Kodi Mukudziwa?
Kodi Ayuda a m’nthawi ya atumwi ankatsatira mwambo wotani poika maliro?
Ayuda ankaika maliro mwamsanga ndipo nthawi zambiri ankaika tsiku lomwelo. Panali zifukwa ziwiri zimene ankachitira zimenezi. Choyamba, munthu akamwalira sankachedwa kuwonongeka chifukwa nyengo ya ku Middle East ndi yotentha kwambiri. Chachiwiri, pa nthawiyo anthu ankaona kuti kuika munthu patatha masiku angapo, kunali kusalemekeza munthuyo komanso achibale ake.
M’Mauthenga Abwino komanso m’buku la Machitidwe, muli nkhani zinayi zonena za maliro amene anaikidwa tsiku lomwelo. (Mateyu 27:57-60; Machitidwe 5:5-10; 7:60–8:2) Zaka zambiri m’mbuyomo, Rakele, mkazi wa Yakobo anamwalira Yakobo ndi banja lake ali pa ulendo. Yakobo sanabwerere kukaika malirowo. Iye anangoika mkazi wakeyo kuphanga “ali m’njira popita . . . ku Betelehemu.”—Genesis 35:19, 20, 27-29.
Nkhani za m’Baibulo zokhudza kuika maliro zimasonyeza kuti Ayuda ankachita zambiri pokonzekera kuika munthu m’manda. Achibale a womwalirayo komanso anzake ankasambitsa thupi lake, kulidzoza mafuta onunkhira kenako n’kulikulunga mu nsalu. (Yohane 19:39, 40; Machitidwe 9:36-41) Anthu okhala pafupi komanso anthu ena ankabwera kudzalira malirowo komanso kudzapepesa banja lofedwalo.—Maliko 5:38, 39.
Kodi Yesu anaikidwa m’manda mofanana ndi mmene Ayuda ankaikira maliro?
Ayuda ambiri ankaika maliro kuphanga lamiyala ndipo ankachita kulisema kuti likhale manda. Miyala yotereyi inkapezeka yambiri ku Isiraeli. Ayuda ankachita zimenezi potsatira zimene makolo awo akale ankachita. Abulahamu, Sara, Isaki, Yakobo ndi ena anaikidwa m’phanga la Makipela pafupi ndi Heburoni.—Genesis 23:19; 25:8, 9; 49:29-31; 50:13.
Yesu anaikidwa m’manda akuphanga ochita kusemedwa. (Maliko 15:46) Nthawi zambiri manda oterewa ankakhala ndi khomo laling’ono. M’katimo, ankakonzamo malo ooneka ngati mashelefu ndipo munthu wa m’banjalo akamwalira ankaikidwa m’mashelefumo. Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankati thupi la munthu womwalirayo likawola, ankasonkhanitsa mafupa ake n’kuwaika m’bokosi lopangidwa ndi mwala. Izi zinkathandiza kuti pazipezeka malo oti adzaike maliro ena m’tsogolo.
Chilamulo cha Mose chinkaletsa Ayuda kuchita mwambo wa maliro pa tsiku la Sabata. Popeza Yesu anamwalira kutatsala maola atatu kuti tsiku la Sabata liyambe, Yosefe wa ku Arimateya ndi anthu ena anamuika m’manda popanda kuchita mwambo wonse wa maliro. (Luka 23:50-56) Chifukwa cha zimenezi, mabwenzi ena a Yesu anapita kumanda ake tsiku la Sabata litatha n’cholinga choti akamalizitse mwambo woika maliro ake.—Maliko 16:1; Luka 24:1.