Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinachititsa kuti mwamuna wina, amene anakulira m’banja lachikatolika yemwenso zinkamuyendera bwino pa ntchito yake yazamalamulo, akhale wa Mboni za Yehova? Nanga n’chiyani chinachititsa kuti munthu wina amene anali chigawenga asinthe n’kuyamba kulalikira uthenga wabwino? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthu amenewa ananena.

“Ndinadziwa kusiyanitsa pakati pa choyenera ndi chosayenera.”​—SEBASTIÃO ALVES JUNQUEIRA

CHAKA CHOBADWA: 1946

DZIKO: BRAZIL

POYAMBA: NDINALI MKATOLIKA WODZIPEREKA

KALE LANGA: Banja lathu linkakhala m’mudzi wina womwe uli pa mtunda wa makilomita pafupifupi 6 kuchokera m’tawuni ya Piquete. Makolo anga anali ndi famu yaing’ono komabe ankatha kukolola zinthu zokwanira banja lathu. Ndinkaphunzira pasukulu ina imene inali m’tawuni ya Piquete, choncho ndinagula njinga yakale imene inkandithandiza kuti ndiziyenda mosavuta popita kusukulu. Anthu ambiri am’dera lathu anali osauka komabe tawuniyi inali yaukhondo ndipo kawirikawiri simunkachitika zinthu zaumbanda. Amuna ambiri m’tawuniyi ankagwira ntchito pafakitale ina imene inkapanga zida zankhondo.

Ndinkakonda kuwerenga kwambiri, choncho ndinalowa sukulu yausilikali yomwe inali mumzinda wapafupi ndi kumene ndinkakhala ndipo m’chaka cha 1966, ndinamaliza maphunziro anga. Kenako ndinayamba kuphunzira zamalamulo pasukulu ina ndipo ndinalandira digiri. Nditamaliza maphunzirowa ndinafunsira ntchito ya mkulu wa apolisi. Mu 1976 ndinayamba ntchitoyi nditakhoza mayeso a boma ndipo nthawi zina ntchito yanga inkaphatikizapo kuyang’anira ndende. Kawirikawiri kundendeko kunkabwera a Mboni za Yehova ndipo ankapempha chilolezo choti alalikire kwa akaidi. Nthawi zonse akabwera ankandilalikiranso ineyo. Ndinkakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo ndinachita chidwi kwambiri nditadziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo nditha kukhala naye pa ubwenzi.

N’kupita kwa nthawi ndinayamba kukwezedwa pa udindo. Mu 1981, ndinakhoza mayeso ena a boma ndipo anandikweza kukhala woweruza wa boma. Kenako mu 2005, ndinasankhidwa kukhala woweruza milandu kukhoti la apilo la ku São Paulo.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditangomaliza maphunziro anga azamalamulo, ndinayamba kuwerenga Baibulo ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndisinthe mmene ndinkaonera zinthu. Ndinali Mkatolika wodzipereka ndipo anthu ena a m’banja mwathu anali ansembe ndipo wina anali bishopu. Ine ndinkathandiza wansembe pa nthawi ya mwambo wa Misa. Wansembeyo asanayambe kulalikira, ndinkawerenga mapemphero angapo kuchokera m’buku la mapemphero. Pa nthawiyo anthu ambiri Akatolika sankawerenga Baibulo kunyumba kwawo, choncho mayi anga anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti ndikumawerenga Baibulo. Iwo anandiuza kuti ndisiye chifukwa zindisokoneza. Koma ndinapitirizabe kuwerenga Baibulo chifukwa ndinkaona kuti silinkandisokoneza.

Ndimaona kuti chidwi changa chachibadwa n’chimene chinachititsa kuti ndipitirizebe kuwerenga Baibulo. Ndinkafuna kudziwa zambiri zokhudza ansembe atchalitchi chathu ndiponso udindo wawo. Ndinayambanso kuwerenga mabuku a kagulu ka anthu amene ankalimbikitsa kuti tchalitchi chiyenera kuyesetsa kuthetsa kupondereza anthu kumene olemera, andale komanso anthu ena ankachita. Koma mfundo zimene anthu amenewa ankanena zinali zosamveka.

Pa nthawi imeneyi, dokotala wina wamano, yemwe anali Mbuda, anandipatsa buku lina limene anthu ena anam’patsa. Mutu wa bukuli unali wakuti Did Man Get Here by Evolution or by Creation? * Ndinalandira bukulo poganiza kuti lili ndi mfundo zofanana ndi buku lakuti The Origin of Species, lolembedwa ndi Charles Darwin. Koma ndinaona kuti mfundo za m’buku la Did Man Get Here by Evolution or by Creation? zinali zomveka, zotsatirika komanso zokopa. Ndinaona kuti chiphunzitso chakuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina n’chopanda umboni.

Kuwerenga buku lonena za chilengedwe kunachititsa kuti chidwi changa chiwonjezeke. Ndinafuna kupeza mabuku enanso amene a Mboni za Yehova amafalitsa. Anthu ena anandiuza za makaniko wina amene anali wa Mboni za Yehova. Nditalankhula naye, anandipatsa mabuku ena a Mboni za Yehova. Pa nthawiyo, sindinavomere zoti ndiziphunzira Baibulo ndi a Mboni chifukwa ndinkaona kuti ndingathe kumaphunzira pandekha.

Nditayamba kuwerenga Baibulo ndinaona kuti, popeza ndinali wokwatira, ndibwino kuti ndiziwerenganso ndi banja langa. Mlungu uliwonse tinkaphunzira monga banja ndiponso tinkawerengera limodzi Baibulo. Popeza banja lathu linali lachikatolika, tonse tinkakhulupirira kwambiri ansembe komanso mabishopu. Koma nditawerenga lemba la Yohane 14:6 ndinachita chidwi kwambiri. Lembali limati: “Yesu anamuuza [wophunzira wake Tomasi] kuti: ‘Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.’” Nditafufuza kwambiri za nkhaniyi, ndinaona kuti chipulumutso chimachokera kwa Yehova kudzera mwa Yesu. Chifukwa cha zimene tinkaphunzitsidwa, ifeyo tinkakhulupirira kuti chipulumutso chimachokera kwa ansembe.

Palinso mavesi ena awiri amene anandichititsa kuti ndisinthe mmene ndinkaonera tchalitchi cha Katolika komanso ziphunzitso zake. Loyamba ndi Miyambo 1:7 limene limanena kuti: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa zinthu. Nzeru ndi malangizo zimanyozedwa ndi zitsiru.” Lachiwiri ndi Yakobo 1:5 limene limati: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” Kuyambira kale ndinali ndi ludzu lauzimu ndipo ngakhale kuti ndinkapita kutchalitchi ludzuli silinkatha. Choncho ndinasiya kupita kutchalitchi.

M’chaka cha 1980 mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Ndikakhala kuti ndili pakhomo, ndinkakhalapo akamaphunzira. Kenako ndinavomera kuti wa Mboni za Yehova wina azindiphunzitsanso ineyo. Komabe panatenga zaka zambiri tisanasankhe zobatizidwa kuti tikhale a Mboni za Yehova. Koma kenako m’chaka cha 1994 mkazi wanga anabatizidwa ndipo ineyo ndinabatizidwa mu 1998.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Takwanitsa kulera ana athu anayi mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna. (Aefeso 6:4) Ana athu awiri aamuna amatumikira m’mipingo ya Mboni imene amasonkhana ndipo amayesetsa kuthandiza anthu ena. Nawonso ana athu awiri aakazi amalalikira mwakhama pofuna kuthandiza anthu ena. Mwezi uliwonse mkazi wanga amatha nthawi yambiri akuthandiza anthu kuphunzira Baibulo ndipo ine ndikutumikira monga mkulu mu mpingo umene timasonkhana.

Nditakhala wa Mboni za Yehova, ndinadziwa kusiyanitsa pakati pa choyenera ndi chosayenera. Pa ntchito yanga monga woweruza milandu, ndimayesetsa kutsanzira Yehova. Ndimayesetsa kuganizira mmene zinthu zilili komanso zimene zachititsa munthuyo kupalamula mlandu ndipo ndimasonyeza chifundo pamene pakufunika kutero.

Ndaweruzapo milandu yambiri yokhudza chiwawa, kuphwanya malamulo, kuzunza ana komanso milandu ina ikuluikulu. Komabe zimenezi sizinandichititse kuti ndikhale munthu wopanda chifundo. Ndikamaonera nkhani pa TV, ndimanyansidwa kuona makhalidwe oipa amene ali ponseponse m’dzikoli. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chondithandiza kudziwa zimene zikuchititsa kuti padzikoli zinthu ziziipiraipira komanso chifukwa chondithandiza kudziwa chiyembekezo chabwino chimene anthufe tili nacho.

“Kukhala m’ndende sikunathandize kuti ndisinthe.”​—KEITH WOODS

CHAKA CHOBADWA: 1961

DZIKO: NORTHERN IRELAND

POYAMBA: NDINALI CHIGAWENGA

KALE LANGA: Ndinabadwa m’chaka cha 1961 m’tawuni ya Portadown, m’dziko la Northern Ireland. Ndinakulira m’banja lachipulotesitanti ndipo tinkakhala m’nyumba zoyandikana kwambiri. Anthu ambiri m’derali anali Akatolika ndi Apulotesitanti. Mabanja ambiri anali osauka ndipo ankakonda kupemphana zinthu.

Ndili mwana ndinali wovuta kwambiri. M’chaka cha 1974 ndinalowa m’gulu lina limene linayambitsa chisokonezo m’dzikoli. Pa nthawi imeneyo zinthu zinafika poipa kwambiri m’dera lathu. Mwachitsanzo, tsiku lina usiku, bambo anga omwe anali manijala pafakitale ina yopanga makalapeti, ankaphunzitsa ntchito anyamata awiri achikatolika omwe ankakhala pafupi ndi nyumba yathu. Ndiyeno munthu wina anaponya bomba pawindo la nyumba ya anyamatawa ndipo linapha bambo awo, mayi awo, komanso mchimwene wawo.

Zinthu zinaipiraipirabe ndipo kenako nkhondo inayambika. Nyumba za Apulotesitanti amene ankakhala m’madera a Akatolika zinkawotchedwa ndipo Akatolika amene ankakhala m’madera a Apulotesitanti nawonso ankazunzidwa. Akatolika ambiri anathawa m’dera limene tinkakhala ndipo linasanduka la Apulotesitanti. Pasanapite nthawi ndinamangidwa chifukwa chophulitsa bomba ndipo ndinalamulidwa kukakhala kundende zaka zitatu.

Ndili kundendeko ndinayamba kucheza kwambiri ndi munthu wina amene anali wodziwika kwambiri m’gulu lina lachipulotesitanti. Tinkangokhala ngati pachibale ndipo kenako ndinagwirizira ukwati wake monga mnzake wapamtima. Komabe kukhala kundende sikunatisinthe. Atatitulutsa, tinayambiranso zandale ndipo tinkachita zoposa zimene tinkachita poyamba. Zimenezi zinachititsa kuti mnzangayu amangidwenso ndipo anaphedwa kundende komweko.

Inenso anayamba kundisakasaka ndipo nthawi ina galimoto yanga inaphulitsidwa ndi bomba. Koma zimenezi zinangondiwonjezera mangolomera.

Pa nthawi imeneyi ndinathandiza nawo kukonza pulogalamu ina yokhudza zisokonezo zimene zinkachitika m’dzikolo ndipo inawulutsidwa pa TV ya ku Britain. Zimenezi zinangondiwonjezera mavuto ena. Mwachitsanzo, tsiku lina nditafika kunyumba ndinapeza kuti mkazi wanga wandithawa. Pasanapite nthawi, mwana wanga wamwamuna anatengedwa ndi bungwe linalake loona za ufulu wa ana chifukwa ankaona kuti sindinali woyenerera kulera mwanayo. Ndimakumbukira kuti tsiku limeneli ndinathedwa nzeru kwambiri moti ndinayang’ana pagalasi n’kunena kuti, “Mulungu ngati mulipodi, chonde ndithandizeni.”

Loweruka la mlungu womwewo, ndinakumana ndi mnzanga wina, dzina lake Paul, yemwe anali atakhala wa Mboni za Yehova. Iye anayamba kundifotokozera mfundo za m’Baibulo. Patapita masiku awiri, Paul ananditumizira magazini ya Nsanja ya Olonda. M’magaziniyi munali nkhani ina yomwe inali ndi mawu a Yesu opezeka palemba la Yohane 18:36. Iye anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” Mawu amenewa anandichititsa chidwi kwambiri ndipo tsiku limeneli ndi lomwe zinthu zinayamba kusintha pa moyo wanga.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Paul anayamba kuphunzira nane Baibulo ndipo kenako wa Mboni wina, dzina lake Bill, anapitiriza kuphunzira nane. Ndimadziwa kuti ndinali munthu wovuta kum’phunzitsa chifukwa ndinkafunsa mafunso ambiri. Nthawi zambiri ndinkaitana atsogoleri achipembedzo osiyanasiyana n’cholinga choti azidzatsutsa zimene Bill anganene. Koma ndinazindikira kuti zimene iye ankaphunzitsa zinali zochokera m’Mawu a Mulungu.

Tsiku lina ndinamuuza Bill kuti asabwere kudzandiphunzitsa chifukwa kudera lathu misewu inali itatsekedwa ndipo ndinkaona kuti mwina anthu amene anatseka misewuwo akanalanda galimoto yake n’kuiwotcha. Koma iye atamva zimenezi anasiya galimotoyo n’kutenga njinga ndipo anabwerabe kudzandiphunzitsa. Iye anachita zimenezi chifukwa anadziwa kuti anthuwo sangamulande njingayo. Tsiku linanso ine ndi Bill tikuphunzira kunyumba kwanga, apolisi ndi asilikali anabwera kudzandigwira. Pamene ankalimbana nane kuti andimange, Bill anandiuza kuti ndidalire Yehova. Zinthu ngati zimenezi zinapangitsa kuti ndiyambe kuganizira kwambiri za moyo wanga.

Tsiku loyamba limene ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kukasonkhana nawo, ziyenera kuti anthu ambiri kumeneko anadabwa kwambiri. Ndinali ndi tsitsi lalitali, ndinavala ndolo komanso ndinavala jekete lachikopa la chipani. Komabe ndinadabwa ndi mmene a Mboni anandilandirira. Ndinachitanso chidwi kuona kuti iwo ndi anthu okoma mtima kwambiri.

Ngakhale kuti ndinali nditayamba kuphunzira Baibulo ndinkachezabe ndi anzanga akale. Komabe patapita nthawi zinthu zimene ndinkaphunzira m’Baibulo zinayamba kukhazikika mu mtima mwanga. Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kutumikira Yehova, ndinayenera kusintha anthu ocheza nawo komanso mmene ndinkaonera nkhani zandale. Kuchita zimenezi kunali kovuta. Koma nditaphunzira zambiri za m’Baibulo komanso ndi thandizo la Yehova, ndinasintha. Ndinameta tsitsi lija, kusiya kuvala ndolo ndiponso ndinagula suti. Zimene ndinkaphunzira zinandithandizanso kusintha mmene ndinkaonera anthu.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinali chigawenga ndipo sindinkati ndapalamula liti milandu. Apolisi komanso anthu ena azamalamulo ankandidziwa monga chigawenga. Koma panopa zinthu zinasintha. Mwachitsanzo, pamene ndinkapita koyamba kumsonkhano wa Mboni za Yehova, umene unachitikira m’tawuni ya Navan, apolisi ankandikayikirabe moti anandiperekeza ulendo wonse, kupita n’kubwera. Koma masiku ano ndimapita kumisonkhanoyi popanda kuperekezedwa. Komanso panopa ndimalalikira mwaufulu limodzi ndi Paul, Bill ndiponso a Mboni ena a mumpingo wathu.

Moyo wanga unasinthiratu ndipo ndinayamba kuchitira limodzi zinthu ndi mpingo. Kenako ndinakumana ndi wa Mboni wina, dzina lake Louise, ndipo tinakwatirana. Komanso mwana wanga uja anandibwenzeranso.

Ndikamaganizira zimene ndinkachita kale, ndimamva chisoni chifukwa cha zoipa zimene ndinkachitira anthu ena. Koma panopa ndimakhulupirira kuti Baibulo lili ndi mphamvu yotha kusintha anthu amene anali ndi makhalidwe oipa n’kukhala anthu abwino. Baibulo limathandizanso anthu kukhala ndi chiyembekezo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma panopa anasiya kulisindikiza.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Mayi anga anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti ndikumawerenga Baibulo