Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Sergey Rayman ndi mkazi wake Valeriya, ali m’khoti pa 9 October 2020

OCTOBER 9, 2020
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Banja Lina Lachinyamata Ndi Lolakwa

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Banja Lina Lachinyamata Ndi Lolakwa

Pa 9 October 2020, khoti la m’boma la Sverdlovskiy mumzinda wa Kostroma linagamula kuti M’bale Sergey Rayman ndi mkazi wake Valeriya ndi olakwa. M’baleyu anauzidwa kuti azitsatira malamulo enaake ali kunyumba kwa zaka 8 pamene mlongoyu anauzidwa zaka 7. Zaka zimenezi ndi zochuluka kwambiri poyerekezera ndi zimene abale ndi alongo athu ku Russia akhala akugamulidwa kuchokera mu 2017, pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linaletsa ntchito zathu m’dzikolo. Panopa M’bale ndi Mlongo Rayman sakufunika kuikidwa m’ndende.