Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale ndi Mlongo Oniszczuk ali limodzi mukolido ya khoti la mumzinda wa Kirov

SEPTEMBER 6, 2019
RUSSIA

M’bale Andrzej Oniszczuk Wamasulidwa Atakhala M’ndende Yayekha kwa Miyezi 11

M’bale Andrzej Oniszczuk Wamasulidwa Atakhala M’ndende Yayekha kwa Miyezi 11

Pa 3 September, 2019, M’bale Andrzej Oniszczuk anatulutsidwa m’ndende ya ku Russia. M’baleyu anali atakhala m’ndende kuyambira pa 9 October, 2018 chifukwa cholambira Yehova. Pa nthawiyi, iye anaikidwa m’ndende yayekha ndipo sankaloledwa kuonana kapena kulankhulana ndi mkazi wake Anna. Ngakhale kuti abwerera kunyumba kwawo, a Oniszczuk analetsedwa kuchita zinthu zina ndipo zimenezi zikutanthauza kuti sangayende maulendo aatali kwambiri. Mlandu wawo udakalipobe.

Tikusangalala kuti M’bale Andrzej Oniszczuk ndi mkazi wake akupitirizabe kukhala okhulupirika pa nthawi yovutayi. Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa amayankha mapemphero onse omwe timapereka m’malo mwa anthu omwe ‘anamangidwa n’kuikidwa m’ndende.’—Akolose 4:2, 3.