Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Kenako Mtendere

Mavuto Kenako Mtendere

Mavuto Kenako Mtendere

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.”​—2 TIMOTEYO 3:1.

N’KUTHEKA kuti munamvapo kapena kuona zinthu zomvetsa chisoni ngati izi:

● Matenda oopsa amene anapha anthu ambirimbiri.

● Anthu miyandamiyanda amene anafa chifukwa cha njala.

● Chivomezi choopsa chomwe chinapha anthu ambiri n’kusiya enanso ochuluka alibe nyumba.

Mu nkhani zotsatirazi muwerenga mfundo zimene zingakuthandizeni kuganizira mofatsa za mavuto osiyanasiyana ngati amenewa. Muonanso kuti Baibulo linalosera kuti zinthu zimenezi zidzachitika “m’masiku otsiriza.” *

Nkhanizi cholinga chake sikukutsimikizirani kuti tikukhala m’dziko lamavuto. Zili choncho chifukwa inuyo muyenera kuti mukudziwa kale za mavuto amenewa. Koma cholinga chake ndi kukuthandizani kuti mukhale ndi chiyembekezo. Nkhanizi zikuthandizani kuona kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi 6 amene tikambirane ndi umboni wakuti “masiku otsiriza” atsala pang’ono kutha. Nkhani zimenezi zifotokozanso zimene anthu ambiri amanena potsutsa maulosiwa ndiponso zitithandiza kudziwa chifukwa chake tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti posachedwapa zinthu zikhala bwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika, werengani mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Padzikoli Pakhale Mavuto?” patsamba 16 ndi 17 m’magazini ino.