3 Mulungu Amakonda Kulanga Amene Amulakwira—Kodi Zimenezi ndi Zoona?
3 Mulungu Amakonda Kulanga Amene Amulakwira—Kodi Zimenezi ndi Zoona?
Mwina munamvapo izi: “Mulungu saiwala tchimo lililonse limene munthu wachita ndipo amalanga munthu wochimwayo kwamuyaya kumoto.”
“Mulungu amagwiritsa ntchito masoka achilengedwe pofuna kulanga anthu ochimwa.”
Zimene Baibulo limaphunzitsa: Lemba la 2 Petulo 3:9 limanena kuti Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” Mulungu sayang’ana kwambiri zinthu zimene timalakwitsa, m’malomwake amayang’ana kwambiri zimene timachita bwino. Maso a Mulungu “akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”—2 Mbiri 16:9.
Baibulo siliphunzitsa zoti kuli malo kumene anthu amakapsa ndipo Mulungu amadana ndi kuzunza munthu kwamuyaya. Chilango chachikulu chimene iye amapereka kwa anthu oipa ndi imfa. (Yeremiya 7:31; Aroma 6:7) Ndipo Mulungu sachititsa masoka achilengedwe omwe amapha anthu mwachisawawa, mosatengera za khalidwe lawo. Masoka amenewa ali m’gulu la zinthu zosayembekezereka zimene zingagwere aliyense.—Mlaliki 9:11.
Kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi kungakuthandizeni bwanji? Kudziwa kuti Mulungu ndi “wokonzeka kukhululuka” ndipo sikuti amangokhalira kuona zolakwa zathu kungatithandize kumuyandikira. (Salimo 86:5) Sitiyenera kutumikira Mulungu chifukwa choopa kuti tikapanda kutero atiimba mlandu kapena atilanga. M’malomwake tiyenera kumukhulupirira kwambiri ndipo tiyenera kuchita zimenezi chifukwa chomukonda. Chikondi chimenechi n’chimene chingatichititse kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingamusangalatse.—Mateyu 22:36-38; 1 Yohane 5:3.
Yehova amafuna kuti aliyense azichita zabwino komabe amadziwa kuti anthu ambiri sangachite zimenezi. Ngati iye atangowasiya anthu amene amachita zoipawo, angafanane ndi wolamulira amene amakhazikitsa malamulo koma osasamala kuti malamulowo akutsatiridwa kapena ayi, n’kumangolekerera kuti zinthu zopanda chilungamo komanso zoipa zizipitirirabe. (Mlaliki 8:11) Kudziwa kuti Mulungu salola kuti zoipa zizichitikabe mpaka kalekale kumatithandiza kukhala ndi chiyembekezo. Mulungu walonjeza kuti adzawononga anthu amene amapitirizabe kuchita zoipa. Iye adzachita zimenezi n’cholinga chakuti “anthu ofatsa” asangalale ndi moyo wosatha padziko lapansi ngati mmene iye ankafunira kuyambira pa chiyambi.—Salimo 37:10, 11, 29. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Mulungu adzachite kuti dzikoli likhale paradaiso, werengani mutu 3 ndi 8 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Kodi Mulungu amafuna kuti tizimulambira chifukwa choopa kuti atilanga?
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
Engravings by Doré