Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Nkhani Yokhudza Zozizwitsa Ili Yofunika Kuidziwa Bwino?

N’chifukwa Chiyani Nkhani Yokhudza Zozizwitsa Ili Yofunika Kuidziwa Bwino?

N’chifukwa Chiyani Nkhani Yokhudza Zozizwitsa Ili Yofunika Kuidziwa Bwino?

“Zozizwitsa zimatsutsana ndi sayansi.”​—RICHARD DAWKINS, YEMWE ANALI PULOFESA WA SAYANSI.

“Pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti zozizwitsa zimachitikadi. Zozizwitsa sizitsutsana ndi zimene anthu amakhulupirira pa nkhani yachipembedzo. Zimangosonyeza kuti Mulungu ndi wachikondi ndipo akupitirizabe kuchita chidwi komanso kusamalira zinthu zimene analenga.”​—ROBERT A. LARMER, PULOFESA WA NZERU ZA ANTHU.

KODI mumakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitikadi?” Mawu ali pamwambawa akusonyeza kuti anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi. Koma kodi inuyo mungayankhe bwanji funso limeneli?

N’kutheka kuti zingakuvuteni kuyankha kuti mumakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitikadi. Mwina mumaganiza kuti ngati mungavomereze kuti mumakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitikadi ndiye kuti anthu ena azikuonani ngati mumakhulupirira zamatsenga kapenanso ndinu wosaphunzira. Palinso anthu ambiri amene amakhala ndi maganizo oterewa.

Koma pansi pa mtima mwina mumakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitikadi. N’kutheka kuti mumakhulupirira zozizwitsa zimene zinalembedwa m’Baibulo monga chozizwitsa chogawanitsa madzi a m’Nyanja Yofiira chimene Mose anachita. Mwina mumakhulupiriranso kuti ngakhale masiku ano zozizwitsa zimachitika. Ndipo lipoti limene linali m’buku lina linanena kuti kafukufuku waposachedwapa anasonyeza kuti “anthu ambiri a kumayiko a azungu amakhulupirira zozizwitsa. Mwachitsanzo, anthu ambiri a ku United States ndiponso anthu 38 pa anthu 100 alionse a ku Britain amakhulupirirabe zozizwitsa.” (The Cambridge Companion to Miracles, lokonzedwanso ndi Graham H. Twelftree) Komatu si Akhristu okha amene amakhulupirira nkhani ya zozizwitsa. Buku lina linanena kuti: “Pafupifupi anthu a zipembedzo zonse amakhulupirira” zozizwitsa.​—⁠Britannica Encyclopedia of World Religions.

N’kuthekanso kuti mwina muli m’gulu la anthu amene amanena kuti: “Zimenezo sizikundikhudza ndipo ndilibe nazo ntchito. Ndipotu ine sichinandichitikirepo chozizwitsa chilichonse.” Koma kodi n’chifukwa chiyani nkhani yokhudza zozizwitsa ili yofunika kuidziwa bwino?

Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti muli ndi matenda osachiritsika, ndiye mwapeza kuti m’magazini ina yodalirika muli nkhani yonena za mankhwala amene angotulukiridwa kumene omwe akhoza kukuchiritsani. Kodi simungapeze nthawi yoti muwerenge nkhaniyo kuti mutsimikizire ngati zilidi zoona? Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa padzikoli pachitika zozizwitsa zazikulu ndipo zozizwitsa zimenezi zidzakhudza munthu aliyense. Kodi simukuona kuti m’pofunika kupatula nthawi yoti mufufuze ngati lonjezo limeneli lili loona?

Komabe tisanakambirane kuti zozizwitsa zimenezi zidzakhala zotani, tiyeni tikambirane kaye mayankho a mfundo zitatu zimene anthu omwe sakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitika amakonda kunena.

[Bokosi patsamba 3]

KODI CHOZIZWITSA N’CHIYANI?

Ndi chinthu chovuta kuchimvetsa chimene chimachitika m’njira yosiyana kwambiri ndi mmene zinthu zimachitikira nthawi zonse ndipo anthu amaona kuti pali mphamvu inayake yachilendo imene imathandiza kuti zoterezi zichitike.