Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 70

Fufuzani Anthu Oyenerera

Fufuzani Anthu Oyenerera

(Mateyu 10:​11-​15)

  1. 1. Ambuye wathu anatisonyeza

    Njira yolalikirira.

    ‘Fufuzani anthu oyenerera

    Ofuna kumva choonadi.

    Muziwapatsa moni eni nyumba

    Ndi kuwafunira mtendere.

    Ngati sanakulandireni

    Sansani fumbi m’mapazi muchoke.’

  2. 2. Onse amene akulandirani

    Alandiranso Ambuye.

    Athandizeni kudziwa Yehova

    Ngati ali oyenerera.

    Musadere nkhawa zoti munene,

    Yehova akuthandizani.

    Mawu anu akakhala okoma,

    Ofatsa adzasangalala.