Zochitika Zapadera

ZOCHITIKA ZAPADERA

Anthu Anasangalala Kwambiri Pamsonkhano wa M’chilankhulo cha Chitagalogi ku Rome

Ku Europe kuli a Mboni za Yehova ambiri amene amalankhula Chitagalogi ndipo msonkhano wa masiku atatuwu unali woyamba kuchitika m’chilankhulo chawo.

ZOCHITIKA ZAPADERA

Anthu Anasangalala Kwambiri Pamsonkhano wa M’chilankhulo cha Chitagalogi ku Rome

Ku Europe kuli a Mboni za Yehova ambiri amene amalankhula Chitagalogi ndipo msonkhano wa masiku atatuwu unali woyamba kuchitika m’chilankhulo chawo.

Mwambo wa Omaliza Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Giliyadi ya Nambala 138

Ophunzirawo anachita mwambowu pa 14 March, 2015. Onse amene anabwera pamsonkhanowu analimbikitsidwa kuti apitirize kuphunzira za Yehova komanso azitsatira chitsanzo cha Yesu.

Lipoti la Msonkhano Wapachaka​—October 2014

Msonkhano wapachaka wosaiwalika wokumbukira kuti patha zaka 100 Ufumu wa Mesiya ukulamulira.

Akuluakulu a Mzinda wa Atlanta Analandira a Mboni za Yehova ndi Manja Awiri

Akuluakulu a mzinda analandira anthu ochokera m’mayiko 28 omwe ankadzachita msonkhano mumzindawu. Misonkhano itatu inachitikira mumzindawu mwezi wa July ndi wa August 2014.

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi—Kalasi Nambala 137

Kuyambira mu 1943, Sukulu ya Giliyadi yathandiza anthu ambiri kumudziwa bwino Mulungu. Onani zimene zinachitika pamwambowu.

Zimene Zinachitika pa Msonkhano Wapachaka​—October 2014

Anthu ambiri anapezeka pa msonkhano wa nambala 130 womwe bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania limachita chaka chilichonse. Onerani zimene zinachitika pa msonkhanowu womwenso ankakumbukira kuti Ufumu wakwanitsa zaka 100 ukulamulira.

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi ya Nambala 137 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Anthu onse amene anafika pamwambowu analimbikitsidwa kuti apitirize kukhala odzichepetsa komanso kuika maganizo a Yehova m’mitima mwawo.

Bungwe Lolamulira linalimbikitsa a Mboni ku Russia ndi ku Ukraine

Anthu a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anapita kukalimbikitsa a Mboni omwe anakhudzidwa ndi mavuto a zandale ku Russia ndi ku Ukraine

Zimene Zinachitika pa Msonkhano Wapachaka​—October 2013

Onani zinthu zosangalatsa zimene zinachitika pa msonkhano wapachaka umene unalumikizidwa pa vidiyo ya pa Intaneti, m’malo 1,830 kuzungulira dziko lapansi.

Mwambo wa Omaliza Maphunziro ku Giliyadi, Kalasi Nambala 135

Sukuluyi imaphunzitsa anthu a Mboni za Yehova amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali kuti azigwira ntchito yolalikira mwaluso kwambiri.

Vidiyo ya pa Intaneti Ikuthandiza Kwambiri

Kodi zinatheka bwanji kuti anthu oposa 1.4 miliyoni a m’mayiko 31 amvetsere msonkhano wapaderawu?

Mwambo wa Omaliza Maphunziro ku Giliyadi, Kalasi Nambala 136

Pa mwambowu panali nkhani zauzimu, kufunsa mafunso anthu amene anamaliza maphunziro komanso zitsanzo zosonyeza zinthu zimene zinkawachitikira mu utumiki wa kumunda.

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 136 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Aphunzitsi a kusukuluyi komanso anthu ena amene anakamba nkhani pamwambawo analimbikitsa ophunzirawo kuti akhale ndi mtima ngati wa Yesu. Anthu amene anafika pamwambowu anasangalala kwambiri chifukwa ena mwa ophunzirawo anafunsidwa mafunso, anachita zitsanzo zosonyeza zimene anakumana nazo mu utumiki.

Lipoti la Msonkhano Wapachaka​—October 2013

Anthu oposa 1.4 miliyoni anamvetsera msonkhano wosaiwalikawu m’mayiko okwana 31. Pamsonkhanowu panatulutsidwa Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi limene lakonzedwanso.

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 135 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Pa September 14, 2013, anthu oposa 10,000 anasonkhana pa mwambo wosangalatsa umenewu. Werengani nkhani yokhudza mwambowu.

Msonkhano Wapadera ku Israel

Mgwirizano wochititsa chidwi wa anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana unaonekera mu 2012 ku Tel Aviv, m’dziko limene kwa zaka zambiri, anthu akhala akudana chifukwa chosiyana mitundu ndi zipembedzo.

Msonkhano Wapadera ku Ireland

A Mboni za Yehova ku Dublin m’dziko la Ireland, analandira alendo ochokera m’mayiko ena amene anabwera ku Msonkhano Wapadera wa mu 2012, umene unali ndi mutu wakuti ‘Tetezani Mtima Wanu!’ Onani zimene ena ananena zokhudza msonkhano umenewu.

A Mboni za Yehova Anachita Misonkhano Yachigawo Yapadera M’mayiko 7

Chaposachedwa, a Mboni za Yehova anachita misonkhano yachigawo yapadera ku Brazil, Costa Rica, Hong Kong, Ireland, Israel, New Zealand ndi ku Sweden.

Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo—Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 134

Ophunzira a m’kalasi nambala 134 a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo anamaliza maphunziro awo pa March 9, 2013. Pamwambowu panakambidwa mfundo zosonyeza mmene sukuluyi ikuthandizira pa ntchito yolalikira kuchokera pamene anaitsegulira zaka 70 zapitazo.

Msonkhano wa “Padziko Lonse Lapansi”

Zaka 50 zapitazo, anthu 583 a Mboni za Yehova anayamba ulendo wa milungu 10 woyenda padziko lonse lapansi.