Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Miliri?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Miliri?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza kudzakhala miliri. Miliri ina imafalikira m’mayiko ambiri. (Luka 21:11) Sikuti miliri imeneyi ndi chilango chochokera kwa Mulungu. Ndipo Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuti athetse matenda onse kuphatikizapo miliri yomwe imafalikira m’mayiko ambiri.

 Kodi Baibulo linaneneratu za miliri?

 Baibulo silitchula mayina a miliri monga COVID-19, Edzi, TB, malungo kapena chimfine cha ku Spain. Koma linaneneratu kuti “kudzakhala miliri” ndi “mliri wakupha.” (Luka 21:11; Chivumbulutso 6:8) Miliri imeneyi ndi mbali ya chizindikiro cha “masiku otsiriza” omwe amatchedwanso “mapeto a nthawi ino.”—2 Timoteyo 3:1; Mateyu 24:3.

 Kodi Mulungu analangapo anthu ndi matenda?

 Baibulo limatchula nthawi zingapo pamene Mulungu analanga anthu pogwiritsa ntchito matenda. Mwachitsanzo, anachititsa anthu ena kudwala khate. (Numeri 12:1-16; 2 Mafumu 5:20-27; 2 Mbiri 26:16-21) Komatu imeneyi sinali miliri ndipo sinafalikire kwa anthu osalakwa. Koma chinali chilango chapadera chopita kwa anthu amene anaphwanya dala malamulo a Mulungu.

 Kodi miliri yomwe ikuchitika masiku ano ndi chilango chochokera kwa Mulungu?

 Ayi. Anthu ena amanena kuti Mulungu akugwiritsa ntchito miliri ndi matenda ena polanga anthu masiku ano. Koma zimenezi n’zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. N’chifukwa chiyani tikutero?

 Chifukwa choyamba n’chakuti matenda akhala akuvutitsa atumiki a Mulungu akale komanso amasiku ano. Mwachitsanzo, Timoteyo yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu ‘ankadwaladwala.’ (1 Timoteyo 5:23) Koma Baibulo silinena kuti iye ankadwaladwala chifukwa chakuti Mulungu sankasangalala naye. Masiku anonso, atumiki ena a Mulungu amadwala kapena kutenga matenda. Nthawi zambiri zimangochitika kuti anthuwo ali pamalo olakwika pa nthawi yolakwika.—Mlaliki 9:11.

 Ndipo Baibulo limanena kuti nthawi yoti Mulungu alange anthu ochita zoipa sinafike. Panopa tili “m’tsiku lachipulumutso,” kutanthauza nthawi imene Mulungu akuitana anthu mwachikondi kuti akhale mabwenzi ake n’cholinga choti adzapulumuke. (2 Akorinto 6:2) Njira imodzi imene akuitanira anthu ndi kuwauza uthenga wolimbikitsa kudzera mu ntchito yolalikira “uthenga wabwino . . . wa Ufumu,” yomwe ikuchitika padziko lonse.​—Mateyu 24:14.

 Kodi miliri idzatha?

 Inde. Baibulo limanena kuti posachedwapa anthu sazidzadwalanso. Mulungu adzathetsa matenda onse mu Ufumu wake. (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Iye adzachotsa mavuto onse, zopweteka, ndiponso imfa. (Chivumbulutso 21:4) Ndipo anthu amene anamwalira adzawaukitsa. Iwo adzakhala ndi moyo wabwino kwambiri padziko lapansi pompano ndipo sazidzadwalanso.—Salimo 37:29; Machitidwe 24:15.

 Mavesi a m’Baibulo onena za matenda

 Mateyu 4:23: “[Yesu] anayendayenda m’Galileya yense kuphunzitsa m’masunagoge mwawo, kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuchiritsa anthu matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.”

 Tanthauzo lake: Zinthu zodabwitsa zochepa zimene Yesu anachita zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu posachedwapa.

 Luka 21:11: “Kudzakhala miliri.”

 Tanthauzo lake: Matenda amene akufalikira padziko lonse, ndi mbali ya chizindikiro cha masiku otsiriza.

 Chivumbulutso 6:8: “Ndinaona hatchi yotuwa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa. Ndipo Manda anali kumutsatira pafupi kwambiri. Iwo anapatsidwa ulamuliro . . . kuti aphe anthu ndi . . . mliri wakupha.”

 Tanthauzo lake: Ulosi wa anthu 4 okwera pamahatchi wa m’buku la Chivumbulutso umasonyeza kuti miliri idzachitika m’nthawi yathu ino.