Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinkamenya Nkhondo Yangayanga Yolimbana Ndi Kupanda Chilungamo Komanso Chiwawa

Ndinkamenya Nkhondo Yangayanga Yolimbana Ndi Kupanda Chilungamo Komanso Chiwawa
  • CHAKA CHOBADWA: 1960

  • DZIKO: LEBANON

  • POYAMBA: NDINALI KATSWIRI WA KUNG FU

KALE LANGA:

Ndinabadwira mumzinda wa Rmaysh, pafupi ndi malire a dziko la Israel ndi Lebanon. Pa nthawiyi kuderali n’kuti kuli nkhondo yapachiweniweni. Ndimakumbukirabe phokoso la kuphulika kwa mabomba lomwe linkamveka ponseponse komanso anthu amene ndinkawaona ataduka miyendo ndi mikono. Moyo unali wovuta kwambiri ndipo chiwawa komanso zinthu zophwanya malamulo zinali ponseponse.

Banja lathu linali lachikatolika ndipo tinalipo anthu 12. Bambo anga ankatanganidwa kwambiri kuti apeze ndalama zosamalira banja lathu. Koma mayi ankaonetsetsa kuti ana tonse tinkapita kutchalitchi. Patapita nthawi ndinayamba kuona kuti tchalitchi nachonso chinkalephera kuthandiza anthu wamba.

Ndili mnyamata, ndinayamba kuchita chidwi ndi masewera a kung fu. Ndinapita kusukulu inayake komwe ndinakaphunzira zambiri za masewerawa ndipo ndinakhala katswiri. Ndinkaganiza kuti, ‘Sindingathe kuthetsa nkhondo komabe ndikhoza kuchititsa kuti anthu asiye kuchita zachiwawa.’ Ndinkati ndikangoona anthu akumenyana, nthawi yomweyo ndinkalowerera. Mwachibadwa ndinali wa mtima wapachala moti sindinkachedwa kulusa. Anthu ambiri a kum’mwera kwa Lebanon ankandiopa chifukwa sindinkanyengerera ndikaona anthu akuchita zinthu zopanda chilungamo komanso zachiwawa.

Mu 1980, ndinalowa m’gulu linalake lochita kung fu lomwe linali mumzinda wa Beirut. Popeza nthawiyi n’kuti kuli nkhondo, maroketi komanso maboma sankati aphulika liti. Ngakhale zinali chonchi, ine ndinkapitabe kukaphunzira kung fu. Maganizo anga onse anali pa masewerawa ndipo ndinkayesetsa kuti ndifanane ndi katswiri wina wa masewerawa, dzina lake Bruce Lee. Ndinatengera zinthu zambiri kwa katswiriyu monga kametedwe, kayendedwe komanso mmene ankakuwira pochita kung fu. Nthawi zonse ndinkakhala wolusa ndipo sindinkaonetsa mano.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Cholinga changa chinali choti ndikakhale katswiri wa kung fu ku China. Tsiku lina ndikuchita masewerawa pokonzekera ulendo wopita ku China, ndinamva kugogoda pakhomo. Anali mnzanga winawake ndipo anabwera ndi a Mboni za Yehova awiri. Pa nthawiyi n’kuti  nditavala zovala zochitira masewera ndipo thukuta linali kamukamu. Nditacheza ndi a Mboniwa kwa kanthawi ndinawauza kuti, “Inetu palibe chimene ndimadziwa chokhudza Baibulo.” Sindinkadziwa kuti chimenechi chikhala chiyambi cha kusintha kwa moyo wanga.

A Mboniwa anandionetsa kuchokera m’Baibulo chifukwa chake anthu sangathe kuthetseratu chiwawa ndi zinthu zopanda chilungamo. Anandifotokozeranso kuti Satana Mdyerekezi ndi amene amayambitsa mavuto amenewa. (Chivumbulutso 12:12) A Mboniwo ankaoneka kuti ndi anthu okonda mtendere komanso ankalankhula mosonyeza kuti akukhulupirira zimene akunenazo. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri. Komanso ndinasangalala kwambiri atandiuza kuti Mulungu ali ndi dzina. (Salimo 83:18) Anandisonyezanso lemba la 1 Timoteyo 4:8 limene limati: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono, koma kukhala wodzipereka kwa Mulungu n’kopindulitsa m’zonse, chifukwa kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwerawo.” Mawu amenewa anandikhudza mtima kwambiri.

Koma anthu a kwathu anauza a Mboniwa kuti asadzabwerenso ndipo ndinadandaula kwambiri ndi zimenezi. Komabe ndinaganiza zosiya kuchita kung fu n’kuyamba kuphunzira Baibulo. Azichimwene anga sanagwirizane ndi zimenezi. Koma ineyo ndinkafunitsitsa kuti ndipeze a Mboni za Yehova kuti ayambe kundiphunzitsa Baibulo.

Ndinayesetsa kufufuza a Mboni koma sindinawapeze. Pa nthawiyi n’kutinso ndili ndi chisoni chifukwa cha imfa ya bambo anga komanso chifukwa cha mavuto ena amene banja lathu linkakumana nawo. Ndinayamba kugwira ntchito pa kampani inayake ya zomangamanga. Tsiku lina munthu wina amene ndinkagwira naye ntchito yemwenso anali wa Mboni, dzina lake Adel, anandifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukuoneka wosasangalala?’ Kenako anayamba kundiuza zimene Baibulo limanena zoti akufa adzauka. Adel anali woleza mtima, wachikondi komanso wokoma mtima ndipo pasanapite nthawi anayamba kundiphunzitsa Baibulo.

Nditayamba kudziwa zambiri, ndinaona kuti ndikuyenera kusintha zinthu zambiri pa moyo wanga. Komatu kuchita zimenezi sikunali kophweka chifukwa zinkandivuta kuugwira mtima ndipo sindinkachedwa kulusa. Komabe Baibulo linandithandiza kuti ndizitha kudziletsa komanso kuugwira mtima. Mwachitsanzo, palemba la Mateyu 5:44 pali mawu a Yesu akuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” Komanso lemba la Aroma 12:19 limati: “Musabwezere choipa, . . . ‘“Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,” watero Yehova.’” Kutsatira malemba ngati amenewa kunandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wa mumtima.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa ndine wa Mboni. Ngakhale kuti poyamba azichimwene anga sankafuna kuti ndiziphunzira Baibulo ndi a Mboni, tsopano anayamba kuwalemekeza. Ndipotu mchimwene wanga wina nayenso ndi wa Mboni ndipo mayi anga ankanena zabwino zokhudza a Mboni za Yehova mpaka pamene anamwalira.

Ndinakwatira mkazi wabwino komanso wokhulupirika, dzina lake Anita, ndipo ndimagwira naye limodzi ntchito yolalikira nthawi zonse. Kuyambira m’chaka cha 2000, ine ndi Anita timakhala mumzinda wa Eskilstuna, ku Sweden, komwe timathandiza anthu kuphunzira Baibulo m’Chiarabu.

Panopa ndimamverabe chisoni anthu amene akuvutika chifukwa cha zinthu zachiwawa zomwe anthu ena amachita. Koma popeza ndimadziwa chifukwa chake zinthu zoipa zimachitika, komanso ndimadziwa kuti posachedwapa Mulungu athetsa mavuto onse, sindidandaula kwambiri ndipo ndimakhala ndi mtendere wa mumtima.—Salimo 37:29.

Ine ndi mkazi wanga timasangalala kuphunzitsa anthu za Yehova