Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 22, 2017
AUSTRIA

Akuluakulu a Tauni Ina ku Austria Anachita Mwambo Wokumbukira a Mboni 31 Omwe Anazunzidwa Komanso Kuphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi

Akuluakulu a Tauni Ina ku Austria Anachita Mwambo Wokumbukira a Mboni 31 Omwe Anazunzidwa Komanso Kuphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi

Meya wa ku Techelsberg, a Johann Koban (pakati), akuvundukula nsalu pa chikwangwani cha chikumbutso limodzi ndi a Peter Stocker (kumanja) komanso Dr. Peter Kaiser (kumanzere) omwe ndi gavanala wa ku Carinthia.

SELTERS, Germany—M’mawa pa 19 May 2017, akuluakulu a boma a m’tauni ya Techelsberg ku Austria, anachita mwambo wokumbukira a Mboni za Yehova omwe anaphedwa kapena kuikidwa m’ndende ndi a chipani cha Nazi. Pamwambowu anavundukula nsalu pa chikwangwani cha chikumbutso cha a Mboni 31 omwe “anazunzidwa m’tauni ya Techelsberg komanso m’madera ena ozungulira.”

Mwambowu unayamba pomwe anthu 60 anayimba nyimbo yakuti “Pitani Patsogolo Mboninu” ndipo poimba nyimboyi sanagwiritse ntchito zida zilizonse. Nyimboyi inapekedwa ndi a Erich Frost omwe anali a Mboni za Yehova. A Frost anaikidwa m’ndende ndi a chipani cha Nazi pa nthawi ya Nkhondo Yachiwiri Ya Padziko Lonse. Nyimbo yakuti “Pitani Patsogolo Mboninu,” imaimbidwabe nthawi zambiri pamisonkhano ya Mboni za Yehova yomwe imachitika padziko lonse. Atangomaliza kuimba nyimboyi, a Johann Koban omwe ndi meya wa ku Techelsberg, a Peter Stocker (mdzukulu wa a Gregor Wohlfahrt Sr., omwenso anazunzidwa nawo pa nthawiyo), Pulofesa Peter Gstettner, Pulofesa Vinzenz Jobst komanso Dr. Peter Kaiser (gavanala) analankhula kwa anthu pafupifupi 350 omwe anapezeka pamwambowu. Nyumba zofalitsa nkhani za ORF 2 ndi ORF Kärnten komanso ofalitsa nkhani ena, anaulutsa zomwe zinachitika pamwambowu.

Pulofesa Peter Gstettner akulankhula kwa anthu omwe ali pamwambowu.

Pa a Mboni 550 omwe anali ku Austria pa nthawi ya Nkhondo Yachiwiri, a Mboni 212 anaikidwa m’ndende chifukwa boma la Germany linkawaona ngati oukira. Ankawaganizira kuti ndi oukira chifukwa choti ankakana kuchita nawo za ndale komanso kulowa usilikali. Kundendeko a Mboni ankakakamizidwa kuti aziika kansalu kapepo ka makona atatu pa mayunifolomu awo, kuti aziwazindikira mosavuta. Pa nthawiyi a Mboni 154 a ku Austria anaphedwa.

Mwambowu usanachitike, maina a anthu 5 a Mboni a m’tauni ya Techelsberg omwe anaphedwa ndi a chipani cha Nazi, (Johann Stossier, Anton Uran, Gregor Wohlfahrt, Sr., Gregor Wohlfahrt, Jr. ndi Willibald Wohlfahrt) analembedwa pa chikwangwani cha chikumbutso ngati “anthu omwe anasowa” pa nthawi ya nkhondo. Pulofesa Gstettner ananena za kufunika kwa mwambowu ponena kuti: “Chikwangwani cha chikumbutsochi chathandiza kuti chilungamo chidziwike. Komanso yakhala ngati njira yokumbukirira anthu omwe anasonyeza kulimba mtima ndi kukhulupirika pa zomwe ankakhulupirira. Zikusonyezanso kuti sikulakwa ngati munthu akukana kuchita zimene anthu ankhanza akumukakamiza kuchita. Ndipo a Mboniwa anasonyeza kuti anapambana.”

Chikwangwani cha ku Techelsberg chokumbukira a Mboni za Yehova 31 amene anaphedwa, kuikidwa m’ndende, kapena kuzunzidwa ndi a chipani cha Nazi pa nthawi ya Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse. Pachikwangwanichi palinso ndakatulo yomwe analemba a Franz Wohlfahrt (onani bokosi m’munsimu) komanso mayina a anthu 5 a Mboni a ku Techelsberg omwe poyamba anawaika pa mndandanda wa “anthu omwe anasowa” pa nthawi ya nkhondo.

A Johann Zimmermann omwe ndi wolankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Austria ananena kuti: “Tikuthokoza kwambiri chifukwa chokhazikitsa mwambowu womwe ukusonyeza kuti akuluakulu a boma akudziwa za kulimba mtima komanso chikhulupiriro chomwe a Mboni za Yehova anasonyeza ngakhale kuti ankazunzidwa koopsa. Sitikukayikira kuti mwambowu uthandizanso anthu ena kuzindikira kuti ngati atamangoganizira kuti kagulu kenakake ndi koukira boma, zingachititse kuti kaguluko kazichitiridwa zinthu zankhanza.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Austria: Johann Zimmermann, +43-1-804-53-45

Germany: Wolfram Slupina, +49-6483-41-3110