Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Chuma Chomwe Chakhala ku banja Lathu kwa Mibadwo 7

Chuma Chomwe Chakhala ku banja Lathu kwa Mibadwo 7

Anthu amanena kuti ndimafanana ndi bambo anga. Amati mmene ndimaimira, maso anga komanso nthabwala zomwe ndimachita, ndi ndendende ngati bambo anga. Komatu si zokhazi. Palinso chuma chamtengo wapatali chomwe chakhala ku banja lathu kwa mibadwo 7. Dikirani ndikufotokozereni.

Bambo akundiuza mbiri ya ku banja kwathu

A Thomas (1) * Williams, omwe anali agogo awo a azigogo anga, anabadwa pa 20 January, 1815 ndipo anabadwira m’tauni ya Horncastle ku England. Koma patangotha zaka ziwiri a Thomas atabadwa, mayi awo anamwalira. Choncho a Thomas, mchemwali wawo ndi azichimwene awo awiri analeredwa ndi bambo awo, omwe anali a John Williams. Bambo awowa anawaphunzitsa ntchito ya ukalipentala. Koma a Thomas atakula sanasankhe kukhala kalipentala.

Patapita nthawi, m’busa wina dzina lake John Wesley, anachoka m’tchalitchi cha ku England n’kuyambitsa kagulu kake. Izi zinapangitsa kuti anthu ambiri a ku England ayambenso kukonda zopemphera. Kagulu kamene John Wesley anayambitsaka, kankalimbikitsa anthu kuphunzira Baibulo komanso kulalikira. Zimene m’busayu ankalalikira zinafala kwambiri ndipo banja la a Williams linalowa m’kaguluka. A Thomas anayamba kulalikira ndipo kenako anakakhala mmishonale m’chigawo cha South Pacific. Mu July 1840, a Thomas ndi a Mary, (2) omwe anali atangokwatirana kumene, anapita kuchilumba cha Lakeba * ku Fiji. Chilumbachi chinapangidwa ndi chiphalaphala chochokera pansi pa nthaka. Pa nthawi imene a Thomas ndi a Mary ankafika pachilumbapa, anthu ambiri a pachilumbapa ankadya anthu anzawo.

ANKAKHALA PACHILUMBA POMWE ANTHU ANKADYA ANZAWO

Banjali litangofika kumene pachilumbapa, linakumana ndi mavuto adzaoneni. Ankagwira ntchito yakalavulagaga kwa maola ambiri, kunja kukutentha. Pachilumbapa pankachitika zinthu zambiri zoipa monga nkhondo, kuzunza akazi amasiye, kupha ana ndiponso kudya anthu. Komanso anthu sankamvetsera uthenga umene banjali linkalalikira. Patapita nthawi a Mary ndi mwana wawo woyamba, dzina lake John, anadwala mwakayakaya. Mu 1843, a Thomas analemba kuti: “Pa nthawiyo, ndinada nkhawa kwambiri . . . ndipo ndinasoweratu mtengo wogwira.” Komabe iwo ndi akazi awo anatha kupirira mavutowa chifukwa ankakhulupirira kwambiri Yehova.

Popeza a Thomas anali kalipentala, anamanga nyumba potengera mapulani a mmene anthu a ku Europe ankamangira nyumba zawo. Nyumbayi inali yokongola zedi ndipo anthu a m’derali anachita nayo chidwi kwambiri. Nyumbayi itatsala pang’ono kutha, akazi awo anabereka mwana wamwamuna wachiwiri, dzina lake Thomas Whitton (3) Williams. Ameneyu ndi amene anali mumzera womwe bambo anga anabadwira.

Mu 1843, a Thomas anathandiza nawo kumasulira Uthenga Wabwino wa Yohane m’Chifiji, ngakhale kuti imeneyi inali ntchito yovuta kwambiri. * Iwo anali katswiri wodziwa za chikhalidwe cha anthu komanso anali ndi luso lotha kuzindikira zinthu. Mu 1858, a Thomas analemba buku m’Chifiji lomwe anafotokozamo zokhudza zimene anapeza pa kufufuza kwawo. (Fiji and the Fijians) Bukuli ndi limodzi mwa mabuku akale ofotokoza mbiri ya ku Fiji.

A Thomas ndi banja lawo anakhala ku Fiji zaka 13 ndipo pa zaka zonsezi ankagwira ntchito yokhetsa thukuta. Koma kenako anayamba kudwaladwala ndipo anasamukira ku Australia. Patapita nthawi yaitali akugwira ntchito monga m’busa, a Thomas anamwalira mumzinda wa Ballarat ku Victoria m’chaka cha 1891.

ANAPEZA CHUMA CHAMTENGO WAPATALI KUPOSA GOLIDE

Mu 1883, a Thomas Whitton Williams ndi akazi awo a Phoebe, (4) anasamukira mumzinda wa Perth ku Western Australia. Pa nthawiyi, mwana wawo wachiwiri dzina lake Arthur Bakewell (5) Williams, n’kuti ali ndi zaka 9. A Arthur analinso mumzera womwe bambo anga anabadwira.

A Arthur ali ndi zaka 22, anayamba kugwira ntchito ku Kalgoorlie pamgodi wina wagolide womwe unali pa mtunda wa makilomita 600 kum’mawa kwa mzinda wa Perth. Ali kumeneku, anawerenga mabuku a Ophunzira Baibulo. Limeneli ndi dzina lomwe a Mboni za Yehova ankadziwika nalo pa nthawiyo. Analembetsanso kuti Ophunzira Baibulo aziwatumizira magazini a Zion’s Watch Tower. A Arthur ankasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira m’magaziniwa moti anayamba kuuza ena zimenezi komanso kuchititsa misonkhano yophunzitsa Baibulo. Kagulu ka anthu komwe kankabwera kudzachita misonkhanoyi kanakula n’kukhala a Mboni za Yehova ambirimbiri omwe ali ku Western Australia masiku ano.

A Arthur anauzanso anthu a m’banja lawo zomwe ankaphunzira. Abambo awo, a Thomas Whitton, anagwirizana ndi zoti a Arthur akhale m’gulu la Ophunzira Baibulo. Koma pasanapite nthawi yaitali, bambo awowa anamwalira. Amayi a a Arthur analowanso m’gulu la Ophunzira Baibulo. Komanso a Violet ndi a Mary omwe anali azichemwali a a Arthur, nawonso anakhala Ophunzira Baibulo. Patapita nthawi, a Violet anakhala mpainiya. Limeneli ndi dzina lomwe a Mboni amene amatha nthawi yaitali akulalikira amadziwika nalo. A Arthur ananena kuti a Violet anali “mpainiya wabwino komanso wodzipereka kwambiri mu Western Australia monse.” Chitsanzo chabwino cha a Violet chinathandiza kwambiri a Arthur komanso mibadwo yotsatira ya banja la a Williams.

Patapita nthawi a Arthur anakwatira n’kusamukira m’tauni ya Donnybrook, yomwe ili kum’mwera chakumadzulo kwa Western Australia. Anthu ambiri a m’tauniyi ankalima zipatso. Ali kumeneko anthu anawapatsa dzina loti, “Nganga Yamisala ya 1914.” Anawapatsa dzinali chifukwa ankalengeza mwakhama ulosi wa m’Baibulo wokhudza chaka cha 1914. * Koma anasiya kuwanyozaku pamene nkhondo yoyamba yapadziko lonse inayamba. A Arthur ankaika mabuku othandiza kuphunzira Baibulo pawindo ya sitolo yawo ndipo ankakonda kulalikira makasitomala awo. Komanso iwo sankagwirizana ndi mfundo yoti kuli Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera. Choncho anaika chikwangwani pawindo la sitolo yawoyo, chonena kuti aliyense amene angapereke umboni wa m’Baibulo woti mfundoyi ndi yolondola, adzamupatsa ndalama zokwana mapaundi 100 a ku Australia. Koma palibe anabwera.

Kunyumba kwa a Arthur n’kumene anthu ankakumana kuti aphunzire Baibulo komanso kuti achite misonkhano ya mpingo m’tauni yonse ya Donnybrook. Kenako, a Arthur anamanga Nyumba ya Ufumu m’tauniyi ndipo iyi inali imodzi mwa Nyumba za Ufumu zoyambirira ku Western Australia. A Arthur ankakonda kuvala suti ndi taye n’kukwera hatchi yawo, dzina lake Doll, ndipo ankalalikira uthenga wa m’Baibulo kuzungulira m’tauni yonse ya Donnybrook. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka zoposa 70 ndipo anthu ankawalemekeza kwambiri.

Ngakhale kuti a Arthur anali ofatsa, ankalalikira uthenga wa m’Baibulo mwakhama ndipo ana awo anatengera chitsanzo chawochi. Mwana wawo wamkazi, dzina lake Florence (6) anakakhala mmishonale ku India. Ana awo aamuna awiri, a Arthur Lindsay (7) ndi a Thomas, anakhalanso akulu mumpingo kwa nthawi yaitali ngati bambo awo.

MAAPOZI OKOMA KWAMBIRI

A Arthur Lindsay Williams, omwe anali bambo awo a agogo anga, anali achifundo komanso aulemu moti anthu ankawakonda chifukwa cha zimenezi. Ankayesetsa kupeza nthawi yocheza ndi anthu komanso kuwathandiza. Analinso katswiri wodula mitengo moti pa zaka 12 analandira mphoto ka 18, pa mpikisano wodula mitengo.

Komabe tsiku lina, a Arthur anakhumudwa kwambiri ndi zimene mwana wawo wazaka ziwiri, dzina lake Ronald, (8) anachita. A Ronald anadula kamtengo ka maapozi komwe kanali pafupi ndi nyumba yawo. Amayi a Ronald anamanga bandeji kamtengoko ndipo katakula kanabereka maapozi okoma kwambiri. Maapozi amenewa anali osiyana ndi maapozi ena, moti anthu anawapatsa dzina loti, Lady Williams. Maapoziwa amakhala apinki ndipo ndi odziwika kwambiri padziko lonse. A Ronald ndi omwe anadzakhala agogo anga.

A Ronald atakula, anayamba ntchito ya zomangamanga. Iwowa ndi agogo aakazi anathandiza nawo pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi malo ena a Mboni za Yehova ku Australia ndi pazilumba za Solomon. Panopa a Ronald ali ndi zaka pafupifupi 80 ndipo ndi mkulu mumpingo komanso amathandizabe kumanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu ku Western Australia.

NDIMAONA KUTI ANATISIYIRA CHUMA CHAMTENGO WAPATALI

Bambo anga omwe ndi a Geoffrey (9) Williams, anatengera chitsanzo cha makolo awochi. Iwo limodzi ndi amayi, dzina lawo a Janice, (10) anayesetsa kuphunzitsa ineyo (12) komanso mchemwali wanga, Katharine (11) mfundo za m’Baibulo. Ndili ndi zaka 13, ndinayamba kutsatira mfundozi pa moyo wanga chifukwa ndimaona kuti ndi zofunika kwambiri. Tili pa msonkhano, a John E. Barr a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova analimbikitsa achinyamata kuti: “Muli ndi mwayi woti mungathe kudziwa ndi kukonda Yehova. Chonde, musataye mwayi umenewu.” Usiku wa tsiku lomwelo ndinauza Yehova m’pemphero kuti ndikufuna kumutumikira ndipo patapita nthawi ndinabatizidwa. Patatha zaka ziwiri, ndinakhala mpainiya.

Panopa, ine ndi mkazi wanga Chloe, ndife apainiya ndipo timalalikira m’tauni ya Tom Price. Tauniyi, ili kumpoto chakumadzulo kwa Western Australia. Komabe timagwira maganyu kuti tizipeza zofunika pa moyo. Makolo anga komanso Katharine ndi mwamuna wake Andrew, nawonso ndi apainiya m’tauni ya Port Hedland. Tauniyi ili pa mtunda wamakilomita 420 kumpoto kwa Western Australia. Bambo ndi ineyo ndife akulu m’mipingo ya Mboni za Yehova ya m’madera omwe timakhala.

Zonsezi zinayamba pamene a Thomas Williams aja, anasankha kutumikira Yehova zaka zambiri zapitazo ndipo ineyo ndi m’badwo wa 7 kuchokera pa iwo. Ndimaona kuti bambo komanso azigogo athu anatisiyira chuma chamtengo wapatali.

^ ndime 5 Manambalawa akusonyeza zithunzi za anthuwa zomwe zili patsamba 12 ndi 13.

^ ndime 6 Chilumbachi chili kum’mawa kwa dziko la Fiji ndipo poyamba chinkadziwika kuti Lakemba.

^ ndime 10 Mmishonale wina, dzina lake John Hunt, ndi amene anamasulira mbali yaikulu ya Chipangano Chatsopano m’Chifiji. Baibulo lomwe anamasuliralo linasindikizidwa mu 1847. Baibuloli ndi lofunika kwambiri chifukwa mumapezeka dzina la Mulungu lakuti, “Yehova” pa Maliko 12:36, Luka 20:42 ndi pa Machitidwe 2:34.

^ ndime 16 Onani Zakumapeto m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pamutu wakuti, “1914 ndi Chaka Chofunika Kwambiri M’maulosi a Baibulo.” Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.ps8318.com/ny.