Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Albania ndi ku Kosovo

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Albania ndi ku Kosovo

 Gwen amene kwawo ndi ku England, anafotokoza mmene anamvera atadzipereka kukalalikira ku Albania * kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Iye ananena kuti: “Sindinkaganizirako kuti ndingachite zambiri potumikira Yehova.”

 Gwen ali m’gulu la Amboni ambiri omwe anasamukira ku Albania kukathandiza nawo pantchito yosonkhanitsa “zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu.” (Hagai 2:7) Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kuti adzipereke? Anasintha zinthu ziti kuti akwanitse kusamuka? Nanga apeza madalitso otani omwe awathandiza kupirira ngakhale kuti akhala akukumana ndi mavuto?

Cholinga chimodzi koma zochitika pa moyo zosiyana

 Ofalitsa onse omwe anabwera kudzathandiza nawo pantchito yolalikira ku Albania, cholinga chawo ndi chofanana. Iwo amakonda Yehova ndipo amafuna kuthandiza anthu ena kuti amudziwe.

 Koma asanasamuke, anasintha zinthu zina pa moyo wawo kuti awonjezere utumiki wawo ndipo zimenezi zinawathandiza kuti akwanitse kupirira mavuto omwe amakhalapo ukamatumikira kudziko lachilendo. Gwen ananena kuti: “Choyamba ndidakali kwathu, ndinayamba kusonkhana ndi kagulu kolankhula Chiabeniya. Kenako ndinapita ku msonkhano wachigawo ku Albania. Patapita nthawi, ndinabwererakonso ndipo ndinakakhalako kwa nthawi kuti ndikaphunzire bwinobwino chilankhulocho.”

Gwen

 Manuela yemwe ali ndi zaka 23 ndipo kwawo ndi ku Italy, anasamukira ku dera lina m’dziko lakwawo lomwelo kuti akathandize mpingo wina waung’ono. Iye ananena kuti: “Ndinatumikira kumeneko kwazaka 4. Kenako ndinamva kuti ku Albania kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Choncho ndinaganiza zopita ku Albania kukachita upainiya kwa miyezi ingapo.”

Manuela (Pakati)

 Federica anali ndi zaka 7 zokha pomwe anamva lipoti la ku Albania pamsonkhano wachigawo. Iye anati: “M’bale amene ankapereka lipotilo ananena kuti ofalitsa a ku Albania ankachititsa maphunziro a Baibulo ambiri ndipo anthu achidwi ankabwera kumisonkhano. Ndinauza makolo anga kuti ndikufuna kupita ku Albania. Zomwe ndinanenazi zinawadabwitsa ndipo bambo anga anandiuza kuti, ‘Uipempherere nkhani imeneyi, ndipo ngati ndi zomwedi Yehova akufuna, akuyankha.’ Patatha miyezi yowerengeka, banja lathu linaitanidwa kuti likatumikire ku Albania.” Tsopano patha zaka zambiri ndipo pano Federica anakwatirana ndi Orges. Onse awiri akutumikira ku Albania ngati atumiki a nthawi zonse.

Orges ndi Federica

 Gianpiero atapuma pantchito, anasamukira ku Albania limodzi ndi mkazi wake Gloria. Iye ananena kuti: “Ana athu onse 5 anakulira ku Italy. Kenako atatu mwa anawa anapita kukatumikira kumayiko ena komwe kunkafunika olalikira ambiri. Tinakhudzidwa mtima ndi nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yamutu wakuti ‘Kodi Mungawolokere ku Makedoniya?’ Tinaganizira mmene tingagwiritsire ntchito ndalama zanga za penshoni kuti tikatumikire ku Albania.”

Gianpiero ndi Gloria

Anakonzekera Mokwanira

 Anthu omwe akufuna kusamukira kumene kukufunika olalikira ambiri, amafunika kukonzekera mokwanira kudakali nthawi komanso kusintha zina ndi zina kuti akwanitse kusamukira kudera latsopano. (Luka 14:28) Pa zinthu zingapo zomwe angachite, ayenera kuganizira mmene angapezere ndalama zokwanira zoti azikagwiritsa ntchito. Adakali ku England, Gwen amene tamutchula kale uja, anaganiza zosamuka nyumba yomwe ankakhala kuti azikakhala ndi mkulu wake n’cholinga choti asungire ndalama. Sophia ndi Christopher omwenso ndi a ku England ananena kuti: “Tinagulitsa galimoto ndi katundu wathu wina. Tinkayembekezera kuti tikakhala ku Albania kwa pafupifupi chaka chimodzi.” Koma ndi zosangalatsa kuti anakhala ku Albania kwa nthawi yaitali.

Christopher ndi Sophia

 Ofalitsa ena amapita ku Albania kwa miyezi yochepa kenako amabwereranso kwawo kukagwira ntchito ndi kusungira ndalama. Pambuyo posungira ndalama amabwereranso ku Albania. Zimenezi ndi zomwe anachitanso Eliseo ndi Miriam. Eliseo ananena kuti: “Miriam amachokera kudera lina la ku Italy komwe kumafika alendo ambiri ndipo kupeza ntchito za kanthawi kochepa sikuvuta. Timatha kukagwira ntchito kwa miyezi itatu ndi kupeza ndalama zomwe timakagwiritsa ntchito kwa miyezi ina 9 tikabwerera ku Albania. Izi ndi zomwe takhala tikuchita kwa zaka 5.”

Miriam ndi Eliseo

Kulimbana ndi Mavuto

 Ofalitsa omwe asamukira kumadera omwe kukufunika olalikira mbiri, ayenera kuzolowera moyo watsopano. Koma chitsanzo cha Akhristu anzawo omwe ndi nzika za kumeneko chingawathandize kupirira. Sophia amene tamutchula kale ananena kuti: “M’nyengo yozizira, ku Albania kumazizira kwambiri kuposanso mmene zimakhalira kwathu. Ndinaphunzira kuvala zovala zomwe alongo akuno amavala.” Grzegorz ndi mkazi wake Sona omwe kwawo ndi ku Poland, amatumikira m’tawuni yokongola ya Prizren kuti Kosovo. * Grzegorz ananena kuti: “Abale ndi alongo akuno ndi odzichepetsa, okoma mtima komanso oleza mtima. Akutiphunzitsa chilankhulo cha kuno ndi zinthu zina. Mwachitsanzo anatiuza za mashopu momwe mumapezeka zinthu zotchipa komanso anatiuza zomwe tingamachite tikafuna kukagula zinthu kumsika.”

Zifukwa Zambiri Zotichititsa Kukhala Osangalala

 Omwe amasamukira ku mayiko ena amapindula chifukwa amakhala paubwenzi wolimba ndi Akhristu anzawo omwe ndi nzika za dzikolo komanso amadziwa bwino chikhalidwe chawo. Sona anafotokoza kuti: “Ndaona mmene chikondi cha Yehova chimasinthira moyo wa anthu. Chikhulupiriro changa chalimba kwambiri nditaona mmene abale asinthira moyo wawo komanso zomwe ankakhulupirira ataphunzira za Yehova. Taona kuti tili ndi udindo woti tiukwaniritse mumpingo. Timatumikira limodzi ndi abale ndi alongo athu omwe pano ndi anzathu kwambiri.” (Maliko 10:29, 30) Gloria ananena kuti: “Ndikudziwa za alongo ambiri omwe anapirira pa nthawi yomwe ankatsutsidwa mwankhanza ndi anthu a m’dera lawo omwe ankadana ndi Amboni. Zimandilimbikitsa kwambiri ndikaona mmene amakondera Yehova.”

Grzegorz ndi Sona

 Anthu omwe anasamukira kumadera omwe kukufunika olalikira ambiri, aphunzira zinthu zofunika zomwe mwina sakanatha kuzidziwa ali kwawo. Mwachitsanzo, awona kuti munthu amene amasiya moyo womwe anauzolowera ndi cholinga chochita zambiri potumikira Yehova amakhala wosangalala. Stefano anafotokoza kuti: “Nthawi zambiri, kwathu ndinkangolalikira mwachidule pa intakomu. Koma anthu a ku Albania kuno amakonda kucheza kwambiri kwinaku akumwa khofi. Munthune ndi wamanyazi kwambiri, ndiye poyamba zinkandichititsa manyazi ndipo sindinkadziwa choti ndichite. Komabe, pamene nthawi inkapita, ndinayamba kuchita chidwi ndi anthu ndipo pano ndimasangalala ndikamacheza nawo. Utumiki wanga ndikuwumva kukoma.”

Alida ndi Stefano

 Leah ndi mwamuna wake William anasamuka ku United States kupita ku Albania. Leah anati: “Kutumikira kuno kwatithandiza kudziwa chikhalidwe cha anthu ena komanso mmene amaganizira. Taphunzira kukhala ochereza, kusonyeza anthu ena ulemu komanso zomwe tingachite kuti tizigwirizana ndi ena. Taphunzira njira zina zolalikirira, kukambirana mfundo za m’Malemba komanso kufotokoza zomwe timakhulupirira.” William anafotokoza kuti: “Anthu ambiri omwe amabwera ku Albania kuno amachita chidwi ndi magombe okongola. Koma ine ndimakonda kukayenda m’mapiri. Komabe chinthu chachikulu chomwe ndimakukondera kuno, ndi mmene anthu ake alili. Anthu ambiri m’midzi yakuno amalalikidwa mwachidule pa ntchito yapadera pokha. Tikapita kolalikira, nthawi zina ndimakhala tsiku lathunthu ndikucheza ndi mabanja angapo.”

William ndi Leah

 Chinthu chachikulu chomwe chimasangalatsa Akhristu omwe anapita ku madera omwe kukufunika olalikira ambiri, ndikuona anthu akuchita chidwi ndi uthenga wabwino. (1 Atesalonika 2:19, 20) Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Laura, anasamukira ku Albania ndipo ananena kuti: “Ndinatumikira m’tauni ya Fier kwa zaka ziwiri ndi hafu basi. Koma pa anthu 120 omwe anabwera m’gulu la Yehova panthawi imeneyi, ine ndinathandizapo anthu 16.” Mlongo wina dzina lake Sandra ananena kuti: “Ndinalalikira mzimayi wina yemwe ankagwira ntchito mumsika. Patapita nthawi anabatizidwa ndipo anabwereranso kumudzi kwawo. Ulendo womwe ndinakumana naye, anandiuza kuti ali ndi maphunziro a Baibulo okwana 15.”

Laura

Sandra

Yehova Anawadalitsa Chifukwa cha Kupirira Kwawo

 Olalikira Ufumu ena omwe anasamukira ku Albania zaka zingapo zapitazo, adakali komweko ndipo akusangalala kwambiri ndi utumiki wawo. Nthawi zina amadabwa kuona kuti anthu ena omwe anawalalikirapo nthawi ina m’mbuyomu, pano akutumikira Yehova. Christopher amene tamutchula kale, ananena kuti: “Ndinakumana ndi bambo wina amene ndinkaphunzira naye Baibulo nditangofika kuno ku Albania. Ndinachita chidwi atafotokoza mwatsatanetsatane zomwe tinakambirana paulendo woyamba womwe ndinkamulalikira. Panopo, iye limodzi ndi mkazi wake ndi atumiki a Yehova obatizidwa.” Federica amene tamutchula kale ananena kuti: “Kumpingo wina, ndinakumana ndi mlongo wina yemwe anandifunsa ngati ndinkamukumbukira. Anandiuza kuti ndinamulalikirapo zaka 9 m’mbuyomo. Nditasamukira ku tauni ina, anayamba kuphunzira Baibulo mpaka kubatizidwa. Ndinkalakwitsa kuganiza kuti chaka chathu choyamba ku Albania sitinachiteko chilichonse chaphindu.”

 Abale ndi alongo omwe anasamukira ku Albania kapena ku Kosovo amathokoza kwambiri Yehova poona mmene wawadalitsira pa khama lomwe anasonyeza komanso powathandiza kukhala ndi moyo wabwino. Pofika pano, Eliseo wakhala ku Albania kwa zaka zambiri, ndipo mwachidule ananena kuti: “Anthufe timapusitsidwa n’kumaganiza kuti tikhoza kukhala ndi moyo wabwino kwambiri tikamadalira zinthu zomwe dzikoli limati ndiye moyo wotsogola. Koma sizikhala zoona. Mfundo za Yehova ndi zomwe zimatithandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino. Utumiki womwe ndikuchita ku Albania wandithandiza kuzindikira zimenezi. Utumikiwu wandithandiza kudziona kuti ndine wofunika. Ndapeza anzanga abwino omwe tonse cholinga chathu ndi chimodzi.” Sandra nayenso anavomereza kuti: “Nditasamukira kumene kukufunika olalikira ambiri, ndinaona kuti Yehova wandipatsa mwayi wogwira ntchito ngati mmishonale, ntchito yomwe ndinkailakalaka kwa nthawi yaitali. Sindinong’oneza bondo kuti ndinabwera ku Albania chifukwa ndimakhala wosangalala kwambiri.”

^ Dziwani zambiri zokhudza mmene ntchito yolalikira yakhala ikuyendera ku Albania powerenga Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2010.

^ Dziko la Kosovo lili kumpoto chakum’mawa kwa Albania. Anthu ambiri ku Kosovo, amalankhula Chiabeniya. Amboni a ku Albania, ku mayiko angapo a ku Europe komanso a ku United States, anadzipereka ndi mtima wonse kuti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu okhala ku Kosovo omwe amalankhula Chiabeniya. Pofika mu 2020, ku Kosovo kunali ofalitsa okwana 256 omwe anali m’mipingo 8, m’magulu atatu komanso m’timagulu tating’ono tiwiri.