Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

MNYAMATA wina wachamba amene anali m’gulu la achinyamata ovutitsa anasiya kusuta. Katswiri wina woimba nyimbo zaphokoso anameta tsitsi lake, lomwe linali lalitali kwambiri, n’kuyamba kudana ndi nyimbo zimene ankakondazo. Munthu wina amene sankafuna kumvera boma kapena kulowa m’chipembedzo chilichonse anakhala mtumiki wa Mulungu. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthu amenewa asinthe chonchi? Taonani zimene anthuwa ananena.

“Ndinakwanitsa kusiyiratu kusuta chamba.”​—PETER KAUSANGA

ZAKA: 32

DZIKO: NAMIBIA

POYAMBA: ANKASUTA CHAMBA KOMANSO ANALI M’GULU LA ACHINYAMATA OVUTITSA

KALE LANGA: Ndinakulira ku Kehemu. Limeneli ndi limodzi mwa madera anayi akuluakulu am’tawuni ya Rundu. Anthu akumeneku ankapeza ndalama pogulitsa mapira, nkhuni ndiponso makala.

Mayi anga anamwalira ndili ndi zaka ziwiri zokha ndipo ndinakula ndi agogo anga aakazi. Banja lathu linali losauka. Poyamba ndinali mwana womvera koma kenako ndinatengera khalidwe loipa la anzanga. Ndili kusukulu ndinalowa m’gulu lina la achinyamata ovutitsa. Motero ndiyamba ndewu, kuvutitsa, kuba, kuzembetsa miyala ya dayamondi ndiponso kuledzera ndi kusuta chamba. Ndinagwidwapo kawiri konse n’kumangidwa chifukwa cha kuba m’nyumba za anthu ndiponso kubera anthu mwachinyengo.

Ndinasiya sukulu ndili fomu 2 ndipo kenako ndinasamuka m’dera lomwe ndinakulira lija kuti ndisiyane ndi anzanga amene ankandilimbikitsa kuchita zoipa. Komabe zinkandivuta kusiya kusuta chamba. Nthawi zina ndinkalolera kuyenda ulendo wautali kuti ndikangopeza ndudu imodzi ya chamba.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Kumayambiriro kwa chaka cha 1999 ndinakumana ndi a Mboni za Yehova amene ankapereka magazini awo kwa anthu mumsewu. Ulemu umene anandisonyeza unandikhudza mtima kwambiri. Nditawerenga uthenga umene unali m’magaziniwo ndinadziwa kuti ndapeza chipembedzo choona. Ndinayamba kuphunzira Baibulo mwakhama ndipo posakhalitsa ndinazindikira kuti ndinayenera kusintha zinthu zina pa moyo wanga n’cholinga choti ndizisangalatsa Yehova Mulungu.

Ndinadziikira tsiku loti ndisiye kusuta ndiponso kutaya chilichonse chokhudzana ndi kusuta. Ndinawauzanso anzanga kuti asamandigawire fodya ndiponso kuti asamasute pafupi ndi ine. Komabe zinthu sizinayende monga mmene ndimaganizira moti kawiri konse ndinakanika kupirira chibaba cha fodya ndiponso chamba chitandigwira. Zimenezi sizinandifooketse ayi. Ndinakumbukira mfundo ya pa Miyambo 24:16, yakuti: “Wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso.” Patapita nthawi, ndinakwanitsa kusiyiratu kusuta chamba.

Nditayamba kudziwa zambiri zokhudza Yehova, ndinafunitsitsa kuti akhale bwenzi langa lapamtima. Lemba limodzi limene linandikhudza mtima kwambiri ndi la Salmo 27:10: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” Nditapitiriza kuphunzira Baibulo mozama, ndinamvetsa tanthauzo la mawu amenewa. Ndinayamba kuona kuti Yehova ndi Atate anga enieni amene amandikonda komanso kundiganizira.

Ndinkapitanso kumisonkhano ya Mboni za Yehova mlungu uliwonse. Kumisonkhano imeneyi ndinkatha kuona kuti anthu amenewa amagwirizana komanso kukondana kwambiri. Aka kanali koyamba m’moyo wanga kukumana ndi anthu achikondi chonchi.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinayamba kudzisamalira, kuvala bwino, kusintha makhalidwe ndiponso kalankhulidwe. Zonsezi zinatheka ndi thandizo la Yehova komanso a Mboni anzanga. Ndikamakumbukira kale langa ndimaona kuti moyo wanga wasintha kwambiri, ngati mmene mbozi imasinthira n’kukhala gulugufe wokongola kwambiri. Achibale anga amasangalala kwambiri poona kuti ndasintha chonchi ndipo tsopano amandidalira. Panopo ndili pabanja ndipo ndimachita zonse zimene ndingathe kuti ndizimusonyeza chikondi mkazi wanga ndiponso kusamalira bwino ana anga.

“Moyo wanga uli ndi cholinga chenicheni.”​—MARCOS PAULO DE SOUSA

ZAKA: 29

DZIKO: BRAZIL

POYAMBA: ANALI M’BANDI INA YOIMBA NYIMBO ZAPHOKOSO

KALE LANGA: Ndinkakhala ndi makolo anga m’tawuni ya Jaguariuna mumzinda wa São Paulo. Makolo anga anali akatolika olimbikira kwambiri ndipo ineyo ndili mwana ndinali m’gulu la anyamata otumikira ku guwa. Chifukwa cha zimenezi anzanga a kusukulu anandipatsa dzina lakuti Bambo Mfumu. Koma ndili ndi zaka 15 ndinayamba kukonda mtundu wa nyimbo zinazake zaphokoso kwambiri. Ndinayamba kucheza ndi anthu oimba nyimbo za chamba chimenechi ndiponso kuweta tsitsi. Mu 1996, bambo anandigulira ng’oma zimene mabandi amagwiritsira ntchito.

Mu 1998 ndinalowa m’gulu lina loimba nyimbo zaphokoso. Nyimbo zimene tinkaimba zinali zausatana ndiponso zotukwana komanso zinkalimbikitsa zachiwawa. Nyimbozi zinasokoneza maganizo ndiponso khalidwe langa. Ndinasintha kwambiri ndipo ndinkangolusa zilizonse.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Ndinakumana ndi Mboni za Yehova koyamba mu 1999. Iwo anapempha kuti aziphunzira nane Baibulo ndipo ndinavomera, ngakhale kuti ndinalibe chidwi kwenikweni. Zimene ndinaphunzirazo zinandithandiza kusintha mmene ndinkaonera moyo.

Anthu ankangonditcha kuti “watsitsi lalitali,” “katswiri woimba,” kapena “katswiri wa ng’oma.” Koma ndinazindikira kuti kukhala woimba nyimbo kunandipatsa mtima wodzikonda ndi wampikisano, ndipo ndinayamba kuona kuti sindikutchuka ndi zinthu zabwino. Ndinazindikira kuti oimba anzanga amene ndinkawalambira analibe cholinga chenicheni pamoyo wawo. Patapita nthawi ndinazindikiranso kuti ngati ndikufuna kusangalatsa Yehova Mulungu, ndiyenera kusiya kumvera nyimbo zaphokosozo ndiponso moyo umene nyimbo zimenezi zimalimbikitsa, wachimasomaso ndiponso wolambira anthu.

Ndinkazikonda kwambiri nyimbozo komanso tsitsi langa lalitali. Sindinkaona kuti ndingathe kukhala popanda zinthu ziwiri zimenezi. Chinanso, ndinali munthu wamtima wapachala ndipo ndinkadziwa kuti ndiyenera kusintha n’kumaugwira mtima. Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuti ndiyambe kukonda kwambiri Yehova. Ndinayamba kum’konda kwambiri Yehova pophunzira za makhalidwe ake monga chikondi, kuleza mtima ndiponso chifundo. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kusintha ndipo anandithandizadi. Ndaona kuti mawu a pa Aheberi 4:12 ndi oonadi. Lemba limeneli limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”

Nditayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova, ndinaona kuti anthu amenewa ndi osiyana kwambiri ndi anthu azipembedzo zina. Kwa nthawi yoyamba m’moyo wanga ndinaona anthu akusonyezana chikondi chenicheni. Chikondi chimenechi chinkaonekera kwambiri makamaka pamisonkhano ikuluikulu imene a Mboniwo ankachita. Ndinagoma kwambiri ndi mmene anthu amene anadzipereka kugwira ntchito zosiyanasiyana pamsonkhanopo ankagwirira ntchito zawo kuti aliyense asangalale ndi msonkhanowo.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndi thandizo la Yehova, tsopano ndimatha kuugwira mtima. Ndimaona kuti ndinasiya mtima wodzikonda ndiponso kunyada.

Kunena zoona, nditangoyamba kumene kuphunzira Baibulo ndinkalakalakabe zinthu zina zimene ndinkachita kale koma panopo sindizilakalakanso. Tsopano moyo wanga uli ndi cholinga chenicheni. Ndimasangalala kuti ndikuphunzira kuchita chidwi ndi anthu ena ndiponso mmene zinthu zikuyendera pamoyo wawo.

“Ndimasangalala kuchita zinthu moganizira ena.”​—GEOFFREY NOBLE

ZAKA: 59

DZIKO: UNITED STATES OF AMERICA

POYAMBA: SANKAFUNA KUMVERA BOMA KAPENA KULOWA CHIPEMBEDZO CHILICHONSE

KALE LANGA: Ndinakulira m’tawuni ya Ipswich, yomwe ili m’mphepete mwa nyanja ku Massachusetts. Anthu ambiri m’tawuni imeneyi anali osauka. Nditakula ndinasamukira m’dera lina lakumidzi ku Vermont. Tikatengera moyo wa anthu a ku North America, tingati ineyo ndi chibwenzi changa tinkakhala moyo wovutika kwambiri. Nyumba yathu inalibe magetsi, choncho tinkakatola nkhuni kunkhalango kuti tiziphikira ndi kuwotha. Tinali ndi chimbudzi chokumba kunja kwa nyumba yathu ndipo nthawi zambiri sitinkagwiritsa ntchito madzi apampopi. Sitinkafuna kumakhala ngati mmene anthu ena onse m’dziko lathu ankakhalira, motero sitinkasamalanso za maonekedwe athu. Ndikukumbukira kuti nthawi ina ndinkanyadira chifukwa choti ndinakwanitsa kukhala miyezi 6 chipeso chisanadutse m’mutu mwanga.

Panthawiyo, asilikali a dziko la United States anapita kukamenya nkhondo ku Vietnam. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kudana ndi mfundo za boma. Ndinaona kuti m’boma ndiponso m’zipembedzo munkachitika zachinyengo kwambiri. Ndinkaganiza kuti boma kapena chipembedzo sizingathandize munthu, choncho ndi bwino kuti aliyense azingoyendera mfundo zake. Motero ndinkaona kuti panalibe vuto kuba chilichonse chimene ndinkafuna.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Ineyo ndi chibwenzi changa tinayamba kuwerenga Baibulo ngakhale kuti sitinkalimvetsa. Panthawiyi ndinkagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo koma ndinkayesetsa kuti ndisiye. Chibwenzi changa chinkafuna kuti tikwatirane ndiponso kuti tikhale ndi ana. Kenaka munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu n’kuyamba kuphunzira nafe Baibulo.

Patangopita nthawi yochepa ndinakwanitsa kusiya makhalidwe anga oipa. Komabe zinkandivuta kuti ndiyambe kutsatira malamulo a boma. Ndinali nditazolowera kukayikira chilichonse. Ndinakula moyo wotayirira kwambiri motero zinali zovuta kwambiri kuti ndiyambe kutsatira malamulo a munthu wina.

Ndinkakhulupirira kuti kuli Mlengi, komabe ndinali ndi maganizo olakwika okhudza Mlengiyo. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo ndinayamba kumvetsa makhalidwe a Yehova Mulungu. Ndinaphunzira kuti Iye anafotokoza momveka bwino zonse zimene amafuna kuti anthufe tizichita ndipo palibe zinthu zina zimene amafuna kuti tizichita zomwe sanatifotokozere bwinobwino. Ndinaphunziranso kuti iye ali ndi cholinga chokonza dzikoli kuti lidzakhale paradaiso. (2 Petulo 3:13) Nditaphunzira mfundo za m’Baibulo zimenezi ndinayamba kufunitsitsa kusintha moyo wanga kuti ndikhale woyenerera kutumikira Mulungu.

Chimene chinandisangalatsa kwambiri ndi a Mboni za Yehova n’chakuti ankakana kulowerera nkhondo. Palibe chipembedzo chinanso cha padziko lonse chimene ndinamvako kuti chinkatsatiranso mfundo ya m’Baibulo imeneyi, yosalowerera m’nkhondo.

Ndinadziwa kuti ndiyenera kuyamba kudzisamalira kuti ndikhale woyenera kutumikira Yehova. Poyamba, zinkandivuta kuvala motsatira mfundo za m’Baibulo, ngati mmene amachitira a Mboni. Ineyo ndi anzanga ena onse tinalibe shati, thalauza kapena nsapato zoti n’kuvalira ku anthu. Ndinalibenso tayi ngakhale imodzi. Komabe ndinameta tsitsi langa n’kuyamba kudzisamalira. Mpaka pano ndimakumbukira zimene zinachitika tsiku langa loyamba kupita kukalalikira khomo ndi khomo. Pakhomo lina panali galasi limene ndinatha kuona mmene ndinkaonekera nditameta. Ngakhale kuti ndinkaoneka bwino ndinadzifunsa kuti, ‘Ndachitiranji zimenezi?’ Komabe patapita nthawi, ndinayamba kusangalala ndi mmene ndinkaonekera.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinakwatirana ndi chibwenzi changa chija ndipo panopo banja lathu ndi losangalala. Ana athu atatu tawaphunzitsa kuti azikonda Yehova ndiponso kuti azim’tumikira. Komanso ndakhala ndi mwayi wothandiza ena kuphunzira mfundo za m’Baibulo zimene zinandithandiza kusintha moyo wanga.

Poyamba ndinkadzitama kuti sindisamala zimene anthu ena akuganiza. Koma panopa ndimasangalala kuchita zinthu moganizira ena ndipo nawonso amandiganizira.

[Mawu Otsindika patsamba 26]

“Ndinkalolera kuyenda ulendo wautali kuti ndikangopeza ndudu imodzi ya chamba”

[Mawu Otsindika patsamba 28]

“Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kusintha mmene ndinkaonera moyo”

[Chithunzi patsamba 29]

“Zinkandivuta kuvala motsatira mfundo za m’Baibulo, ngati mmene amachitira a Mboni”