Kodi Anthu Onse Omwe Amati Ndi Akhristu Ndi Akhristudi?
Kodi Anthu Onse Omwe Amati Ndi Akhristu Ndi Akhristudi?
KODI padziko lapansili pali Akhristu angati? Buku lina linanena kuti m’chaka cha 2010 padzikoli panali Akhristu pafupifupi 2.3 biliyoni. (Atlas of Global Christianity) Koma buku lomweli linasonyeza kuti Akhristu amenewa ali m’zipembedzo zosiyanasiyana zoposa 41,000 ndipo chipembedzo chilichonse chili ndi ziphunzitso komanso malamulo akeake. Chifukwa cha kuchuluka kwa zipembedzo zachikhristu kumeneku, m’pake kuti anthu ena zimawavuta kudziwa chipembedzo choona. Iwo amadzifunsa kuti, ‘Kodi onse amene amati ndi Akhristu, amatsatiradi Khristu?’
Kuti tidziwe yankho la funso limeneli tiyeni tiyerekeze chonchi: Munthu amene akufuna kulowa m’dziko lina amayenera kunena dziko limene akuchokera kwa munthu woona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko. Amayeneranso kusonyeza pasipoti yake ngati umboni wa zimene wanenazo. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu woona ayenera kuchita zambiri, osati kungonena kuti ndi Mkhristu. Iye amayenera kupereka umboni wakuti amakhulupiriradi Khristu. Kodi angapereke umboni wotani?
Mawu akuti “Mkhristu” anayamba kugwiritsidwa ntchito pambuyo pa chaka cha 44 C.E. Luka, yemwe analemba nawo Baibulo, anati: “Ku Antiokeya, n’kumene ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.” (Machitidwe 11:26) Onani kuti anthu amene ankatchedwa Akhristu anali ophunzira a Khristu. Kodi munthu amakhala bwanji wophunzira wa Yesu Khristu? Buku lina linati: “Kukhala wotsatira wa Yesu kapena kuti wophunzira wake kumatanthauza kudzipereka ndi mtima wonse . . . kuti pa moyo wako udzatsatira zimene Yesu anaphunzitsa zivute zitani.” (The New International Dictionary of New Testament Theology) Choncho, Mkhristu woona ndi amene zivute zitani amatsatira ziphunzitso komanso malamulo a Yesu, yemwe anayambitsa Chikhristu.
Popeza pali anthu ambiri amene amati ndi Akhristu, kodi masiku ano n’zotheka kudziwa Akhristu oona? Kodi Yesu ananena kuti otsatira ake enieni tingawadziwe bwanji? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti muone mmene Baibulo limayankhira mafunso amenewa. Mu nkhani zimenezi tikambirana zinthu zisanu zimene Yesu ananena zomwe zingatithandize kudziwa otsatira ake enieni. Tionanso mmene Akhristu oyambirira ankachitira zinthu zimenezi. Tikambirananso kuti, pa anthu ambirimbiri amene amanena kuti ndi Akhristu, ndi anthu ati amene amachitadi zinthu zosonyeza kuti ndi Akhristu oona.