Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Pushpa Ghimire (kumanzere) ndi Mlongo Tirtha Maya Ghale (kumanja) amangidwa ndi unyolo umodzi. Pa nthawiyi n’kuti akuyembekezera kuti atulutsidwe m’ndende ku Nepal pa 4 November, 2019

NOVEMBER 15, 2019
NEPAL

A Mboni za Yehova Awiri Osalakwa Atulutsidwa M’ndende Poyembekezera Apilo ku Nepal

A Mboni za Yehova Awiri Osalakwa Atulutsidwa M’ndende Poyembekezera Apilo ku Nepal

Pa 4 November, 2019, alongo awiri omwe mayina awo ndi: Tirtha Maya Ghale komanso Pushpa Ghimire anatulutsidwa m’ndende poyembekezera kaye apilo ya mlandu wawo. Khoti linagamula kuti akhale m’ndende kwa miyezi itatu ndipo anali atakhalamo kwa mwezi wosachepera umodzi. Alongowa anamangidwa chifukwa cholambira Mulungu ngakhale kuti umenewu ndi ufulu wovomerezeka ndi boma la Nepal komanso ndi malamulo a m’mayiko ena.

Mu November 2018, Mlongo Ghale ndi Mlongo Ghimire anamangidwa chifukwa chouza anthu achidwi mfundo za m’Baibulo mumsewu. Atakhala m’ndende kwa masiku 13, alongowa anatulutsidwa pabelo pamtengo wokwera kwambiri wa ndalama zokwana pafupifupi madola 930 a ku America. Komabe, apolisi anapitirizabe kufufuza mlandu wokhudza alongowa.

Pa 10 December, 2018, khoti linayamba kuzenga mlandu wa alongowa ndipo linapitiriza kumvetsera mlanduwu kwa miyezi 10. Pa 25 September, 2019, khoti la m’boma la Rupandehi linagamula kuti alongowa akagwire ukaidi kwa miyezi itatu kundende ndiponso apereke chindapusa cha ndalama pafupifupi madola 23 a ku America.

Khotili linanena kuti alongowa anapalamula mlandu wokopa anthu ena kuti alowe m’chipembedzo chawo chifukwa choti anapezeka ndi mabuku achipembedzo ndiponso ankagawira anthu ena. Popeza kuti dziko la Nepal ndi membala wa bungwe la United Nations ndiponso linasaina Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale, dzikoli liyenera kuwonetsetsa kuti nzika zake zili ndi ufulu wosintha chipembedzo chawo komanso kuuza ena zimene amakhulupirira pamalo ena aliwonse. Zomwe Mlongo Ghale ndi Mlongo Ghimire anachita sikunali kukakamiza anthu kusintha chipembedzo chawo, koma ankangogawira mabuku achipembedzo kwa anthu omwe ankafuna kumvetsera. Pa chifukwa chimenechi, maloya oimira alongowa anakapanga apilo ku Khoti Lalikulu pa 31 October, 2019. Khotili linagamula kuti alongowa sakuyenera kupitiriza kukhala m’ndende pa nthawi ya apiloyi, choncho anatulutsidwa kaye poyembekezera chigamulo chomaliza cha khotili.

Tikupemphera kuti Yehova apitirize kupereka mzimu wake woyera kwa Mlongo Ghale ndi Mlongo Ghimire komanso awapatse mphamvu, chimwemwe, ndi mtendere pamene akuyembekezera chigamulo chomaliza cha khoti la apilo.—Aroma 15:13.