Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA

Kodi Mumalankhulana ndi Mulungu?

Kodi Mumalankhulana ndi Mulungu?

Mabwenzi apamtima amalankhulana pafupipafupi. Amalankhulana kudzera pa foni, kalata, Intaneti kapena kutumizirana imelo. Ifenso kuti tikhale anzake apamtima a Mulungu, tiyenera kumalankhula naye pafupipafupi. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

Tingalankhule ndi Yehova popemphera kwa iye. Komabe, tikamapemphera sitiyenera kulankhula motayirira ngati tikulankhula ndi munthu wamsinkhu wathu. Tiyenera kuzindikira kuti tikulankhula ndi Mlengi wathu, yemwe ndi Wamkulu m’chilengedwe chonse. Choncho, tiyenera kulankhula naye mwaulemu kwambiri. Komabe, pali zinthu zomwe tiyenera kuchita kuti Mulungu azimva mapemphero athu. Tiyeni tikambirane zitatu mwa zinthu zimenezi.

Choyamba, tiyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu yekha basi, osati kwa Yesu, oyera mtima kapena kwa zifaniziro. (Ekisodo 20:4, 5) Pa nkhaniyi Baibulo limati: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Chachiwiri, tiyenera kupemphera kudzera m’dzina la Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu. Yesu anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Chachitatu, mapemphero athu ayenera kukhala ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Baibulo limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” *1 Yohane 5:14.

Mabwenzi apamtima amalankhulana pafupipafupi

Komatu, ubwenzi sungapite patali ngati munthu mmodzi yekha ndi amene amalankhula. Anthu omwe ndi mabwenzi a pamtima amalankhulana ndipo zimenezi ndi zomwe zimalimbitsa ubwenzi wawowo. Choncho, nafenso tiyenera kulola Mulungu kuti azitilankhula ndipo tiyenera kumvetsera. Kodi mukudziwa njira imene Mulungu amagwiritsa ntchito akafuna kulankhula nafe?

Masiku ano, Yehova Mulungu amalankhula nafe kudzera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. (2 Timoteyo 3:16, 17) N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyerekeze kuti mwalandira kalata yochokera kwa mnzanu wapamtima. Mutawerenga kalatayo mungauze anthu ena nkhani imene ili m’kalatayo, ndipo munganene kuti: “Nkhani imeneyi wandiuza ndi mnzanga.” Komatu mnzanuyo sanakuuzeni nkhaniyo pamasom’pamaso, koma wachita kukulemberani kalata. Mofanana ndi zimenezi, mukamawerenga Baibulo, Yehova amakhala akulankhula nanu. N’chifukwa chake Gina, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ananena kuti: “Ndimaona kuti, ngati ndikufuna kuti Yehova azindiona kuti ndine mnzake, ndiyenera kuwerenga Baibulo chifukwa ndi kalata imene wandilembera. Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kwandithandiza kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu.” Kodi inuyo mumalola kuti Yehova azilankhula nanu tsiku lililonse powerenga Baibulo tsiku ndi tsiku? Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muziona kuti Mulungu ndi mnzanu wapamtima.

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene pemphero limatithandizira kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, werengani mutu 17 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.