Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira imfa ya Yesu?
Zinali zofunika kuti Yesu atifere kuti anthufe tidzapeze moyo wosatha. Anthu sanalengedwe kuti azichita zoipa, azidwala komanso kuti azifa. (Genesis 1:31) Koma zimenezi zimachitika chifukwa tonse tinatengera uchimo kuchokera kwa Adamu. Choncho, Yesu anapereka moyo wake kuti atiwombole ku uchimo ndi imfa.—Werengani Mateyu 20:28; Aroma 6:23.
Mulungu anasonyeza kuti amatikonda kwambiri potumiza Mwana wake kuti adzatifere. (1 Yohane 4:9, 10) Yesu anauza ophunzira ake kuti azikumbukira imfa yake pochita mwambo wachidule ndipo azigwiritsa ntchito mkate ndi vinyo. A Mboni za Yehova amachita mwambo umenewu chaka chilichonse posonyeza kuyamikira chikondi chomwe Mulungu komanso Yesu anatisonyeza.—Werengani Luka 22:19, 20.
Kodi ndani ayenera kudya mkate komanso kumwa vinyo?
Pa nthawi imene Yesu ankauza ophunzira ake kuti azikumbukira imfa yake, ananenanso za pangano lina lapadera. (Mateyu 26:26-28) Panganoli linali loti ophunzirawo ndi anthu ena ochepa adzakhala mafumu komanso ansembe ndi Yesu kumwamba. Ngakhale kuti anthu ambiri amapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu, amene ayenera kudya mkate komanso kumwa vinyo ndi okhawo amene ali m’panganoli.—Werengani Chivumbulutso 5:10.
Kwa zaka pafupifupi 2,000, Yehova wakhala akusankha anthu oti akalamulire ndi Yesu kumwamba. (Luka 12:32) Anthuwa ndi ochepa poyerekeza ndi amene adzakhale padziko lapansi mpaka kalekale.—Werengani Chivumbulutso 7:4, 9, 17.