Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Kodi Baibulo ndi Mawudi a Mulungu?
Timayembekezera kuti buku lochokera kwa Mulungu liyenera kukhala lapadera kwambiri. Baibulo ndi buku lotero. Pali Mabaibulo ambirimbiri amene asindikizidwa ndipo ali m’zinenero zambiri. Malangizo amene amapezeka m’Baibulo, amathandiza anthu kusintha n’kukhala abwino.—Werengani 1 Atesalonika 2:13; 2 Timoteyo 3:16.
Tikudziwa kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu chifukwa limalosera molondola za m’tsogolo. Palibe munthu amene angathe kuneneratu zam’tsogolo, pokhapokha atatsogoleredwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo taganizirani za buku la Yesaya. Mpukutu wa bukuli womwe unalembedwa zaka 100 Yesu asanabadwe, unapezeka kuphanga lina pafupi ndi Nyanja Yakufa. Mpukutuwu unanena kuti mzinda wa Babulo udzakhala bwinja. Mawu amenewa anakwaniritsidwa patapita zaka zambiri kuchokera pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi.—Werengani Yesaya 13:19, 20; 2 Petulo 1:20, 21.
Kodi Baibulo linalembedwa bwanji?
Baibulo linalembedwa kwa zaka zoposa 1,600. Anthu 40 amene analemba Baibulo analemba zinthu zogwirizana, pa mutu wankhani umodzi. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Zinatheka chifukwa choti Mulungu ndi amene ankawatsogolera.—Werengani 2 Samueli 23:2.
Nthawi zina Mulungu ankalankhula ndi anthu amene analemba Baibulo kudzera mwa angelo, masomphenya kapena maloto. Nthawi zambiri, Mulungu ankaika m’maganizo a wolembayo mfundo zimene akufuna kuti zilembedwe, ndipo ankalola munthuyo kusankha yekha mawu amene akufuna kugwiritsa ntchito polemba mfundozo.—Werengani Chivumbulutso 1:1; 21:3-5.