KHALANI MASO
Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Mwana Wanu?—Mmene Baibulo Lingathandizire Makolo
Achinyamata ambiri akusokonekera maganizo ndipo malo ochezera a pa intaneti ndi amene akuchititsa kwambiri zimenezi.”—Dr. Vivek Murthy, dokotala wamkulu wa maopaleshoni ku America, New York Times, June 17, 2024.
Kodi makolo angateteze bwanji ana awo ku mavuto amene amabwera chifukwa chogwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti? Baibulo limapereka malangizo othandiza.
Zimene makolo angachite
Ganizirani mfundo za m’Baibulo izi.
“Wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.”—Miyambo 14:15.
Poganizira mavuto omwe amabwera chifukwa chogwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, musamakakamizike kulola mwana wanu kuti azigwiritsa ntchito malowa. Musafulumire kumulola kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, mpaka atakula ndithu moti akhoza kumatsatira malamulo omwe munamuikira okhudza kuchuluka kwa nthawi yomwe angamalowe pamalowa, kusankha bwino anthu ocheza nawo komanso kupewa zinthu zosayenera.
Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?” komanso yakuti “Kuphunzitsa Mwana Wanu Wachinyamata Kukhala Wosamala Pogwiritsa Ntchito Intaneti.”
“Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu”—Aefeso 5:16.
Ngati mwalola mwana wanu kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, muzimuikira malamulo oti azitsatira ndipo muzimufotokozera mmene malamulowo angamutetezere. Muzichita chidwi ndi mmene mwanayo akuchitira zinthu. Ngati wayamba khalidwe lina lachilendo, zingasonyeze kuti akufunika kuti asamagwiritse ntchito kwambiri malo ochezera a pa intaneti.
Gwiritsani ntchito vidiyo yamakatuni yakuti Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti kuti muthandize mwana wanu kudziwa chifukwa chake tiyenera kudziletsa tikamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.
Phunzirani Zambiri
Baibulo limanena kuti tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1-5) Koma limaperekanso malangizo othandiza kwambiri. Nkhani zoposa 20 zomwe zili ndi malangizo ochokera m’Baibulo othandiza makolo ndi ana awo zingapezeke pa nkhani iyi yonena zokhudza kuvutika maganizo kwa achinyamata.