Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Abulahamu Anali Ndani?

Kodi Abulahamu Anali Ndani?

Kodi Abulahamu Anali Ndani?

PALI anthu ochepa akale amene moyo wawo umakhudza kwambiri zipembedzo za padziko lonse lapansi. Koma Abulahamu * amalemekezedwa ndi Ayuda, Asilamu, ndiponso Akhristu. Iwo amamutchula kuti ndi “munthu wofunika kwambiri m’Malemba” komanso ndi “chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya chikhulupiriro.” Baibulo limamutchula kuti ndi “tate wa onse . . . okhala ndi chikhulupiriro.”​—Aroma 4:11.

Kodi n’chifukwa chiyani Abulahamu amapatsidwa ulemu kwambiri chonchi? Chifukwa chimodzi n’chakuti, Abulahamu ndi munthu yekhayo amene Baibulo limamutchula mwachindunji kuti bwenzi la Mulungu.​—Yesaya 41:8; Yakobo 2:23.

Komatu, Abulahamu anali munthu wamba ngati ife tomwe. Iye anakumana ndi mavuto ambiri ofanana ndi amene ifenso timakumana nawo ndipo anawagonjetsa. Kodi mukudziwa zimene zinamuthandiza? Tiyeni tikambirane zimene Baibulo limanena zokhudza munthu ameneyu.

Mmene Anakulira

Abulahamu anabadwa m’chaka cha 2018 B.C.E. ndipo anakulira mumzinda wa Uri. (Genesis 11:27-31) Mzinda umenewu unali waukulu ndiponso wotukuka kwambiri. Anthu ambiri a mumzindawu ankalambira mafano. N’kutheka kuti Tera, yemwe anali bambo a Abulahamu, ankalambiranso mafano osiyanasiyana. (Yoswa 24:2) Koma Abulahamu anasankha kulambira Yehova * yekha m’malo molambira milungu yopanda moyo.

Kodi n’chiyani chinathandiza Abulahamu kuti asankhe kulambira Yehova? Abulahamu anabadwa kutatsala zaka 150 kuti Semu, yemwe anali mwana wa Nowa, amwalire. Ngati Abulahamu ankacheza ndi munthu wachikulire kwambiri ameneyu, ndiye kuti anaphunzira zambiri. N’kutheka kuti Semu anauza Abulahamu mmene zinalili pa nthawi ya Chigumula komanso mmene anapulumukira. Abulahamu ayenera kuti anadziwa kufunika kolambira Yehova Mulungu yemwe anapulumutsa Semu ndi banja lake ku Chigumula chimenechi.

Kaya Abulahamu anamva za Mulungu woona kuchokera kwa Semu kapena kwa munthu wina, iye anagwiritsa ntchito zimene anamvazo. Yehova, “amene amayesa mitima,” anaona chinachake chabwino mwa munthu ameneyu ndipo anamuthandiza kuti akhale munthu wabwino kwambiri.​—Miyambo 17:3; 2 Mbiri 16:9.

Moyo Wake

Abulahamu anali ndi moyo wosangalala ndipo anakhala kwa nthawi yaitali. Iye ankakumana ndi mavuto pa moyo wake koma zimenezi sizinapangitse kuti moyo wake ukhale wopanda phindu. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene anakumana nazo pa moyo wake.

Abulahamu anauzidwa ndi Mulungu kuti asamuke ku Uri kumene ankakhala ndipo anamuuza kuti amusonyeza koti akakhale. Abulahamu ndi Sara sankadziwa kumene akupita komanso chifukwa chake Mulungu wawauza kuti asamuke. Komabe iwo anatsatira zimene Mulungu anawauzazo. Kenako Abulahamu ndi Sara anayamba kukhala m’mahema m’dziko la Kanani ndipo moyo wawo wonse ankangokhala ngati alendo.​—Machitidwe 7:2, 3; Aheberi 11:8, 9, 13.

Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzatulutsa mtundu waukulu mwa iye koma pa nthawiyo n’kuti Abulahamu ndi Sara alibe mwana aliyense. Yehova ananenanso kuti mabanja onse apadziko lapansi adzapeza madalitso chifukwa cha Abulahamu. (Genesis 11:30; 12:1-3) Patapita nthawi, Yehova anamutsimikizira kuti adzakwaniritsadi lonjezoli. Komanso iye anauza Abulahamu kuti mbewu yake idzakhala yambiri ngati nyenyezi zakumwamba.​—Genesis 15:5, 6.

Abulahamu ali ndi zaka 99 ndipo Sara atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 90, Yehova anawalonjeza kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna. Zimenezi zinaoneka ngati zosatheka koma pasanapite nthawi Abulahamu ndi Sara anazindikira kuti palibe “chosatheka ndi Yehova.” (Genesis 18:14) Patatha chaka chimodzi, Abulahamu anakhala ndi mwana wamwamuna ndipo anam’patsa dzina lakuti Isaki. Pa nthawi imeneyi n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 100. (Genesis 17:21; 21:1-5) Mulungu analonjeza kuti anthu onse adzadalitsidwa kwambiri kudzera mwa Isaki.

Patadutsa zaka zingapo, Yehova anauza Abulahamu kuti achite chinthu chinachake chovuta. Iye anauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wake wokondedwa, Isaki. Pa nthawiyi Isaki anali asanakwatire komanso alibe mwana. * Ngakhale kuti Abulahamu anavutika maganizo poona kuti zimenezi zichititsa kuti mwana wake afe, iye anamvera zimene Mulungu ananenazi ndipo anali wokonzeka kupereka Isaki nsembe. Abulahamu ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu anali ndi mphamvu zoukitsa Isaki, ngati patafunika kutero, kuti akwaniritse malonjezo Ake. (Aheberi 11:19) Abulahamu atangotsala pang’ono kupereka nsembe mwana wake, Isaki, Mulungu anamuletsa kuti asamuphe. Mulungu anayamikira Abulahamu chifukwa chosonyeza kumvera. Kenako Yehova anabwerezanso malonjezo amene anauza Abulahamu poyamba paja.​—Genesis 22:1-18.

Abulahamu anamwalira ali ndi zaka 175. Baibulo limanena kuti iye “anamwalira ali wokalamba” komanso “atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutira.” (Genesis 25:7, 8) Choncho Abulahamu anaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo lina la Mulungu lakuti iye adzamwalira mwamtendere atakhala ndi moyo wabwino komanso wautali.​—Genesis 15:15.

Mbiri Imene Anasiya

Abulahamu ndi munthu wofunika m’mbiri yakale komanso wodziwika kwambiri ndi anthu a m’zipembedzo zambiri. Ndipotu mpaka pano zimene iye anachita ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe. (Aheberi 11:8-10, 17-19) Tiyeni tikambirane makhalidwe anayi abwino amene Abulahamu anali nawo. Tiyamba ndi khalidwe limene iye amadziwika nalo kwambiri, lomwe ndi chikhulupiriro.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Poyamba, Abulahamu ankatchedwa Abulamu ndipo mkazi wake ankatchedwa Sarai. Kenako Mulungu anasintha dzina la Abulamu kukhala Abulahamu, kutanthauza “Tate wa Khamu la Anthu” komanso dzina la Sarai kukhala Sara, kutanthauza “Mfumukazi.” (Genesis 17:5, 15) Koma mu nkhanizi tizingowatchula kuti Abulahamu ndi Sara.

^ ndime 6 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

[Bokosi patsamba 4]

Munthu Wofunika Kwambiri mu Mbiri ya M’Baibulo

Machaputala 10 oyambirira a m’buku la Genesis amafotokoza mbiri ya anthu angapo omwe anali ndi chikhulupiriro. Ena mwa anthu amenewa ndi Abele, Inoki ndi Nowa. Komatu machaputala 15 otsatira amanena za munthu mmodzi yekha, yemwe ndi Abulahamu.

Ndipotu mfundo zina zikuluzikulu za m’Baibulo, pomwe zinkatchulidwa koyamba, nkhani yake inali yokhudza Abulahamu. Mwachitsanzo, tikamawerenga nkhani zokhudza moyo wa Abulahamu timapeza . . .

▪ pamene Baibulo limatchula koyamba zoti Mulungu ndi chishango, kapena kuti Mtetezi, wa atumiki ake.​—Genesis 15:1; onani Deuteronomo 33:29; Salimo 115:9; Miyambo 30:5.

▪ pamene Baibulo limanena koyamba zokhudza kukhulupirira Mulungu.​Genesis 15:6.

▪ pamene Baibulo limatchula koyamba mawu akuti mneneri.​Genesis 20:7.

▪ pamene Baibulo limatchula koyamba za chikondi chimene kholo limakhala nacho pa mwana wake.​—Genesis 22:2.