Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yodzilemba Matatuu?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limanena za matatuu malo amodzi okha palemba la Levitiko 19:28 lomwe limati: “Musamadziteme zizindikiro.” Mulungu anapereka lamuloli ku mtundu wa Aisiraeli n’cholinga choti asamafanane ndi anthu a mitundu yoyandikana nayo omwe ankadzilemba pathupi lawo mayina komanso zizindikiro za milungu yawo. (Deuteronomo 14: 2) Ngakhale kuti masiku ano Akhristu satsatira Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli, mfundo ya mu lamuloli ndi yofunika kuiganizira.
Kodi n’zoyenera kuti Mkhristu adzilembe tatuu?
Malemba otsatirawa angakuthandizeni kuganizira mwakuya nkhaniyi:
“Akazi azidzikongoletsa . . . mwaulemu.” (1 Timoteyo 2:9) Mfundo imeneyi imagwira ntchito kwa akazi ndi amuna omwe. Tifunika kuganizira mmene zochita zathu zingakhudzire anthu ena m’malo momangochita zimene tikuona kuti zitisangalatsa.
Anthu ena amadzilemba matatuu n’cholinga chofuna kutchuka pamene ena amafuna kusonyeza kuti thupilo ndi lawo. Koma Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti: “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Choncho muzigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza” kuti muone chifukwa chake mukufuna kudzilemba tatuu. Ngati mukungofuna kutchuka kapena kusonyeza kuti muli m’gulu linalake, kumbukirani kuti pakadzapita nthawi maganizo amenewa adzakutherani koma matatuu amene mwadzilembawo amakhalapobe. Kuganizira mofatsa cholinga chanu kungakuthandizeni kuti musankhe zochita mwanzeru.— Miyambo 4:7.
“Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Munthu akafuna kudzilemba tatuu nthawi zambiri saganizira kaye mofatsa koma matatuuwo amapangitsa kuti munthuyo avutike kupeza anthu ocheza nawo komanso ntchito. Komanso matatuu amapweteka pochotsa ndipo pamafunika ndalama zambiri. Kafukufuku komanso anthu amene amachita malonda ochotsa anthu matatuu amasonyeza kuti anthu ambiri amene ali ndi matatuu amanong’oneza bondo kuti anadzilemba matatuu.