Kodi Mukudziwa?
Kodi kale anthu ankatumiza bwanji makalata?
Boma la Perisiya linali ndi anthu apadera amene ankagwira ntchito yotumiza makalata a boma. Buku la m’Baibulo la Esitere limafotokoza mmene zimenezi zinkachitikira. Limati: “Moredekai analemba makalatawo m’dzina la Mfumu Ahasiwero ndi kuwadinda ndi mphete yodindira ya mfumu. Atatero anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma okwera pamahatchi . . . amene anali kuwagwiritsa ntchito potumikira mfumu.” (Esitere 8:10) Aroma ankagwiritsanso ntchito njira yomweyi potumiza makalata a boma komanso okhudza zausilikali.
Anthu wamba, ngati mtumwi Paulo, sankaloledwa kutumiza makalata pogwiritsa ntchito njira imeneyi. Ngati munthu ndi wolemera, ankatha kutuma kapolo wake kuti akamuperekere kalata. Koma anthu ambiri ankangopatsira munthu aliyense amene akulowera kumene kukupita kalatayo. Anthu oterewa ankakhala achibale awo, anzawo, asilikali kapena amalonda. Komabe ankafunika kuonetsetsa kuti munthu amene akumupatsirayo ndi wodalirika ndipo akafikitsadi kalatayo. Baibulo limasonyeza kuti ena mwa makalata amene Paulo analemba ankapatsira Akhristu anzake kuti akamuperekere kumene iwo akupita.—Aefeso 6:21, 22; Akolose 4:7.
Kodi nkhani zamalonda zinkayenda bwanji mu Isiraeli wakale?
Chuma cha dziko la Isiraeli chinkadalira kwambiri ulimi, kuweta ziweto komanso malonda a msintho. Baibulo limatchula za malo ena amene ankachitirapo malonda. Malo amenewa ndi monga “Chipata cha Nkhosa,” “Chipata cha Nsomba” komanso “Chipata cha Mapale.” (Nehemiya 3:1, 3; Yeremiya 19:2) Mayinawa ankatchulidwa potengera zinthu zimene zinkagulitsidwa pamalopo. Baibulo limatchulanso za ‘msewu wa ophika mkate’ wa ku Yerusalemu komanso zinthu zina zimene zinkagulitsidwa.—Yeremiya 37:21.
Kodi mitengo ya zinthu kalelo inali yotani? Buku lina lonena za Baibulo linati: “Pakapita nthawi mitengo ya zinthu inkasintha, choncho n’zovuta kudziwa mmene mitengo ya zinthu inalili kalelo.” Komabe mabuku akale, kuphatikizapo Baibulo, amasonyeza kuti ngakhale pa nthawi imeneyo mitengo ya zinthu inkapitiriza kukwera. Mwachitsanzo, nthawi zambiri akapolo ankagulidwa pogwiritsa ntchito ndalama zachitsulo. Yosefe anagulitsidwa ndi ndalama za siliva 20, zomwe ziyenera kuti anali masekeli okwanira kugulira kapolo m’zaka za m’ma 1700 B.C.E. (Genesis 37:28) Patatha zaka 300 mtengo wa kapolo unakwera kufika pa masekeli 30. (Ekisodo 21:32) Pomafika zaka za m’ma 700 B.C.E., mtengowu unakwera n’kufika pa masekeli 50. (2 Mafumu 15:20) Patapita zaka 200, mu ulamuliro wa Perisiya, mtengo wa kapolo unafika pa masekeli 90 kapena kupitirira. Choncho kukwera mitengo kwa zinthu sikunayambe lero.