Kodi Chiyembekezo Ndingachipeze Kuti?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limanena kuti Mulungu akufuna kutipatsa “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.” a (Yeremiya 29:11) Ndipotu chimodzi mwa zifukwa zimene Mulungu anatipatsira Malemba, ndi choti ‘tikhale ndi chiyembekezo komanso kuti atithandize kupirira ndiponso kutilimbikitsa.’ (Aroma 15:4) Monga mmene tionere, malangizo anzeru a m’Baibulo angatithandize kuthana ndi mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Komanso zimene Baibulo limalonjeza zingatithandize kuti tiziyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino mtsogolo.
Zimene zili munkhaniyi
Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?
Baibulo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo, potisonyeza zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
Muzidalira malangizo anzeru opezeka m’Baibulo. Lemba la Salimo 119:105 limati: “Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.” Kuwala kwa mphamvu kungatithandize m’njira ziwiri. Choyamba, kungatithandize kuunikira zinthu zimene zili patsogolo pathu. Ndipo chachiwiri, kungatithandize kuunikira zinthu zomwe zili patali. Mofanana ndi zimenezi, mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuthana ndi mavuto amene tikukumana nawo panopa ndipo zimenezi zingathandize kuti tsiku lililonse tizikhala ndi chiyembekezo. Zimene Baibulo limaphunzitsa zingatithandize kuti tikhalenso ndi mphamvu komanso zingatithandize kukhala wosangalala. (Salimo 19:7, 8) Ndiponso Baibulo limatithandiza kudziwa zimene Mulungu akufuna kudzachitira anthu komanso dziko lapansi mtsogolo. Kuyembekezera zinthu zimenezi kungatithandize kuti tizikhala osangalala.
Muzilola kuti ena akuthandizeni: Nthawi zina tikathedwa nzeru chifukwa cha mavuto, tingayambe kumadzipatula, osamafuna kucheza ndi achibale ndiponso anzathu. Koma Baibulo limanena kuti kuchita zimenezi ndi kosathandiza chifukwa kungachititse kuti tisankhe zinthu molakwika komanso mosaganiza bwino. (Miyambo 18:1) Achibale komanso anzathu angatithandize kuti tiziganiza bwino. Akhozanso kutithandiza kupeza njira zabwino zothanirana ndi vuto limene takumana nalo. (Miyambo 11:14) Komanso akhoza kutitonthoza komanso kutilimbikitsa ndipo zimenezi zingatipatse mphamvu zoti tipirire mpaka zinthu zitayambiranso kuyenda bwino.—Miyambo 12:25.
Muzipemphera kwa Mulungu. Baibulo limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” b (Salimo 55:22) Ndi pomveka kuti Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” (Aroma 15:13) Mukhoza kumuuza “nkhawa zanu zonse” muli ndi chikhulupiriro kuti akumverani, chifukwa amakuderani nkhawa. (1 Petulo 5:7) Ndipotu Baibulo limati Mulungu, “adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”—1 Petulo 5:10.
Muzilola kuti mayesero azikuthandizani kukhulupirira kwambiri zimene Mulungu walonjeza. Baibulo limalonjeza kuti munthu womvera Mulungu “adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.” (Miyambo 1:33) Nthawi ina ku Australia kutachitika mphepo yamkuntho, katundu wa mayi wina dzina lake Margaret, anawonongeka. Koma mayiyu sankangokhalira kudandaula chifukwa anazindikira kuti chuma sichikhalitsa. Kungoyambira nthawi imeneyo, anayamba kuganizira za zinthu zofunika kwambiri zomwe ndi banja lake, anzake, ubwenzi wake ndi Mulungu komanso chiyembekezo chimene chimapezeka m’Baibulo.— Salimo 37:34; Yakobo 4:8.
Kodi Baibulo limathandiza anthu kuti aziyembekezera zotani?
Baibulo limalonjeza kuti posachedwa, anthu onse adzakhala ndi tsogolo labwino komanso kuti dzikoli lidzakhala malo abwino kwambiri. Mavuto amene tikukumana nawo masiku ano ndi umboni woti tili ‘m’masiku otsiriza’ a dzikoli. (2 Timoteyo 3:1-5) Posachedwapa, Mulungu adzakonza zinthu padzikoli ndipo adzathetsa zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto onse. Iye adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito boma lomwe limatchedwa kuti Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15) Yesu ankaganizira za boma limeneli pomwe ananena mu pemphero lachitsanzo kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.
Baibulo limanena momveka bwino zimene Mulungu akufuna kudzachitira anthu. Onani mavuto ena amene Ufumu wa Mulungu udzathetse:
Sikudzakhalanso njala. “Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.”—Salimo 67:6.
Sikudzakhalanso matenda. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.
Sikudzakhalanso imfa. Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwa anthu onse], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
a Timayembekezera chinthu chimene tikuchilakalaka komanso chomwe tikukhulupirira kuti tichipeza. Chiyembekezo chikhoza kukhala chinthu chimene tikuchiyembekezera kapena chimene chikutipangitsa kuyembekezera zinazake.
b Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.—Salimo 83:18.