28 JUNE 2024
RUSSIA
Alongo Atatu Apezedwa ndi Mlandu ku Republic of Kalmykia, ku Russia
Pa 24 June 2024, khoti lamumzinda wa Elista ku Republic of Kalmykia linapeza kuti Mlongo Tsagan Khalgaeva, Mlongo Yekaterina Menkova ndiponso Mlongo Kishta Tutinova ndi olakwa. Mlongo Khalgaeva komanso Mlongo Menkova anagamulidwa kuti kwa zaka ziwiri azitsatira malamulo enaake ali panyumba. Mlongo Tutinova anagamulidwa kuti azitsatira malamulo enaake ali panyumba kwa zaka zitatu. Alongowa sakufunika kupita kundende panopa.
Zokhudza Mlongoyu
Timayamikira alongowa omwe ndi chitsanzo chabwino cha masiku ano pa nkhani yosonyeza chikhulupiriro. Timayamikiranso Yehova chifukwa amaona mayesero onse omwe timakumana nawo ndipo adzatidalitsa chifukwa chokhala okhulupirika.—Salimo 37:18.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
16 February 2023
Kishta anamutsegulira mlandu
28 February 2023
Nyumba zawo zinafufuzidwa. Kishta anatumizidwa kumalo omwe ankayembekezera kuzengedwa mlandu
1 March 2023
Tsagan anachotsedwa ntchito chifukwa ankaimbidwa mlandu woti ndi chigawenga. Kishta anatulitsidwa kumalo komwe ankamusunga poyembekezera mlandu wake ndipo anamuika pa ukaidi wosachoka panyumba
21 July 2023
Kishta anamasulidwa pa ukaidi wosachoka panyumba
19 December 2023
Yekaterina ndi Tsagan anawatsegulira mlandu. Onsewa anauzidwa kuti asamayende m’madera ena
9 February 2024
Kishta anauzidwa kuti asamayende m’madera ena
1 April 2024
Mlandu unayamba kuzengedwa
24 June 2024
Anapezedwa olakwa ndipo anagamulidwa kuti azitsatira malamulo enaake ali panyumba