Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 112

Yehova Ndi Mulungu Wamtendere

Yehova Ndi Mulungu Wamtendere

(Afilipi 4:9)

  1. 1. M’lungu wachikondi

    Mwalonjeza mtendere.

    Mutipatse mzimu wanu

    Uzitithandizabe.

    Chikhulupiriro

    Chimatithandizadi

    Kuti tikhale anzanu.

    Tilidi pamtendere.

  2. 2. Timamvetsa zinthu,

    Timaona kuwala.

    Mumatitsogolera

    M’dziko lomwe ndi lamdima.

    Nthawi idzafika

    Pomwe nkhondo zidzatha.

    Dalitsani khama lathu

    Tikhale amtendere.

  3. 3. Mulitu ndi gulu

    Kumwamba ndi padziko,

    Lomwe ndi logwirizana

    Lolengeza Ufumu.

    Mu Ufumu wanu

    Simudzakhala nkhondo.

    Tidzakhala mwamtendere

    Padziko mpaka kale.