YANDIKIRANI MULUNGU
‘Amadzaza Mitima Yathu’
Kodi Yehova amatisamaliradi kapena alibe nazo ntchito za mavuto amene anthufe timakumana nawo? Baibulo limapereka yankho lolimbikitsa kwambiri. Mulungu amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. Tsiku lililonse amatichitira zinthu zabwino ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anthu osayamika. Tiyeni tione zimene mtumwi Paulo ananena.—Werengani Machitidwe 14:16, 17.
Polankhula ndi anthu a mumzinda wa Lusitara, omwe sankalambira Mulungu, Paulo ananena kuti: “M’mbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuyenda m’njira zawo. Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.” Kodi mawu amenewa ankatanthauza chiyani kwa anthu amene Paulo ankawalalikira?
Anthu a ku Lusitara sanavutike kumvetsa zimene Paulo ankanena. Zili choncho chifukwa anthuwa ankakonda ulimi komanso ankakhala m’dera limene nthaka yake inali yachonde ndiponso mvula inkagwa bwino. Koma Paulo anawauza kuti Mulungu ndi amene amagwetsa mvula komanso amabweretsa nyengo ya zokolola. Choncho iye anawathandiza kuzindikira mfundo yakuti akamakolola chakudya chambiri n’kumasangalala ndi zakudya zokoma, azikumbukira kuti Mulungu ndi amene wawapatsa zinthuzo.
Mawu amene Paulo anauza anthu a ku Lusitara amatiphunzitsa zinthu zingapo zokhudza Yehova Mulungu.
Yehova amatipatsa ufulu wosankha zochita. Mawu a Paulo anasonyeza kuti Yehova analola anthu omwe sanali Ayuda “kuyenda m’njira zawo.” Buku lina lothandiza anthu omasulira Baibulo linanena kuti mawu amenewa amatanthauza “kuchita zimene akufuna,” kapena “kuchita zimene akuona kuti n’zoyenera.” Yehova satikakamiza kuti tizimulambira. Anatipatsa ufulu woti tizitha kusankha tokha zimene tikufuna kuchita.—Deuteronomo 30:19.
Yehova amafuna kuti timudziwe. Paulo anafotokoza kuti Mulungu “sanangokhala wopanda umboni.” Buku talitchula kale lija linanena kuti mawu amenewa akhozanso kutanthauza kuti “Mulungu wathandiza anthu kumudziwa kuti iye ndi wotani.” Zimene Mulungu analenga zimapereka umboni wosatsutsika wa “makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso,” ndipo ena mwa makhalidwe amenewa ndi ubwino, nzeru, mphamvu ndi chikondi. (Aroma 1:20) Yehova wathandiza anthu kuti amudziwe kudzera m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16, 17) N’zoonekeratu kuti Mulungu amafuna kuti timudziwe.
Tsiku lililonse Mulungu amatichitira zinthu zabwino ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anthu osayamika
Yehova amafuna kuti tizisangalala. Paulo ananenanso kuti Mulungu ‘amadzaza mitima yathu ndi chakudya komanso chimwemwe.’ Ngakhale munthu wochimwa amene sachita zimene Yehova amafuna amadya n’kumasangalala ndi moyo. Komabe, Mulungu amafuna kuti tizikhala osangalala nthawi zonse ndipo zimenezi zingatheke ngati timaphunzira n’kumachita zimene iye amafuna.—Salimo 144:15; Mateyu 5:3.
Tonsefe timasangalala ndi zabwino zimene Yehova amatichitira tsiku lililonse. Choncho inuyo mungachite bwino kuphunzira zimene mungachite kuti muzisonyeza kuyamikira pa zinthu zabwino zomwe Mulungu amakuchitirani.
Mavesi amene mungawerenge mu July