Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Wandichitira Zazikulu

Yehova Wandichitira Zazikulu

Ndili mnyamata ndinkakonda kucheza ndi anzanga, kusambira komanso kuponya mpira. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 17 zokha ndipo ndinkaona kuti tsogolo langa ndi lowala. Koma zimene zinachitika tsiku lina madzulo zinasintha tsogolo langa. Ndinachita ngozi yoopsa ya njinga yamoto yomwe inachititsa kuti ziwalo zanga zisiye kugwira ntchito kuyambira pakhosi mpaka kumiyendo. Zimenezi zinachitika zaka 30 zapitazo ndipo mpaka pano sindichoka pabedi.

Ndinakulira mumzinda wa Alicante womwe uli kum’mawa kwa dziko la Spain. Ndili mnyamata ndinkangoyendayenda chifukwa makolo anga sankandisamalira. Pafupi ndi nyumba yathu panali shopu yokonzerapo matayala owonongeka ndipo ndinayamba kucheza ndi José María yemwe ankagwira ntchito pashopuyo. José anali munthu wabwino kwambiri ndipo ankandikonda kuposa makolo anga. Ndikakhala pa mavuto ankandithandiza moti ndinkamuona ngati mchimwene wanga komanso mnzanga ngakhale kuti anali wamkulu kwa ine ndi zaka 20.

Nthawi ina José María anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Zinkachita kuonekeratu kuti ankasangalala ndi zimene akuphunzira m’Baibulo ndipo nthawi zambiri ankandiuza zimene waphunzira. Ndinkamvetsera mwaulemu koma ndinalibe nazo ntchito kwenikweni. Popeza nthawiyi ndinali wachinyamata, ndinkatanganidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. Koma pasanapite nthawi zinthu zinasintha.

NGOZI IMENE INASINTHA MOYO WANGA

Sindikonda kulankhula kwambiri zimene zinachititsa kuti ndivulale koma zomwe ndinganene n’zakuti ndinavulala chifukwa cha chibwana komanso kupusa. Koma ngoziyi inawononga tsogolo langa. Ngoziyi isanachitike ndinali mnyamata wamphamvu zake koma itachitika zinthu zinasintha moti ndinkalephera kuchita chilichonse ndipo ndinagonekedwa m’chipatala. Zinali zovuta kuti ndivomereze zimene zinandichitikirazo ndipo ndinkangoti bola kufa.

José María anabwera kudzandiona, ndipo atachoka anakauza a Mboni za Yehova a ku mpingo wake kuti azidzandiona kuchipatalako. A Mboniwo ankabwera kawirikawiri ndipo zimenezi zinandikhudza kwambiri. Atangondichotsa kuchipinda cha anthu odwala mwakayakaya, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboniwo. Ndinazindikira chifukwa chimene anthu amavutikira ndi kufa komanso chimene Mulungu amalolera kuti zoipa zizichitika. Ndinaphunziranso zinthu zimene Mulungu analonjeza kuti zidzachitika mtsogolo, pa nthawi imene padziko lonse lapansi padzakhala anthu abwino okhaokha ndipo sipadzakhala munthu wonena kuti: “Ndikudwala.” (Yesaya 33:24) Apa ndinazindikira kuti ndili ndi tsogolo labwino kwambiri.

Nditatuluka m’chipatala, ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo ndinadziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova kwa nthawi yochepa. Ndinayambanso kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo ndinkalalikira nawo. Pa November 5, 1988 ndinabatizidwa m’malo apadera amene anakonzedwa ndipo pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 20. Yehova Mulungu anandithandiza kuti ndiyambenso kusangalala ndi kuona kuti moyo wanga uli ndi tsogolo. Kodi ndikanasonyeza bwanji kuti ndikuyamikira zimene Yehova wandichitira?

NDIKUTUMIKIRABE YEHOVA NGAKHALE KUTI NDINE WOLUMALA

Ndinkafunitsitsa kutumikira Yehova moti sindinalole kuti kulumala kwanga kundilepheretse kuchita zimenezi. (1 Timoteyo 4:15) Poyamba zinali zovuta chifukwa makolo anga sankafuna kuti ndikhale wa Mboni za Yehova. Koma a Mboni anzanga ankandikonda ngati m’bale wawo weniweni. Ankandithandiza kuti ndizipita kumisonkhano komanso kuti ndizilalikira.

Patapita nthawi matenda anakula ndipo ndinkafunika kumasamaliridwa mwapadera masana ndi usiku womwe. Ndinafufuza kwa nthawi yaitali malo abwino osamalira anthu olumala ndipo ndinawapeza mumzinda wa Valencia. Malowa ali pamtunda wa makilomita 160 kumpoto kwa dera la Alicante ndipo kunangokhala ngati kwathu.

Ndimayesetsabe kulalikira ngakhale kuti sindichoka pabedi

Ndikupitirizabe kutumikira Yehova ngakhale kuti panopa sindichoka pabedi. Ndinagula kompyuta pogwiritsa ntchito ndalama zomwe ndimalandira chifukwa chakuti ndine wolumala ndipo ndinaiika pafupi ndi bedi langa. Ndinagulanso foni ya m’manja ndipo m’mawa uliwonse, munthu amene amandisamalira amandiyatsira kompyuta ndi foniyi. Kuti ndichite zinthu zina ndi zina pa kompyuta, ndimagwiritsa ntchito kachipangizo kenakake komwe ndimakayendetsa ndi chibwano. Palinso kandodo kapadera komwe ndimakaika pakamwa ndipo ndimakagwiritsa ntchito polemba pakompyuta ndi poimba foni.

Ndimaimba foni pogwiritsa ntchito kandodo

Zipangizozi zimandithandiza m’njira zambiri. Mwachitsanzo, ndimakwanitsa kugwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org komanso LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower ndipo zinthu zimenezi zandithandiza kwambiri. Tsiku lililonse ndimaphunzira Baibulo komanso kufufuza nkhani m’mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ndimachita zimenezi kuti ndimudziwe bwino Yehova komanso makhalidwe ake. Ndikasowa wocheza naye kapena ndikayamba kudandaula, ndimapeza zinthu pawebusaiti ya jw.org zomwe zimandilimbikitsa.

Ngakhale kuti sindimayenda n’kupita kumisonkhano, ndimachita nawobe zinthu zina monga kuyankha, kupemphera, kukamba nkhani, kuwerenga pa phunziro la Nsanja ya Olonda komanso kumvetsera misonkhano. Zimenezi zimatheka chifukwa chakuti misonkhano yonse imalumikizidwa pakompyuta yanga moti ndimaona kuti ndikusonkhana ndi a Mboni anzanga.

Kompyuta komanso foni yanga zimandithandizanso kuti ndizilalikira. Popeza ndimangogona pabedi, sindingakwanitse kukalalikira kunyumba ndi nyumba ngati mmene a Mboni ena onse amachitira. Koma zipangizozi zimandithandiza kuti ndiziuzabe anthu zimene ndimakhulupirira ngakhale kuti ndine wolumala. Ndimasangalala kwambiri kulalikira pogwiritsa ntchito foni ndipo akulu a mumpingo wathu anandipempha kuti ndiziyang’anira ntchito yolalikira pa foni. Izi zimathandiza kuti a Mboni enanso amene sangathe kuchoka pakhomo chifukwa cha mavuto ena azitha kulalikira.

Akuchititsa phunziro la Baibulo

Koma sikuti ndimangodalira kompyuta ndi telefoni kuti ndilankhule ndi anthu. Tsiku lililonse kumabwera anzanga kudzacheza nane. Anzangawo amabwera ndi achibale awo komanso anthu ena omwe amafuna kuphunzira Baibulo ndipo nthawi zambiri amandiuza kuti ndikambirane nawo. Nthawi zina mabanja amabwera kudzacheza nane komanso kuti tipangire limodzi kulambira kwa pabanja. Ndimasangalala kwambiri makamaka ana aang’ono akakhala pafupi ndi bedi langa n’kumandiuza chifukwa chimene amakondera Yehova.

akuchita kulambira kwapabanja ndi anzake

Ndimayamikira kwambiri anthu amene amabwera kudzacheza nane. Nthawi zambiri m’chipinda mwanga mumakhala anthu ambiri ndipo ena amakhala ochokera kutali. Anthu amene amandisamalira kumene ndimakhalaku amachita chidwi kwambiri ndi chikondi chimene ndimasonyezedwa. Ndimathokoza Yehova tsiku lililonse chifukwa chondipatsa mwayi wokhala m’gulu la anthu ogwirizanali.

PANG’ONOPANG’ONO

Munthu akandifunsa kuti ‘mukupezako bwanji?’ Ndimangoyankha kuti, “Pang’onopang’ono.” Ndikudziwa kuti pali anthu enanso amene ali ndi mavuto. Ndipo kaya zinthu zili bwanji pamoyo wathu, Akhristu tonse tikumenya “nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro.” (1 Timoteyo 6:12) Kodi n’chiyani chomwe chandithandiza kuti ndizichitabe khama kwa zaka zambiri ngakhale kuti ndili ndi mavuto? Tsiku lililonse ndimapemphera kwa Yehova ndipo ndimamuthokoza chifukwa chondithandiza kuzindikira kuti moyo wanga uli ndi tsogolo labwino. Ndimayesetsanso kutumikira Mulungu mwakhama ndiponso kuganizira zinthu zabwino zomwe ndikuyembekezera.

José María

Nthawi zambiri ndimaganizira za dziko latsopano komanso mmene ndidzasangalalire ndikadzayambiranso kudumpha ndi kuthamanga. Ndimakonda kuchita nthabwala ndi mnzanga uja José María, yemwe panopa akudwala poliyo. Ndimamufunsa kuti, titadzachita mpikisano wothamanga m’dziko latsopano, ukuganiza kuti ndani angadzawine? Iye amandiyankha kuti: “Zowinazo zilibe ntchito. Chofunika kwambiri n’kudzakhala m’dziko latsopano n’kumatha kuthamanga.”

Si zinali zophweka kuti ndivomereze vuto langali. Ndinazindikira kuti chibwana chimalandadi. Koma ndikusangalala kwambiri kuti Yehova sananditaye m’malo mwake wandichitira zambiri. Mwachitsanzo, wandipatsa a Mboni anzanga ambirimbiri omwe amandikonda ngati m’bale wawo ndipo ubale umenewu sudzatha. Wandipatsanso mwayi wophunzitsa anthu za iye ndiponso wandilonjeza zinthu zabwino mtsogolo. Mwachidule ndinganene kuti Yehova wandichitira zazikulu.