Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Zipembedzo Zizichitira Zinthu Pamodzi?
“Kodi zipembedzo zimagwirizanitsa anthu kapena zimawagawanitsa?” Funso limeneli linali m’magazini ina yotchedwa The Sydney Morning Herald. Pa anthu amene anayankha, ambiri ananena kuti zipembedzo zimachititsa kuti anthu asamagwirizane.
KOMA anthu amene amalimbikitsa zoti zipembedzo zizichitira limodzi zinthu, amaona kuti zipembedzo zimagwirizanitsa anthu. Munthu wina amene anayambitsa gulu loti achinyamata a zipembedzo zosiyanasiyana azichitira zinthu pamodzi, dzina lake Eboo Patel, ananena kuti: “Palibe chipembedzo chomwe sichifuna kuti anthu ake azikhala achifundo, . . . azisamalira zinthu zachilengedwe, . . . komanso azikhala ochereza.”
Nthawi zambiri Abuda, Akatolika, Apulotesitanti, Ahindu, Asilamu komanso anthu ena amasonkhana pamodzi kuti akambirane nkhani zokhudza umphawi, ufulu wa anthu, kuletsa ntchito yopanga mabomba komanso kuthandiza anthu kuti azisamalira zinthu zachilengedwe. Anthuwa amakumana pamodzi kuti akambirane zimene angachite kuti azigwirizana komanso kuti azichitira zinthu limodzi. Nthawi zambiri amachitira limodzi zikondwerero, kuyimba, mapemphero, miyambo yoyatsa makandulo komanso zinthu zina.
Kodi zimenezi zingathandizedi kuti zipembedzo zonse zizigwirizana? Kodi Mulungu amagwirizana ndi zoti zipembedzo zizichitira zinthu limodzi, n’cholinga chofuna kuthandiza kuti zinthu ziziyenda bwino padzikoli?
KODI ANTHU AYENERA KUCHITA ZOTSUTSANA NDI BAIBULO CHIFUKWA CHOFUNA KUGWIRIZANA?
Bungwe lina la anthu a zipembedzo zosiyanasiyana, omwe amachitira zinthu limodzi, limadzichemerera kuti lili ndi anthu ochokera m’zipembedzo 200 ndipo limagwira ntchito zake m’mayiko 76. Bungweli limati cholinga chake chachikulu ndi “kuthandiza kuti anthu a zipembedzo zosiyanasiyana azigwirizana.” Koma izi ndi nkhambakamwa chabe, chifukwa si zimene zimachitikadi. Mwachitsanzo, malinga ndi zimene akuluakulu ena a bungweli ananena, pokonza mfundo za bungweli, anafunika kusamala kwambiri kuti asakhumudwitse zipembedzo zina zomwenso ndi mamembala a bungweli chifukwa kupanda kutero zipembedzozo sizikanasainira mfundozo. N’chifukwa chiyani zinali choncho? Chifukwa china n’choti panali kusagwirizana pa nkhani yoti Mulungu atchulidwe mu mfundozo kapena ayi. Zotsatira zake zinali zakuti Mulungu sanatchulidwe.
Ndiye ngati zipembedzo zachita mgwirizano koma sakufuna kuti azitchula Mulungu, kodi mgwirizanowo uli ndi phindu lililonse? Komanso ngati bungweli linapewa kutchula Mulungu mu mfundo zake, likusiyana bwanji ndi mabugwe wamba ongothandiza anthu? Mpakedi kuti bungweli silimadzitchula kuti ndi bungwe lokhudza zachipembedzo koma limati ndi “logwirizanitsa anthu.”
KODI KULIMBIKITSA KUTI ANTHU AZIKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO N’KOKWANIRA?
Munthu wina yemwe amagwirizana ndi zoti zipembedzo zizichitira zinthu pamodzi, dzina lake Dalai Lama, anati: “Zipembedzo zonse zikuluzikulu zimaphunzitsa za chikondi, chifundo komanso kukhululukirana.” Dalai Lama ananenanso kuti: “Anthufe tiyenera kusonyeza makhalidwe amenewa nthawi zonse.”
N’zoona kuti makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri. Chifukwatu pophunzitsa mfundo ya makhalidwe abwino, Yesu anati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) Koma kodi kungolimbikitsa anthu kukhala ndi makhalidwe abwino n’kokwanira?
Ponena za anthu amene ankati ankatumikira Mulungu, mtumwi Paulo anati: “Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.” Kodi vuto la anthuwa linali chiyani? Paulo ananena kuti “posadziwa chilungamo cha Mulungu, iwo sanagonjere chilungamocho koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.” (Aroma 10:2, 3) Popeza anthuwa sankadziwa molondola zimene Mulungu ankafuna kuti azichita, chikhulupiriro chawo komanso zonse zimene ankachita zinali zopanda phindu.—Mateyu 7:21-23.
KODI BAIBULO LIMAVOMEREZA ZOTI ZIPEMBEDZO ZIZICHITIRA LIMODZI ZINTHU?
Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere.” (Mateyu 5:9) Yesu ankachita zimene ankaphunzitsa chifukwa ankalimbikitsa anthu kuti asamachite zachiwawa. (Mateyu 26:52) Komanso ankauza anthu a zipembedzo zonse zimene angachite kuti azikhala mwamtendere ndi ena. Anthu amene ankachita zomwe Yesu ankaphunzitsa ankakondana kwambiri ndipo izi zinachititsa kuti azigwirizana. (Akolose 3:14) Koma kodi cholinga chachikulu cha Yesu chinali kugwirizanitsa anthu osiyanasiyana kuti azikhala mwamtendere basi? Kodi iye ankachita mapemphero limodzi ndi anthu azipembedzo zina?
Afarisi komanso Asaduki, omwe anali atsogoleri achipembedzo, ankadana kwambiri ndi Yesu mpaka ankafuna kumupha. Kodi Yesu anatani? Analangiza ophunzira ake kuti: “Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu.” (Mateyu 15:14) Yesu anakana kuchita zinthu limodzi ndi anthu amenewa.
Patapita nthawi, mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa mumzinda wa Korinto ku Girisi. Mzinda umenewu unkadziwika kuti munali anthu azikhalidwe komanso zipembedzo zosiyanasiyana. Kodi Akhristu a kumeneko ankayenera kuchita chiyani? Mtumwi Paulo anawauza kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.” Kodi n’chifukwa chiyani Paulo anawauza zimenezi? Iye anati: “Pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angagawane chiyani ndi wosakhulupirira?” Kenako anawapatsa malangizo akuti: “Tulukani pakati pawo, lekanani nawo.”—2 Akorinto 6:14, 15, 17.
Apatu n’zoonekeratu kuti Baibulo limaletsa zoti anthu azipembedzo zosiyanasiyana azichitira zinthu pamodzi. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Nanga kodi n’chiyani chingathandize kuti anthu padzikoli azigwirizana?’
CHIMENE CHINGATHANDIZE KUTI ANTHU AKHALEDI OGWIRIZANA
Asayansi amene anakhazikitsa malo ochitira kafukufuku mlengalenga, anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa panali mgwirizano pakati pa mayiko 15 amene ankagwira ntchitoyi. Zimenezi zinatheka chifukwa choti mayiko onsewo anagwirizana ndi mfundo zoyendetsera ntchitoyi.
Koma izi n’zosiyana ndi zimene zipembedzo zosiyanasiyana, zomwe zimapangira zinthu pamodzi, zimachita. Ngakhale kuti iwo amati amalimbikitsa mgwirizano komanso kulolerana, sizitheka kuti azikhulupirira zofanana. Zotsatira zake n’zoti akulepherabe kugwirizana pa nkhani zokhudza makhalidwe abwino komanso ziphunzitso.
M’Baibulo muli mfundo zimene Mulungu amafuna kuti anthu aziyendera. Tiyenera kutsatira mfundo zimenezi pa moyo wathu. Anthu amene amayendera mfundo zimenezi, aphunzira kugwira ntchito limodzi mwamtendere komanso mogwirizana. Iwo sakumana ndi mavuto amene amakhalapo chifukwa cha kusiyana mafuko kapena zipembedzo. Mulungu ananeneratu kuti zimenezi zidzachitika pamene anati: “Ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.” Choncho mgwirizano umatheka chifukwa cha kulankhula “chilankhulo choyera,” kapena kuti kutsatira mfundo za Mulungu zokhudza kulambira.—Zefaniya 3:9; Yesaya 2:2-4.
A Mboni za Yehova akukuitanani kuti mudzapite ku Nyumba ya Ufumu ya kufupi ndi kwanu kuti mudzaone nokha zoti iwo ndi anthu amtendere komanso ogwirizana.—Salimo 133:1.