Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 23, 2018
ITALY

Msonkhano Wofunika Kwambiri Wokambirana Zimene Zachitika pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi Unachitikira ku Yunivesite ya Padua

Msonkhano Wofunika Kwambiri Wokambirana Zimene Zachitika pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi Unachitikira ku Yunivesite ya Padua

ROME—Lachisanu pa 24 November, 2017, madokotala, oona zinthu zoyenera ndi zosayenera pa nkhani ya zamankhwala, komanso akatswiri a zamalamulo, anakumana pa Yunivesite ya Padua yomwe ndi imodzi mwa mayunivesite akale kwambiri ku Italy kuti apange msonkhano womwe mutu wake unali woti “Kodi Pali Njira Ziti Zothandizira Odwala Akuluakulu Omwe Akana Kuikidwa Magazi?—Kupulumutsa Magazi mu 2017.” Unduna wa Zaumoyo ku Italy komanso mabungwe a sayansi oposa 25 a ku Italy ndi amene anapereka thandizo loyendetsera msonkhanowu.

Dr. Luca P. Weltert

Anthu akhala akukhulupirira kuti kuika munthu magazi kulibe vuto lililonse ndipo ndi njira yokhayo yopulumutsira moyo wa anthu omwe adwala kwambiri kapena omwe akufunika kupangidwa opaleshoni. Koma anthu ambiri omwe anayankhula pamsonkhanowu, sanagwirizane ndi maganizo amenewa. Mmodzi mwa akatswiri omwe anali pamsonkhanowu, a Dr. Luca P. Weltert, omwe amapanga maopaleshoni aziwalo zapachifuwa pa European Hospital ku Rome, anati: “Msonkhano walerowu watithandiza kuzindikira kuti kuika munthu magazi n’koopsa ndipo nthawi zambiri kumakhala kosafunika.”

Madokotala enanso omwe anali pamsonkhanowu anagwirizana ndi zimene a Weltert ananenazi. Iwo anagwirizana ndi mfundoyi potengera zimene akhala akukumana nazo pothandiza odwala komanso zimene kafukufuku wina wasayansi anapeza kuti odwala ambiri omwe aikidwa magazi amamwalira, amadwala matenda ena, amakhala nthawi yayitali m’chipatala, komanso amapezeka ndi mavuto ena aakulu. *

“Msonkhano walerowu watithandiza kuzindikira kuti kuika munthu magazi n’koopsa ndipo nthawi zambiri kumakhala kosafunika.”—Dr. Luca P. Weltert, omwe amapanga maopaleshoni aziwalo zapachifuwa pa European Hospital ku Rome

Zimene asayansi anapezazi, komanso kuchuluka kwa ndalama zomwe zimagwiritsidwa ntchito pa nkhani yoika anthu magazi, zinachititsa kuti mu 2010 Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse lipeze njira yothandiza kugwiritsira ntchito bwino magazi a odwala. Bungweli linaona kuti, kuti zimenezi zitheke, pakufunika kuti akatswiri osiyanasiyana pa nkhani zaumoyo azigwira ntchito limodzi komanso azigwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pothandiza odwala, zomwe cholinga chake ndi kuteteza moyo wa odwala, kuthandiza kuti ntchito yopanga maopaleshoni iziyenda bwino kwambiri, komanso kuchepetsa kwambiri kuika anthu magazi akamathandizidwa. Kenako bungweli linauza mayiko onse 193 omwe ndi mamembala a bungwe la United Nations kuti ayambe kutsatira njira zosiyanasiyana zothandiza kugwiritsa bwino ntchito magazi a odwala.

Pulofesa Stefania Vaglio

Pofotokoza zokhudza njira yatsopano yogwiritsa ntchito bwino magazi a odwala, Pulofesa Stefania Vaglio, yemwe ndi mkulu woona za kuika anthu magazi pa chipatala cha Sant’Andrea University ku Rome, ananena kuti poyamba kuthandiza odwala kunkadalira kugwiritsa ntchito magazi amene anthu ena apereka, koma panopa “odwala akuthandizidwa pogwiritsa ntchito magazi awo omwewo.” Cholinga chimodzi chogwiritsira ntchito njira yogwiritsa ntchito bwino magazi a odwala ndi “kuchepetsa kutaika kwa magazi pochita zinthu mosamala kwambiri pothandiza wodwalayo,. . . mwa kukhala tcheru komanso kuchita chilichonse chofunika n’cholinga chofuna kupulumutsa magazi a wodwalayo.” Pulofesa Vaglio ananenanso kuti njira yopulumutsa magazi a wodwala pamene wodwalayo akuthandizidwa, “ndi yothandiza kuti wodwalayo alandire thandizo labwino kwambiri.”

Dr. Campagnaro, omwe amachita maopaleshoni osiyanasiyana pachipatala cha Verona University, anatsimikizira kuti kugwiritsa ntchito njira zosaika munthu magazi n’kothandiza. Atamaliza kuunika zomwe zinachitika pamene odwala ena ankachitidwa maopaleshoni ovuta kwambiri a m’mimba kuyambira chakumapeto a zaka za m’ma 1990, anati: “Panali mavuto ochepa popanga opaleshoni odwala omwe sanaikidwe magazi komanso chiwerengero cha omwalira chinali chochepa, kusiyana ndi odwala omwe anaikidwa magazi.”

“Panali mavuto ochepa popanga opaleshoni odwala omwe sanaikidwe magazi komanso chiwerengero cha omwalira chinali chochepa, kusiyana ndi odwala omwe anaikidwa magazi.”—Dr. Tommaso Campagnaro, omwe amachita maopaleshoni osiyanasiyana pachipatala cha Verona University

Wachiwiri kwa Pulofesa a Anna Aprile

Dr. Campagnaro komanso anthu ena ambiri amene anayankhula pamsonkhanowu, anayamikira a Mboni za Yehova pamaso pa anthu onse chifukwa chochititsa madokotala kuti apeze njira zothandizira odwala popanda kuwaika magazi. Wachiwiri kwa pulofesa wa za malamulo a zachipatala pa Yunivesite ya Padua, a Anna Aprile anati: “Tikuyamikira a Mboni za Yehova chifukwa choyambitsa nkhani ya ufulu wokana kuikidwa magazi, ndipo zimenezi zithandiza aliyense kuti aganizire nkhaniyi komanso kuti tizitha kuthandiza odwala pogwiritsa ntchito magazi ochepa.”

“Tikuyamikira a Mboni za Yehova chifukwa choyambitsa nkhani ya ufulu wokana kuikidwa magazi . . .”—Anna Aprile, wachiwiri kwa pulofesa wa za malamulo a zachipatala pa Yunivesite ya Padua

Anthu omwe analankhula pamsonkhanowu anali akatswiri ochita zinthu zosiyanasiyana zachipatala monga zokhudza kugonetsa munthu popanga opaleshoni, zokhudza mtima, matenda a azimayi okhudza ziwalo zoberekera, zamagazi, zotupa komanso zamafupa. Komabe, uthenga waukulu kwambiri pamsonkhanowu unali wofanana, womwe unali woti mabungwe azachipatala, opanga malamulo, komanso anthu onse ayenera kumagwiritsa ntchito njira yogwiritsira ntchito bwino magazi a wodwala poganizira zimene zafalitsidwa pa nkhaniyi komanso zimene akatswiri azachipatala akhala akukumana nazo pogwira ntchito yawo.

Anthu omwe anapezeka pamsonkhano wa ku Yunivesite ya ku Padua akumvetsera zinthu zina zomwe zikufotokozedwa pamsonkhanowu.

Dr. Weltert anawonjezeranso kuti: “Kupanga opaleshoni yong’amba mtsempha waukulu kwambiri wa mtima, ndi opaleshoni yaikulu kwambiri imene ingachitike m’thupi mwa munthu. . . . Ndiye ngati opaleshoni imeneyi imatha kuchitika popanda kuika munthu magazi, zikutanthauza kuti n’zotheka kupanga opaleshoni iliyonse popanda kumuika munthu magazi.”

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Italy: Christian Di Blasio, +39-06-872941

^ ndime 4 Mwachitsanzo, zotsatira za kafukufuku wina waposachedwapa amene anachitikira ku Western Australia, zomwenso zinatulutsidwa m’magazini ina yodziwika bwino yofotokoza za kuika anthu magazi, zinatchulidwanso pamsonkhano wa ku Padua. Olemba kafukufukuyu anafotokoza zotsatira zomwe anapeza pa ntchito yaikulu yokhazikitsa njira yabwino yothandizira odwala pogwiritsa bwino ntchito magazi a odwalawo yomwe inatenga zaka 6. Anaunika zotsatira za odwala okwana 605,046 omwe anagonekedwa ku zipatala 4 zosamalirako akuluakulu omwe akufunika kuthandizidwa mwapadera. Pa nthawi yochita kafukufukuyu, njira zogwiritsa ntchito magazi pothandiza odwala zinachepa ndi 41 peresenti. Pa nthawi yomweyinso, chiwerengero cha odwala omwe ankamwalira chinachepa ndi 28 peresenti, ndipo nthawi yomwe odwala ankakhala m’chipatala inachepa ndi 15 peresenti, pomwe chiwerengero cha odwala amene ankatengera matenda m’chipatala momwemo chinachepa ndi 21 peresenti komanso chiwerengero cha anthu omwe ankadwala matenda a mtima ndi matenda oumitsa ziwalo chinachepa ndi 31 peresenti. Choncho kuyamba kutsatira njira yogwiritsa ntchito bwino magazi a odwala kunathandiza kuti odwala ambiri asamamwalire, magazi asamagwiritsidwe ntchito kwambiri pothandiza odwala, komanso kuti ndalama zisamawonongeke zambiri.