Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

Kupemphera N’kothandiza Kwambiri

Kupemphera N’kothandiza Kwambiri

Aliyense asanayambe kuchita chinachake, amayamba kaye waganizira phindu lomwe angapeze. Kodi n’kulakwa kufunsa ngati pemphero lilidi lothandiza? Ayi sikulakwa. Ngakhalenso Yobu anafunsapo kuti: “Nditamuitana, kodi angandiyankhe?”—Yobu 9:16.

M’nkhani zapitazi, taona kuti pemphero si mwambo chabe wa chipembedzo kapena njira yongothandiza kuti munthu apezeko bwino. Mulungu woona amamvetsera komanso kuyankha tikamapemphera mogwirizana ndi zimene amafuna. Ndipotu amafuna kuti tikhale anzake. (Yakobo 4:8) Ndiye kodi tikamapemphera nthawi zonse, tingapeze phindu lanji? Tiyeni tikambirane zinthu zingapo zomwe zingatithandize kudziwa kuti kupemphera si kutaya nthawi.

Kukhala ndi mtendere wamumtima.

Aliyense akakumana ndi mavuto enaake, amakhala ndi nkhawa. Ndiye zikatere, Baibulo limanena kuti ‘tizipemphera mosalekeza’ komanso kuti ‘zopempha zathu zizidziwika kwa Mulungu.’ (1 Atesalonika 5:17; Afilipi 4:6) Baibulo limasonyeza kuti ngati titapemphera kwa Mulungu, ‘mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima ndi maganizo athu.’ (Afilipi 4:7) Choncho tikamauza Atate wathu wakumwamba nkhawa zathu, timakhala ndi mtendere wamumtima. Lemba la Salimo 55:22 limasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti tizichita zimenezi. Limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”

“Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”—Salimo 55:22

Anthu ambiri amene amatsatira malangizo amenewa amaona kuti zimenezi n’zoona. Mayi wina wa ku South Korea, dzina lake Hee Ran, anati: “Ngakhale kuti panopa ndikukumana ndi mavuto aakulu, ndimamvako bwino ndikapemphera kwa Mulungu. Ndimakhala ngati ndatula chimtolo cholemera n’kupezanso mphamvu zondithandiza kupirira.” Mayi winanso wa ku Philippines, dzina lake Cecilia, ananena kuti: “Ndimada nkhawa ndikamaganizira za mayi anga omwe ndi achikulire kwambiri ndipo satha kundizindikira. Ndimadanso nkhawa ndikaganizira mmene ndingalerere ana anga. Koma kupemphera kwa Mulungu kumandithandiza kuti ndisamangoganizira kwambiri za mavuto angawa. Ndimadziwa kuti Yehova andithandiza.”

Kupirira ukamakumana ndi mayesero.

Kodi mukuvutika kwambiri maganizo kapena mukukumana ndi mavuto ena oopsa kwambiri? Ndi bwino kupemphera kwa Mulungu “amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” ndipo maganizo anu angakhalenso m’malo. (2 Akorinto 1:3, 4) Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu atavutika maganizo kwambiri, “anagwada ndi kuyamba kupemphera” ndipo kenako “mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:41, 43) Munthu wina amene anavutikapo maganizo ndi Nehemiya. Anthu oipa sankafuna kuti Nehemiya agwire ntchito ya Mulungu ndipo anayamba kumuopseza. Nehemiya anapemphera kwa Mulungu kuti: “Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.” Zimene zinachitika pambuyo pake zimasonyeza kuti Mulungu anamuthandizadi kuti asakhale ndi mantha ndipo anapitiriza kugwira ntchito yake. (Nehemiya 6:9-16) Bambo wina wa ku Ghana, dzina lake Reginald, ananena kuti: “Ndimati ndikapemphera makamaka pa nthawi imene ndapanikizika kwambiri, ndimamva bwino. Ndimaona kuti ndafotokoza mavuto anga kwa munthu amene angathedi kundithandiza komanso kundilimbitsa mtima. Zikatero ndimaona kuti palibe chifukwa chokhaliranso ndi nkhawa.” Choncho tikamapemphera, Mulungu adzatithandiza komanso kutilimbikitsa.

Mulungu amatipatsa nzeru.

Zinthu zina zomwe timasankha zimakhudza tsogolo lathu komanso la anthu a m’banja lathu. Ndiye tingatani kuti tizisankha zinthu mwanzeru? Baibulo limati: “Ngati wina akusowa nzeru [makamaka pa nthawi ya mayesero], azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” (Yakobo 1:5) Tikapempha nzeru kwa Mulungu, adzatithandiza ndi mzimu wake woyera kuti tisankhe zinthu mwanzeru. Ndipotu tingathe kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake woyera chifukwa Yesu ananena kuti: “Atate wakumwamba . . . adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.

“Nthawi zonse ndinkapemphera kwa Yehova kuti anditsogolere komanso kuti ndizisankha bwino zochita.”—Kwabena wa ku Ghana

Ngakhalenso Yesu ankapemphera kwa Atate wake kuti amuthandize kusankha zochita. Baibulo limanena kuti pamene Yesu ankafuna kusankha atumwi ake 12, “anachezera kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.”—Luka 6:12.

Anthu enanso masiku ano, aonapo Mulungu akuyankha mapemphero awo n’kuwathandiza kusankha zinthu mwanzeru. Mwachitsanzo mayi wina wa ku Philippines, dzina lake Regina, amakumana ndi mavuto ambiri. Anachotsedwa ntchito, mwamuna wake anamwalira komanso amavutika kulera ana ake. N’chiyani chimamuthandiza kusankha zinthu mwanzeru komanso kupirira mavutowa? Mayiyu ananena kuti: “Ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize.” Bambo wina wa ku Ghana, dzina lake Kwabena, nayenso amakonda kupemphera kwa Mulungu. Anati: “Ndinkagwira ntchito ya zomangamanga ndipo ndinkalandira malipiro abwino, koma kenako basi ndinachotsedwa ntchito. Nthawi zonse ndinkapemphera kwa Yehova kuti anditsogolere komanso kuti ndizisankha bwino zochita. Ndimaona kuti Yehova anandithandiza kuti ndiphunzire ntchito yomwe imandipatsa mpata wochita zinthu zauzimu komanso nthawi yochita zomwe ndikufuna.” Inunso mungachite bwino kumapemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru komanso kuchita zimene amafuna.

M’nkhaniyi takambirana mfundo zochepa zomwe zatithandiza kuona kuti kupemphera n’kofunika kwambiri. (Onani mfundo zina pabokosi la mutu wakuti: “Kodi Pemphero Ndi Lothandiza Bwanji?”) Nanunso mukhoza kuona kuti pemphero ndi lothandiza ngati mutadziwa bwino Mulungu komanso zimene amafuna. Ngati mungakonde, mungapemphe wa Mboni za Yehova aliyense kuti azikuphunzitsani Baibulo. * Ndipo kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mukhale bwenzi la Mulungu amene ndi “Wakumva pemphero.”—Salimo 65:2.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri, funsani a Mboni za Yehova a kudera lanulo, kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.ps8318.com/ny.