”​—AROMA 12:18.

KODI mukawerenga mavesi amenewa mumaganiza kuti ndi otsutsana? Anthu ambiri samvetsa chifukwa chake Mulungu analamula kuti Akanani awonongedwe, akawerenga zimene Baibulo limanena kuti anthu azikhala mwamtendere. * (Yesaya 2:4; 2 Akorinto 13:11) Choncho, iwo amaona kuti malemba amenewa amatsutsana.

Inuyo mukanakhala ndi mwayi wolankhula ndi Mulungu pankhaniyi, kodi mukanam’funsa chiyani? Taonani mafunso asanu amene azunguza mitu anthu ambiri ndiponso mayankho ake ochokera m’Baibulo.

1. N’chifukwa chiyani Akanani anathamangitsidwa m’dziko limene ankakhala? N’chifukwa choti iwo ankakhala m’dziko lomwe silinali lawo. Tikutero chifukwa zaka pafupifupi 400 zimenezi zisanachitike, Mulungu analonjeza Abulahamu, yemwe anali munthu wokhulupirika, kuti adzapereka dziko la Kanani kwa mbadwa zake. (Genesis 15:18) Mulungu anakwaniritsa lonjezoli pamene anathandiza mtundu wa Aisiraeli, womwe unali mbadwa za Abulahamu, kuti ukhale m’dziko la Kanani. Mwina anthu ena anganene kuti Akanani anali eniake a dzikolo chifukwa Aisiraeli anachita kuwapeza. Koma Mulungu, yemwe ndi mwini chilengedwe chonse, ndi amene ali ndi ufulu wonse wopatsa anthu malo amene iyeyo wafuna kuti azikhala.​—Machitidwe 17:26; 1 Akorinto 10:26.

2. N’chifukwa chiyani Mulungu sanalole kuti Akanani azikhala limodzi ndi Aisiraeli? Mulungu anachenjeza Aisiraeli ponena za Akanani kuti: “Asakhale m’dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa ine; pakuti ukatumikira milungu yawo, kudzakukhalira msampha ndithu.” (Eksodo 23:33) Patapita nthawi, mneneri Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa.” (Deuteronomo 9:5) Kodi anthu a ku Kanani ankachita zoipa zotani?

Iwo ankakonda kuchita zachiwerewere, kulambira milungu yonyenga ndiponso kupereka ana awo nsembe. Katswiri wina wa zochitika za m’nthawi ya Baibulo, dzina lake Henry H. Halley, ananena kuti akatswiri ofukula zinthu zakale ku Kanani “anapeza mitsuko yambiri imene munali mafupa a ana omwe anaperekedwa nsembe kwa Baala [yemwe anali mulungu wotchuka ku Kanani].” Katswiriyu anapitiriza kuti: “Dera lonse la Kanani linali ngati manda a ana ongobadwa kumene. . . . Polambira milungu yawo, Akanani ankachita zachiwerewere ndiponso ankapha ana awo oyamba kubadwa n’kuwapereka nsembe kwa milungu imeneyi. Zikuoneka kuti, zochita za Akanani zinali zofanana kwambiri ndi za anthu a ku Sodomu ndi Gomora. . . . Akatswiri amene anafukula zinthu zakale kumizinda ya ku Kanani amadabwa kuti Mulungu sanawononge mwamsanga anthu amenewo.”

3. Popeza panalinso anthu ena oipa, n’chifukwa chiyani Mulungu anasankha kuwononga Akanani okha? Powononga anthu, Mulungu nthawi zonse amawononga oipa okha basi. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Nowa pamene “dziko lapansi . . . linadzala ndi chiwawa,” Mulungu anabweretsa chigumula chimene chinawononga anthu onse oipa, kupatulapo banja la Nowa lokha. (Genesis 6:11; 2 Petulo 2:5) Mulungu anawononganso mizinda ya Sodomu ndi Gomora pamene machimo a anthu a m’mizindayo anachuluka kwambiri. (Genesis 18:20; 2 Petulo 2:6) Komanso, Mulungu ananena kuti adzawononga mzinda wa Nineve, womwe unali likulu la dziko la Asuri, chifukwa unali “mudzi wa mwazi.” Komabe, Mulungu sanawononge mzindawu chifukwa anthu ake analapa. (Nahumu 3:1; Yona 1:1, 2; 3:2, 5-10) Koma Mulungu anawononga Akanani pofuna kuteteza Isiraeli, mtundu umene munadzabadwira Mesiya.​—Salmo 132:11, 12.

4. Kodi zimene Mulungu anachita powononga Akanani, zikugwirizana ndi mfundo yakuti iye ndi wachikondi? Kungoiona nkhaniyi, munthu angaganize kuti zimene Mulungu anachita powononga Akanani sizikugwirizana ndi khalidwe lake la chikondi. (1 Yohane 4:8) Komabe, tikaunika nkhaniyi bwinobwino, timaona kuti Mulungu anachita zimenezi chifukwa cha chikondi.

Iye anali atadziwa kale kuti zochita za Akanani zidzawalowetsa m’mavuto. Komabe, m’malo mowawononga nthawi yomweyo, iye analeza mtima mpaka panadutsa zaka 400 kufikira nthawi imene anaona kuti machimo awo ‘akwanira.’​—Genesis 15:16.

Yehova anawononga Akanani ataona kuti machimo awo achulukitsa moti sangasinthenso. Ngakhale zinali choncho, sikuti iye anapha Akanani onse mwachisawawa. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa choti panali anthu ena omwe ankafunitsitsa kulapa, monga Rahabi ndi Agibeoni, omwe iye anawachitira chifundo.​—Yoswa 9:3-11, 16-27; Aheberi 11:31.

5. N’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe ndi wachikondi, amawononga anthu ena? Funso limeneli n’lomveka chifukwa kuwononga moyo wa munthu si nkhani yosangalatsa. Komabe, Mulungu anawononga anthu oipa chifukwa choti ndi wachikondi. Mwachitsanzo, munthu akavulala kwambiri mwendo kapena mkono, nthawi zambiri madokotala samachitira mwina koma kuudula. Koma palibe dokotala yemwe amasangalala kudula mwendo kapena mkono wa munthu. Ngakhale zili choncho, madokotala amachitabe zimenezi, ngakhale kuti n’zosangalatsa, pofuna kuti munthuyo asafe.

Mofanana ndi zimenezi, Yehova sanasangalale kuwononga Akanani. Iye ananena kuti: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa.” (Ezekieli 33:11) Powononga Akanani, Yehova ankateteza mtundu wa Aisiraeli kuti udzatulutse Mesiya yemwe adzathandize anthu onse a chikhulupiriro kuti adzapulumuke. (Yohane 3:16) Chifukwa cha zimenezi, Mulungu sanalole kuti Akanani awononge khalidwe la Aisiraeli. Motero, Mulungu analamula Aisiraeli kuti awononge Akanani kapena awathamangitse m’dziko lomwe ankakhala. Pochita zimenezi, Mulungu anasonyeza kuti ndi wachikondi kwambiri. Ngakhale kuti zinali zosasangalatsa, iye anawononga Akanani n’cholinga chothandiza atumiki ake okhulupirika.

Zimene Tikuphunzirapo

Kodi nkhani yonena za kuwonongedwa kwa Akanani, ili ndi phindu lililonse kwa ife masiku ano? Inde, chifukwa lemba la Aroma 15:4 limati: “Zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitika ku Kanani? Nanga zikutipatsa chiyembekezo chotani?

Pali zambiri zimene tingaphunzire pankhani imeneyi. Mwachitsanzo, Mulungu mwachifundo sanawononge Rahabi ndiponso Agibeoni chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro. Zimenezi zikutikumbutsa mfundo yoti aliyense amene akufunitsitsa kutumikira Mulungu angathe kutero, ngakhale kuti anachita machimo ambiri m’mbuyomu.​—Machitidwe 17:30.

Nkhani ya kuwonongedwa kwa Akanani ikutithandiza kukhala ndi chiyembekezo cha zimene Mulungu adzachite posachedwapa. Nkhaniyi ikutithandizanso kudziwa kuti Mulungu sadzalola kuti anthu oipa awononge anthu abwino. M’malomwake, Baibulo limatitsimikizira kuti posachedwapa, Mulungu awononga anthu onse oipa ndipo apulumutsa anthu omwe amamukonda n’kuwalowetsa m’dziko la tsopano, momwe mudzakhala chilungamo. (2 Petulo 2:9; Chivumbulutso 21:3, 4) Panthawi imeneyo, mawu otonthoza awa adzakwaniritsidwa: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko: Pakudulidwa oipa udzapenya.”​—Salmo 37:34.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Munkhani ino, mawu akuti “Akanani” akutanthauza mitundu yonse imene Mulungu analamula kuti Aisiraeli aithamangitse m’dziko lolonjezedwa.

[Bokosi patsamba 14]

Kodi Mulungu Amasangalala ndi Nkhondo Zimene Anthu Akumenya Masiku Ano?

Kodi lamulo limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli kuti awononge Akanani, likusonyeza kuti iye amasangalala ndi nkhondo zimene anthu akumenya masiku ano? Ayi. Tikutero chifukwa cha mfundo zitatu izi:

Masiku ano, palibe mtundu uliwonse wa athu umene Mulungu akuukonda mwapadera. Aisiraeli atakana kuti Yesu sanali Mesiya, Mulungu anasiya kugwiritsira ntchito mtundu wawo kumuimira pazinthu zosiyanasiyana, monga pankhondo. (Mateyo 21:42, 43) Motero, Yehova anayamba kuona Aisiraeli mofanana ndi mmene amaonera mitundu ina yonse. (Levitiko 18:24-28) Kuyambira nthawi imeneyo, palibe mtundu wina uliwonse padzikoli umene unganene kuti Mulungu amawuthandiza pomenya nkhondo.

Masiku ano, Yehova salamula atumiki ake kuti azikhala m’dziko kapena dera linalake lapadera. M’malomwake, atumiki ake amapezeka ‘m’dziko lililonse, fuko lililonse ndi mtundu’ uliwonse padzikoli.​—Chivumbulutso 7:9; Machitidwe 10:34, 35.

Yesu ananena momveka bwino kuti otsatira ake sayenera kumenya nawo nkhondo. Polangiza otsatira ake za kuwonongedwa kwa Yerusalemu komwe kunali pafupi, iye sanawauze kuti adzakhale momwemo n’kumenya nkhondo. M’malomwake anawauza kuti adzathawe, ndipo iwo anathawadi. (Mateyo 24:15, 16) M’malo momenya nkhondo, Akhristu oona amadalira Ufumu wa Mulungu womwe posachedwapa udzachotseratu anthu onse oipa.​—Danieli 2:44; Yohane 18:36.

[Chithunzi patsamba 15]

Nkhani ya Rahabi ikusonyeza kuti aliyense amene akufunitsitsa kusangalatsa Mulungu, angathe kutero