Chipilala Chakale cha ku Iguputo Chili Ndi Umboni wa Nkhani ya M’Baibulo
Chipilala chokhala ndi zithunzi cha mamita 8 mukuchionachi, chili pafupi ndi khomo lolowera kukachisi wakale wa ku Iguputo wa mulungu wotchedwa Amuni ku Kanaki. Akatswiri amanena kuti zithunzizi zimasonyeza Farao Sisaki akugonjetsa mayiko a kumpoto chakummawa kwa Iguputo, kuphatikizapo Yuda ndi ufumu wakumpoto wa Isiraeli.
Zithunzizi zikusonyeza Amuni akupereka akapolo oposa 150 kwa Sisaki, yemwe ankatchedwanso kuti Sheshonk. a Kapolo aliyense akuimira umodzi mwa mizinda kapena mtundu wa anthu omwe anagonjetsedwa. Ndipo mayina a mizindayo analembedwa pa zinthu zozungulira zomwe zili pathupi la kapolo aliyense. Mayina ambiri omwe analembedwa pa zithunzizi amawerengekabe bwinobwino mpaka pano, ndipo ena ndi odziwika bwino m’Baibulo. Ena mwa mayinawa ndi Beti-seani, Gibeoni, Megido komanso Sunemu.
Nkhani yoti Aiguputo anaukira Yuda imapezekanso m’Baibulo. (1 Mafumu 14:25, 26) Ndipotu Baibulo limafotokoza mwatsatanetsatane zimene Sisaki anachita poukira Yuda. Limanena kuti: “M’chaka chachisanu cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki mfumu ya Iguputo anabwera kudzaukira Yerusalemu. . . . Anabwera ndi magaleta 1,200 ndi amuna okwera pamahatchi 60,000. Anabweranso ndi anthu osawerengeka kuchokera ku Iguputo. . . . Sisakiyo analanda mizinda ya Yuda yomwe inali ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo pamapeto pake anafika ku Yerusalemu.”—2 Mbiri 12:2-4.
Kuwonjezera pa zithunzi za ku Kanaki, palinso maumboni ena akale osonyeza kuti Sisaki anaukira dziko la Isiraeli. Mwachitsanzo, pa chidutswa cha chipilala chachikumbutso chomwe chinapezeka mumzinda wa Megido, panalembedwanso dzina lakuti “Sheshonk.”
Nkhani ya m’Baibulo yosonyeza kuti Sisaki anagonjetsa Yuda ndi umboni wakuti anthu omwe analemba Baibulo anali oona mtima. Iwo analemba moona mtima zokhudza nkhondo zimene anapambana komanso zimene analuza. Komatu anthu ambiri olemba mbiri yakale, salemba zinthu moona mtima chonchi.
a Dzinali linalembedwa kuti “Sisaki” m’Baibulo potengera mmene amalitchulira m’Chiheberi.