12 JULY 2024
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Anthu Ambiri Akhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Beryl
Pa 30 June 2024, Mphepo yamkuntho yotchedwa Beryl inadutsa kum’mwera kwa chilumba cha Martinique ku West Indies. Tsiku lotsatira, mphamvu za mphepoyo zinawonjezereka ndipo inawomba komanso kuwononga zinthu m’dera la Windward Islands, lomwe likuphatikizapo ku Barbados, Grenada, Saint Vincent komanso ku Grenadines. Tsiku lotsatira, inawombanso mwamphamvu kwambiri ku Venezuela. Kenako mphepoyi anadutsa m’mbali mwa doko lakum’mwera kwa Jamaica. Pa 5 July, mphepo yamphamvuyi inadutsa ku Yucatán ku Mexico isanawononge kum’mwera kwa United States.
Mphepoyi inkathamanga liwiro la makilomita 270 pa ola ndipo kulikonse komwe inkadutsa kunkagwa chimvula komanso inawononga nyumba, mabizinesi ndi zinthu zina. Mpaka pano, anthu mamiliyoni angapo omwe akukhala m’madera okhudzidwawa alibe magetsi, madzi komanso zinthu zina zofunika. Malipoti akusonyeza kuti anthu oposa 30 anaphedwa.
Mmene Mphepo Yamkunthoyi Yakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Martinique (West Indies)
Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala
Ofalitsa 6 anasamuka m’nyumba zawo
Nyumba imodzi inawonongedweratu
Nyumba imodzi inawonongedwa kwambiri
Nyumba imodzi inawonongedwa pang’ono
Palibe Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongedwa
Windward Islands
Palibe m’bale kapena mlongo wathu yemwe anaphedwa
Ofalitsa 7 anavulala
Ofalitsa 67 anasamuka m’nyumba zawo
Nyumba 39 zinawonongedwa kwambiri
Nyumba 31 zinawonongedwa pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongedweratu
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongedwa kwambiri
Nyumba za Ufumu 4 zinawonongedwa pang’ono
Venezuela
Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala
Ofalitsa 30 anasamutsidwa m’nyumba zawo
Nyumba 12 zinawonongedwa kwambiri
Nyumba 9 zinawonongedwa pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongedwa kwambiri
Jamaica
Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala
Ofalitsa 18 anasamutsidwa m’nyumba zawo
Nyuma 24 zinawonongedwa kwambiri
Nyumba 75 zinawonongedwa pang’ono
Nyumba za Ufumu 19 zinawonongedwa pang’ono
Mexico
Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa kapena kuvulala
Ofalitsa 320 anasamutsidwa koma tsopano anabwerera kunyumba zawo
Nyumba 11 zinawonongedwa pang’ono
Palibe Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongedwa
United States
Palibe m’bale kapena mlongo wathu amene anaphedwa
Ofalitsa 6 anavulala
Ofalitsa 242 anasamutsidwa
Nyumba 4 zinawonongedweratu
Nyumba 33 zinawonongedwa kwambiri
Nyumba 471 zinawonongedwa pang’ono
Palibe Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongedwa
Ntchito Yopereka Chithandizo
Oyang’anira madera komanso akulu akuthandiza anthu onse okhala m’madera okhudzidwawa powalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwathandiza m’njira zina. Kuwonjezera pamenepa, Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi okwana 6 anakhazikitsidwa kuti aziyang’anira ntchito yopereka thandizo.
Pemphero lathu ndi lakuti Yehova apitirize kutonthoza onse omwe akumudalira pa nthawi yovutayi.—2 Akorinto 1:3, 4.