Ulosi Wachinayi: Kupanda Chikondi
Ulosi Wachinayi: Kupanda Chikondi
“Anthu adzakhala . . . osakonda mabanja awo.”—2 TIMOTEYO 3:1-3, God’s Word.
● Munthu wina dzina lake Chris amagwira ntchito ku bungwe lina ku North Wales, lothandiza anthu amene akuchitiridwa nkhanza m’banja. Iye ananena kuti: “Ndikukumbukira kuti tsiku lina ku ntchito kwathu kunabwera mayi wina amene anali atamenyedwa kwambiri moti sindinathe kumuzindikira kuti ndi amene anabweranso tsiku lina. Zoterezi zikachitika, azimayi ena amavutika maganizo kwambiri moti ukamalankhula nawo, saatha n’komwe kukuyang’ana.”
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? M’dziko lina la ku Africa kuno, pa azimayi atatu aliwonse, mayi mmodzi anagwiriridwapo ali mwana. M’dziko lomwelo atapanga kafukufuku anapeza kuti pafupifupi hafu ya amuna onse m’dzikolo amaona kuti palibe vuto kumenya akazi awo. Komabe si akazi okha amene amachitiridwa nkhanza m’banja. Mwachitsanzo ku Canada pa amuna 10 alionse, atatu amamenyedwa kapena kuchitiridwa nkhanza zina ndi akazi awo.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Kuchitirana nkhanza m’banja sikunayambe lero. Koma kungoti masiku ano anthu akuchita chidwi kwambiri ndi nkhani zimenezi kuposa kale.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? N’zoona kuti masiku ano pali nkhani ndiponso mabungwe ambiri amene akudziwitsa anthu za nkhanza zimene zikuchitika m’banja. Komabe kodi kudziwa zimenezi kwapangitsa kuti nkhanzazi zichepe? Ayi. Anthu ambiri akuchita zinthu zosonyeza kuti sakonda mabanja awo.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi sizoona kuti lemba la 2 Timoteyo 3:1-3 likukwaniritsidwa? Kodi sizoona kuti masiku ano anthu ambiri amachita zinthu zosonyeza kuti sakonda akazi kapena amuna awo ngakhale kuti mwachibadwa munthu amayenera kukonda anthu a m’banja lake?
Ulosi wina wachisanu umene ukukwaniritsidwa masiku ano ndi wokhudza dziko lapansili. Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.
[Mawu Otsindika patsamba 7]
“Kuchitirana nkhanza m’banja ndi limodzi mwa mavuto aakulu amene anthu ambiri amakonda kubisa. Pa avereji, mayi amachitiridwa nkhanza ndi mwamuna wake kokwana ka 35 asanakanene ku polisi.”—WOFALITSA NKHANI ZA M’BUNGWE LINA LA KU WALES LOONA ZA NKHANZA ZA M’BANJA.