Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 9, 2016
ARMENIA

Gulu Loyamba la Mboni za Yehova ku Armenia Lamaliza Kugwira Ntchito Zimene Linapatsidwa Litakana Kulowa Usilikali

Gulu Loyamba la Mboni za Yehova ku Armenia Lamaliza Kugwira Ntchito Zimene Linapatsidwa Litakana Kulowa Usilikali

Gulu loyamba la achinyamata a Mboni za Yehova limene linavomerezedwa kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali, layesetsa kugwira ntchitozo mokhulupirika ndiponso mwakhama. Pasanabwere gulu limeneli, panali gulu linanso la achinyamata a Mboni limene linakana usilikali ndipo linalamulidwa kuti likakhale kundende. Ndiyeno mu 2013, dziko la Armenia linakonzanso malamulo ake ndipo linayamba kuvomereza anthu amene akana kulowa usilikali kuti azipatsidwa ntchito zina. Panopa, a Mboni oposa 200 avomerezedwa kuti angathe kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Pofika mu June 2016, a Mboni okwana 16 anali atamaliza kugwira ntchito zimene anapatsidwa.

Dongosolo Loti Anthu Amene Akana Kulowa Usilikali Azipatsidwa Ntchito Zina Likuyenda Bwino

Achinyamata a Mboni oyambirira omwe amaliza kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali, poyamba anawatsekera m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikaliwo. Lamulo latsopano lovomereza kugwira ntchito zina litakhazikitsidwa, achinyamatawo anauzidwa kuti akagwire ntchito zinazo. Pofika mu January 2014, iwo anali atayamba kugwira ntchito monga kudzala kapinga ndi maluwa, kusesa m’misewu, kuthandizira ogwira ntchito m’zipatala ndi ntchito zina.

Achinyamata amene amaliza kugwira ntchitowo, akuthokoza boma chifukwa chowalola kugwira ntchito zimene zapindulitsadi anthu, monga kusamalira ovutika komanso kukongoletsa malo osiyanasiyana. Chifukwa cha dongosolo limeneli, achinyamata amene amaliza ntchito zimene apatsidwa amakhala anthu odalirika m’madera awo ndipo amakhala ndi mbiri yabwino.

Davit Arakelyan yemwe ali ndi zaka 22, anamaliza kugwira ntchito yomwe anapatsidwa yothandizira ma nesi osamalira okalamba. Iye anati: “Ntchitoyi yandithandiza kukhala munthu wopanda chibwana, wodalirika komanso wakhama. Ndikusangalala kuti ndinagwira ntchito imene ndinapatsidwa ndi boma ndipo ndinathandiza anthu. Anthu amene ndinkagwira nawo ntchito kumaloko kuphatikizaponso anthu ena a m’deralo, anayamikira ntchito yomwe tinagwira.” Mikhayil Manasyan, yemwenso ali ndi zaka 22 ndipo anapatsidwa ntchito ku unduna woona zinthu zogwa mwadzidzidzi, ananena kuti: “Kugwira ntchito ndi undunawu kwandithandiza kuti ndiphunzire luso latsopano limene ndikhoza kumaligwiritsa ntchito kuti ndizipeza zofunika pa moyo wanga. Ndikusangalala kuti ndagwira ntchito imene ndinapatsidwa ndi boma yomwenso sikutsutsana ndi zomwe ndimakhulupirira.”

Kodi Zimene Lachita Dziko la Armenia Zithandizanso Mayiko Ena Kuti Azipereka Ntchito Zina Kwa Anthu Omwe Akana Usilikali?

Posachedwapa, dziko la Armenia lachitapo kanthu pokonzanso malamulo ake n’cholinga chakuti malamulowo azipereka ufulu kwa anthu omwe akana usilikali. Gawo 41 ndime 3 la malamulo atsopanowo, omwe anayamba kugwira ntchito mu December 2015, limati: “Aliyense amene ndi nzika ya dziko lino ndipo sakufuna kugwira ntchito ya usilikali chifukwa cha chipembedzo chake kapena zimene amakhulupirira, azipatsidwa ufulu wogwira ntchito zina.” Komiti Yoona za Malamulo ya Bungwe la Mayiko a ku Ulaya inayamikira dziko la Armenia chifukwa chochita zimenezi ndipo inati “imeneyi ndi njira yabwino yotetezera chigamulo chomwe chinaperekedwa pa mlandu wa pakati pa a Bayatyan ndi Dziko la Armenia.”    a

Zimene dziko la Armenia lachita pokhazikitsa dongosolo loti amene sakufuna usilikali azigwira ntchito zina, n’zogwirizana ndi mfundo zimene mayiko ambiri amayendera. Dzikoli, lomwe poyamba linkapereka chilango kwa anthu amene akukana kulowa usilikali, panopo limalemekeza ufulu umene anthuwo ali nawo wotsatira zimene amakhulupirira. Panopo dzikolo lapindula kwambiri chifukwa cha ntchito zimene anthuwo amagwira ndipo ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa mayiko ena amene amalanga anthu omwe akana usilikali. Zimene zachitika ku Armenia ndi umboni wakuti kukhazikitsa dongosololi kungathandize kwambiri boma komanso nzika zake.

Poyankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Armenia, bambo Tigran Harutyunyan ananena kuti: “Ndife osangalala chifukwa chakuti dziko la Armenia lachitapo kanthu pofuna kuteteza maufulu osiyanasiyana amene anthu ali nawo, zomwe zikuphatikizapo ufulu wokana kugwira ntchito ya usilikali. Panopo achinyamata a Mboni ku Armenia angathe kugwira ntchito zimene sizikusemphana ndi zomwe amakhulupirira ndipo ntchitozo zimathandiza anthu ambiri.”

a Chigamulo cha mlandu wa pakati pa a Bayatyan ndi Dziko la Armenia ([GC], no. 23459/03, ECHR 2011) chomwe chinaperekedwa ndi Khoti Lalikulu Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya chinali chosaiwalika. Imeneyi inali nthawi yoyamba kuti khotili ligamule kuti gawo 9 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya limateteza ufulu wa anthu amene akana kulowa usilikali. Gawo 9 limanena kuti munthu ali ndi ufulu wonena maganizo ake, ufulu wotsatira zimene amakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza.