Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Nyumba ya Ufumu N’chiyani?

Kodi Nyumba ya Ufumu N’chiyani?

Nyumba ya Ufumu ndi nyumba yolambiriramo imene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito pochita zinthu zosiyanasiyana zokhudza kupembedza Mulungu. Padziko lonse pali Nyumba za Ufumu masauzande ambirimbiri. Mlungu uliwonse, mipingo ya Mboni za Yehova yopitirira 105,000 imakumana m’nyumba zimenezi.

Nyumba ya ufumu iliyonse imakhala ndi holo imene amachitiramo misonkhano yophunzitsa Baibulo komanso amakambiramo nkhani za m’Baibulo. Monga mmene amakhalira maholo ambiri, kutsogolo kwa maholo ambiri a m’Nyumba za Ufumu kumakhala malo okwera amene okamba nkhani pamisonkhanoyi amaimako. Nthawi zambiri maholo amenewa amakhala ndi malo oti mungakhale anthu kuyambira pa 100 mpaka 300. Nyumba za Ufumu zina zimakhala ndi kalasi imodzi kapena angapo, ofesi ndi laibulale imene imakhala ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo komanso ndi zinthu zina zofufuzira nkhani zosiyanasiyana zimene aliyense wa pampingopo amatha kugwiritsira ntchito akafuna kufufuza zinazake.

Komabe, mu Nyumba ya Ufumu iliyonse simukhala zinthu zimene zimapezeka m’matchalitchi ambiri monga gome kapena guwa, kapenanso mitanda, zosema ndi zifanizo zilizonse. N’chifukwa chiyani zimenezi sizimapezekamo? Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti kugwiritsira ntchito zinthu zoterezi n’kotsutsana ndi lamulo la m’Baibulo lakuti “thawani kupembedza mafano.” (1 Akorinto 10:14; Yohane 4:24) Matchalitchi ndiponso akachisi ambiri amamangidwa moti azigometsa anthu ndipo amakongoletsedwa mwadzaoneni. Koma mosiyana ndi zimenezi, Nyumba za Ufumu sazimanga moti zizigometsa anthu, choncho sizikhala ndi zinthu zimene sadzazigwiritsa ntchito iliyonse. Zimene amaganizira kwambiri pomanga Nyumba ya Ufumu si kaonekedwe ka nyumbayo ayi, koma ntchito yake, yomwe ndi kuphunziriramo Baibulo.

N’chifukwa chiyani malowa amatchedwa Nyumba ya Ufumu? Anthu akasonkhana pa Nyumba ya Ufumu, cholinga chawo chachikulu chimakhala kuphunzira Baibulo ndiponso kumvetsera uthenga wofunika kwambiri wa m’Baibulo wokhudza “ufumu wa Mulungu.” Ndipotu nkhani ya Ufumu wa Mulungu ndi imene inali yaikulu kwambiri pa utumiki wa Yesu. (Luka 4:43) Choncho, dzina lakuti Nyumba ya Ufumu, limene linayamba kugwiritsidwa ntchito m’ma 1930, limasonyeza bwino cholinga cha nyumba zimenezi, chomwe ndi kupititsa patsogolo kulambira koona ndiponso kugwiritsidwa ntchito ndi mipingo ya Mboni za Yehova monga likulu la ntchito yolalikira za ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ (Mateyo 24:14) Motero Nyumbazi sizigwiritsidwa ntchito pochita maphwando kapena ntchito iliyonse yopezera ndalama. Anthu amapereka ndalama mwakufuna kwawo kuti zigwiritsidwe ntchito pomanga, polipirira zinthu zosiyanasiyana zimene zimafunikira nyumba ikatha, ndiponso pokonza zimene zawonongeka. Koma mu Nyumba ya Ufumu sayendetsamo mbale ya chopereka. M’malomwake, amaika bokosi pamalo enaake kuti aliyense amene akufuna kupereka ndalama aikemo.

Padziko lonse, Nyumba za Ufumu zimagwiritsidwa ntchito yofanana, koma zimakhala zosiyana kukula kwake komanso kamangidwe kake. M’dera lililonse, amamanga nyumbazi mogwirizana ndi zida zomangira, nyengo komanso kapezedwe ka Mboni za Yehova za kumeneko. Nyumba zina amazimanga ndi njerwa, matabwa, kapenanso miyala. Zina zimangokhala ndi denga lokha, kapena amazimangira makoma awiri okha a msungwi ndipo denga lake limakhala la udzu.

Aliyense ndi wolandiridwa pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu ina iliyonse. (Aheberi 10:25) Ndipo mlungu uliwonse kumachitika msonkhano umene unakonzedwa n’cholinga choti ukhale msonkhano umene mfundo zimakhudza munthu aliyense. Pamsonkhanowu amakamba nkhani ya m’Baibulo yomwe imakhala ndi mfundo zothandiza kwa anthu mumpingowo komanso kwa alendo onse amene angabwere. Tikukupemphani kuti tsiku lina mudzapite ku Nyumba ya Ufumu imene muli nayo pafupi ndi kukadzionera nokha zonsezi.