Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu—Kodi Anachita Zotani pa Moyo Wake?

Yesu—Kodi Anachita Zotani pa Moyo Wake?

“Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.”​—YOHANE 4:34.

TIKAGANIZIRA mmene zinthu zinalili pa nthawi imene Yesu analankhula mawu amenewa, tingadziwe zimene iye ankaziona kuti ndi zofunika kwambiri pa moyo wake. Pa nthawiyi, Yesu ndi ophunzira ake anali atayenda ulendo wautali m’mawa wonse m’njira ya m’mapiri yodutsa ku Samariya. (Yohane 4:6, mawu am’munsi) Poganiza kuti Yesu anali ndi njala ophunzira ake anamupatsa chakudya. (Yohane 4:31-33) Zimene Yesu ananena zinasonyeza bwino cholinga chachikulu pa moyo wake. Kwa iye kuchita chifuniro cha Mulungu kunali chinthu chofunika kwambiri kuposa kudya. Zonena komanso zochita za Yesu zinasonyeza kuti cholinga chake chinali kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi zina zimene Yesu anachita ndi ziti?

Analalikira ndiponso kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu

Baibulo limafotokoza ntchito imene Yesu ankagwira. Limati: “Anayendayenda m’Galileya yense kuphunzitsa . . . [ndi] kulalikira uthenga wabwino wa ufumu.” (Mateyu 4:23) Yesu sankangolalikira kapena kulengeza kwa anthu za Ufumu wa Mulungu. Koma iye ankawaphunzitsanso, zimene zikutanthauza kuti ankawalangiza, kuwafotokozera mfundo ndi kuwafika pa mtima ndi mfundo zomveka. Mfundo yaikulu ya uthenga wa Yesu inali Ufumu.

Nthawi yonse ya utumiki wake, Yesu ankaphunzitsa anthu tanthauzo la Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzachite. Taonani mfundo zotsatirazi zokhudza Ufumu wa Mulungu, ndiponso Malemba amene aikidwa omwe akutiuza zimene Yesu ananena pa mfundoyo.

  • Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba ndipo Yesu ndi amene Yehova wamusankha kuti akhale Mfumu ya Ufumu umenewu.​—MATEYU 4:17; YOHANE 18:36.

  • Ufumu wa Mulungu udzayeretsa dzina la Mulungu ndipo udzachititsa kuti chifuniro chake chichitike padziko lapansi monga kumwamba.​—MATEYU 6:9, 10.

  • Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso.​—LUKA 23:42, 43.

  • Ufumu wa Mulungu ubwera posachedwapa ndipo udzakwaniritsa cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi. *​—MATEYU 24:3, 7-12.

Anachita Zozizwitsa

Yesu ankadziwika kuti anali “Mphunzitsi.” (Yohane 13:13) Komabe pa zaka zitatu ndi hafu zimene anachita utumiki wake, iye anachitanso zozizwitsa zambiri. Iye anachita zozizwitsa zimenezi pa zifukwa ziwiri izi. Choyamba anachita zimenezi pofuna kutsimikizira kuti anatumizidwadi ndi Mulungu. (Mateyu 11:2-6) Chachiwiri, zinasonyeza zimene iye adzachite akadzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, ndipo pa nthawiyo adzachita zambiri kuposa pamenepo. Taonani zina mwa zozizwitsa zimene iye anachita.

Tangoganizirani mmene moyo padziko lapansi udzakhalire wosangalatsa, Mfumu yamphamvu imeneyi ikamadzalamulira.

Anathandiza anthu kudziwa Yehova Mulungu

Pa nkhani ya kuphunzitsa ena za Yehova, palibe amene angaphunzitse bwino kuposa Mwana wa Mulungu, yemwe anadzadziwika ndi dzina lakuti Yesu Khristu. Popeza Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” iye anakhala ndi Yehova kumwamba kwa nthawi yaitali kuposa angelo onse. (Akolose 1:15) Zimenezi zikusonyeza kuti iye anali ndi nthawi yambiri yotha kutengera kwambiri maganizo a Atate wake. Iye anaphunziranso kwambiri za chifuniro, mfundo ndiponso njira za Atate wake.

Mpake kuti Yesu ananena kuti: “Palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.” (Luka 10:22) Pamene Yesu anali padziko lapansi, mofunitsitsa anathandiza anthu kudziwa kuti Atate wake ndi wotani. Zinthu zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zapadera kwambiri chifukwa iye pophunzitsa, ankakumbukira zinthu zimene anaphunzira kumwamba, kumalo aulemerero pamaso pa Mulungu Wamwambamwamba.​—Yohane 8:28.

Zimene Yesu anachita pothandiza anthu kudziwa kuti Atate wake ndi wotani tingaziyerekeze ndi zimene thiransifoma ya magetsi imachita. Thiransifoma imatenga magetsi amphamvu kwambiri n’kuwasintha kuti akhale ndi mphamvu yochepa, kuti zipangizo zimene zikufunika magetsi ochepa mphamvu zithe kuwagwiritsa ntchito mosavuta. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaphunzitsa anthu zinthu zimene anaziphunzira kumwamba zokhudza Atate wake. Koma anawaphunzitsa m’njira yoti anthuwo athe kumvetsa mosavuta komanso athe kuzitsatira.

Taonani njira ziwiri zimene Yesu anathandizira anthu kudziwa kuti Atate wake ndi wotani.

  • Zimene Yesu anaphunzitsa, zinathandiza anthu kudziwa zoona zokhudza dzina, chifuniro komanso mmene Yehova amachitira zinthu.​—YOHANE 3:16; 17:6, 26.

  • Zimene anachita, zinathandiza anthu kudziwa makhalidwe osiyanasiyana a Yehova. Yesu anasonyeza bwino makhalidwe a Atate wake moti tingati ananena kuti: ‘Ngati mukufuna kudziwa kuti Atate wanga ndi wotani, ingoonani ineyo.’​—YOHANE 5:19; 14:9.

Timagoma ndi zimene Yesu anachita pa moyo wake. Koma tingapindule kwambiri ngati titazindikira chifukwa chake anafa komanso ngati titachita zinthu mogwirizana ndi zimene taphunzira.

^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri za Ufumu wa Mulungu komanso chifukwa chake tikunena kuti ubwera posachedwa, werengani mutu 8 wakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani” ndi mutu 9 woti “Kodi Tili ‘M’masiku Otsiriza’?, m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.