Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Italy

 

2019-11-05

ITALY

Ku Italy Kunachitika Mwambo Wokumbukira a Mboni za Yehova Omwe Anazunzidwa ndi Chipani cha Nazi

Mwambo wokumbukira a Mboni za Yehova masauzande omwe anazunzidwa ndi chipani cha Nazi kumayiko a ku Europe unachitikira pa Risiera di San Sabba mumzinda wa Trieste ku Italy.

2019-08-14

ITALY

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Italy Lagamula Kuti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wopanga Zosankha pa Nkhani ya Chithandizo Chamankhwala

Chigamulo chaposachedwapa chinapereka ufulu kwa abale athu wopanga zosankha pa nkhani yokhudza chithandizo chamankhwala chomwe akufuna.

2019-08-30

ITALY

Madokotala ku Italy Anasonyeza Chidwi pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi

Misonkhano iwiri imeneyi inathandiza kuti akatswiri ambiri azachipatala adziwe njira zatsopano zokhudza kuthandiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi. Komanso, madokotala opanga maopaleshoni anafotokozera abale ndi alongo zinthu zabwino zomwe akhala akukumana nazo akamagwira ntchito ndi a Mboni za Yehova.

2018-09-27

ITALY

Khoti la ku Sicily Linagamula Kuti Odwala Omwe Ndi a Mboni za Yehova Ali Ndi Ufulu Wosankha Chithandizo cha Mankhwala

Aka ndi koyamba kuti khoti ku Italy ligamule kuti dokotala ndi wolakwa chifukwa chophwanya ufulu womwe munthu aliyense ali nawo wosankha zomwe ziyenera kuchitika pa thupi lake mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.

2018-09-27

ITALY

Kufunsa a Luca P. Weltert, M.D.

“Taona kuti pali kusintha kwakukulu chifukwa chochepetsa kugwiritsa ntchito magazi pothandiza odwala ndipo zimenezi sizinakhudze odwala a Mboni okha, koma zakhudzanso dziko lonse lapansi chifukwa pali maumboni ochuluka osonyeza kuti kuchepetsa kugwiritsa ntchito magazi kuli ndi zotsatira zabwino kwambiri.”

2018-07-09

ITALY

Msonkhano Wofunika Kwambiri Wokambirana Zimene Zachitika pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi Unachitikira ku Yunivesite ya Padua

Anthu akhala akukhulupirira kuti kuika munthu magazi kulibe vuto lililonse ndipo ndi njira yokhayo yopulumutsira moyo wa anthu omwe adwala kwambiri kapena omwe akufunika kupangidwa opaleshoni. Koma anthu ambiri omwe anayankhula pamsonkhanowu, sanagwirizane ndi maganizo amenewa.

2018-07-09

ITALY

Kufunsa a Pulofesa Antonio D. Pinna, M.D.

“Ndikuganiza kuti kukana magazi chifukwa cha chipembedzo si vuto. Palinso odwala ena amene safuna kuikidwa magazi koma si a Mboni.”