Kodi Tchimo N’chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Munthu amachimwa ngati akuchita kapena kuganiza zinthu zomwe Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, amachimwa ngati sanatsatire mfundo kapena malamulo a Mulungu. (1 Yohane 3:4; 5:17) Koma Baibulo limanenanso kuti munthu amachimwa akalephera kuchita zinthu zoyenera.—Yakobo 4:17.
M’zinenero zoyambirira zomwe anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, mawu akuti tchimo amatanthauza “kuphonya.” Mwachitsanzo, ku Isiraeli wakale kunali asilikali omwe ankati akaponya mwala ndi gulaye, ‘sankaphonya.’ Ngati mawuwa atamasuliridwa mmene analili m’chinenero choyamba, angalembedwe kuti ‘sankachimwa.’ (Oweruza 20:16) Choncho, tchimo lingatanthauze kuphonya kapena kuti kulephera kuchita zimene Mulungu amafuna.
Popeza Mulungu ndi amene anatilenga, iye ndi woyenera kutipatsa mfundo zoti tiziyendera. (Chivumbulutso 4:11) Choncho tidzayankha mlandu kwa Mulungu ngati titamachita zinthu zolakwika.—Aroma 14:12.
Kodi n’zotheka kupeweratu kuchita machimo?
Ayi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23; 1 Mafumu 8:46; Mlaliki 7:20; 1 Yohane 1:8) N’chifukwa chiyani zili choncho?
Poyamba Adamu ndi Hava anali anthu angwiro. Sankachimwa chifukwa analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:27) Koma kenako, iwo anakhala ochimwa chifukwa sanamvere Mulungu. (Genesis 3:5, 6, 17-19) Choncho pamene anayamba kubereka ana, anawapatsiranso uchimowo. (Aroma 5:12) N’chifukwa chake Mfumu Davide ya Isiraeli inanena kuti: ‘Ndinabadwa ndili wochimwa.’—Salimo 51:5.
Kodi machimo ena ndi aakulu kuposa ena?
Inde. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu a ku Sodomu anali “oipa, ndipo anali ochimwa kwambiri” komanso ‘tchimo lawo linali lalikulu kwambiri.’ (Genesis 13:13; 18:20) Tiyeni tione mfundo zitatu zomwe zingatithandize kudziwa ngati tchimo ndi lalikulu kapena ayi.
Mtundu wake. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipewa machimo aakulu monga chiwerewere, kulambira mafano, kuba, kuledzera, kupha munthu komanso kukhulupirira mizimu. (1 Akorinto 6:9-11; Chivumbulutso 21:8) Baibulo limasiyanitsa machimowa ndi machimo ena omwe munthu amachita mosaganizira monga kulankhula kapena kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. (Miyambo 12:18; Aefeso 4:31, 32) Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamaone tchimo lililonse kukhala laling’ono chifukwa zingachititse kuti tiyambe kuchita machimo aakulu.—Mateyu 5:27, 28.
Cholinga chake. Anthu ena amachita machimo chifukwa sadziwa zimene Mulungu amafuna. (Machitidwe 17:30; 1 Timoteyo 1:13) Baibulo silichepetsa machimo amenewa, koma limangowasiyanitsa ndi machimo amene anthu ena amachita mwadala. (Numeri 15:30, 31) Munthu amene amachita machimo mwadala amakhala ndi ‘mtima woipa.’—Yeremiya 16:12.
Kuchita mobwerezabwereza. Baibulo limasiyanitsanso munthu amene wachita tchimo kamodzi kokha ndi munthu amene amachita mobwerezabwereza. (1 Yohane 3:4-8) Mulungu adzaweruza anthu amene amachita “machimo mwadala” pambuyo poti adziwa zolondola.—Aheberi 10:26, 27.
Anthu amene anachita machimo aakulu akhoza kumva chisoni kwambiri ndi zimene anachitazo. Mwachitsanzo, Mfumu Davide inanena kuti: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.” (Salimo 38:4) Komabe Baibulo limanena kuti: “Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.”—Yesaya 55:7.