Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yolimbikitsa Kwa Anthu Osweka Mtima

Nkhani Yolimbikitsa Kwa Anthu Osweka Mtima

Yandikirani Mulungu

Nkhani Yolimbikitsa Kwa Anthu Osweka Mtima

‘YEHOVA sangandikonde.’ Mawu amenewa ananena ndi mayi wina wachikhristu yemwe kwa nthawi yaitali anadwala matenda ovutika maganizo. Iye ankaona kuti Yehova sangamuthandize. Koma kodi n’zoonadi kuti Yehova sathandiza atumiki ake omwe akuvutika maganizo? Yankho lolimbikitsa la funso limeneli likupezeka m’mawu ouziridwa amene wamasalimo Davide analemba pa Salimo 34:18.

Davide ankadziwa zimene zimachitika mtumiki wokhulupirika wa Yehova akakhala kuti akuvutika maganizo kwambiri chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo. Ali mnyamata, iye anakhalapo moyo wothawathawa chifukwa Mfumu Sauli inkafunitsitsa kumupha chifukwa chomuchitira nsanje. Davide anathawira mumzinda wa Gati womwe unali kudera la Afilisiti. Iye anachita zimenezi poganiza kuti Sauli sangaganize n’komwe zokamuyang’ana kumeneko chifukwa Afilisiti anali adani a Aisiraeli. Koma Davide atadziwa kuti Afilisiti amuzindikira ndipo akufuna kumupha, ananamizira kuti ndi wamisala ndipo anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi. Davide anazindikira kuti Mulungu ndi amene anamupulumutsa ndipo zimenezi n’zimene zinachititsa kuti alembe Salimo 34.

Kodi Davide ankakhulupirira kuti Mulungu sangathandize anthu amene akukumana ndi mavuto omwenso akuona kuti Iye sawawerengera? Davide analemba kuti: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Vesi 18) Tiyeni tione chifukwa chake tingati mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri.

“Yehova ali pafupi.” Buku lina limati mawu amenewa “akufotokoza momveka bwino kuti Ambuye amakhala tcheru ndipo amaona zonse zimene zikuchitika komanso nthawi zonse amakhala wokonzeka kuti athandize ndiponso kupulumutsa anthu ake.” N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amaona zimene zikuchitikira anthu ake. Iye amaona mavuto amene atumiki ake akukumana nawo ‘m’nthawi yovuta’ ino komanso amadziwa mmene akumvera mumtima mwawo.​—2 Timoteyo 3:1; Machitidwe 17:27.

“Anthu a mtima wosweka.” Anthu a m’zikhalidwe zina amati munthu amakhala ndi “mtima wosweka” ngati munthuyo akukonda munthu wina koma winayo sakumukonda iyeyo. Koma katswiri wina wamaphunziro ananena kuti mawu amenewa akunena za “zinthu zonse zimene zimachititsa kuti munthu akhale wachisoni ndiponso wosasangalala.” Ngakhale atumiki okhulupirika a Mulungu nthawi zina angakumane ndi mavuto amene angawachititse kukhala osweka mtima.

“Odzimvera chisoni mumtima mwawo.” Anthu amene akuvutika maganizo ndi zinazake angamadzione kuti ndi achabechabe ndipo angayambe kuona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Buku lina la omasulira Baibulo limanena kuti mawu amenewa angamasulidwenso kuti “anthu amene alibiretu chiyembekezo.”

Koma kodi Yehova amatani akaona anthu “a mtima wosweka” komanso “odzimvera chisoni mumtima mwawo?” Kodi iye sawathandiza poganiza kuti anthu oterewa ndi osafunika kuti iye aziwakonda ndiponso kuwaganizira? Ayi ndithu, iye satero. Mofanana ndi kholo lachikondi limene limathandiza komanso kutonthoza mwana wake amene akuvutika maganizo, Yehova ali pafupi ndi atumiki ake amene amamuchonderera kuti awathandize. Iye ndi wofunitsitsa kuwatonthoza komanso kukhazikitsa pansi mtima wawo wosweka ndi wachisoni. Yehova angawapatse nzeru ndi mphamvu kuti athe kupirira mayesero onse amene akukumana nawo.​—2 Akorinto 4:7; Yakobo 1:5.

Tikukupemphani kuti muphunzire zimene mungachite kuti muyandikire Yehova. Mulungu wachifundo ameneyu akutilonjeza kuti: “Ine ndimakhala . . . ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa, kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.”​—Yesaya 57:15.

Mavesi amene mungawerenge mu June:

Salimo nambala 26 mpaka 59