Kodi Kubadwanso Kumatanthauza Chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Mawu akuti “kubadwanso” akunena za kusintha kwa ubwenzi wa pakati pa munthuyo ndi Mulungu. (Yohane 3:3, 7) Anthu omwe abadwanso ndi amene Mulungu wayamba kuwaona kuti ndi ana ake enieni. (Aroma 8:15, 16; Agalatiya 4:5; 1 Yohane 3:1) Ubwenzi wa pakati pa anthuwo ndi Mulungu umasintha moti Mulungu amayamba kuwaona kuti ali m’banja lake.—2 Akorinto 6:18.
N’chifukwa chiyani munthu amabadwanso?
Yesu anati: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.” (Yohane 3:3) Choncho kubadwanso kumakonzekeretsa munthu kuti akalamulire ndi Khristu mu Ufumu wa Mulungu. Ufumuwu umalamulira kuchokera kumwamba ndipo n’chifukwa chake Baibulo limanena kuti anthu amene ‘amaberekedwa mwatsopano’ amalandira ‘cholowa chimene anawasungira kumwamba.’ (1 Petulo 1:3, 4) Mulungu amathandiza anthu amene abadwanso kudziwa kuti ‘adzalamulira limodzi ndi Khristu monga mafumu’ ndipo anthuwa sakayikira zimenezi.—2 Timoteyo 2:12; 2 Akorinto 1:21, 22.
Kodi munthu amabadwanso bwanji?
Yesu ananena kuti anthuwo amabadwanso “mwa madzi ndi mzimu.” (Yohane 3:5) Mawuwa akutanthauza kuti anthuwo amabatizidwa m’madzi ndipo kenako ndi mzimu woyera.—Machitidwe 1:5; 2:1-4.
Yesu anali munthu woyamba kubadwanso. Iye anabatizidwa mumtsinje wa Yorodano ndipo kenako Mulungu anamudzoza (kapena kuti kumubatiza) ndi mzimu woyera. Choncho Yesu anabadwanso n’kukhala mwana wauzimu wa Mulungu ndipo ankayembekezera kudzabwerera kumwamba. (Maliko 1:9-11) Mulungu anakwaniritsa zimene Yesu ankayembekezerazi pomuukitsa kuti akhale ndi thupi lauzimu.—Machitidwe 13:33.
Anthu enanso amene amabadwanso amabatizidwa kaye m’madzi asanalandire mzimu woyera. a (Machitidwe 2:38, 41) Akabadwanso amayembekezera kuti adzapita kumwamba ndipo Mulungu amakwaniritsa zimenezi powaukitsa.—1 Akorinto 15:42-49.
Maganizo olakwika amene anthu ali nawo okhudza kubadwanso
Maganizo olakwika: Munthu ayenera kubadwanso kuti adzapulumuke kapena kuti akhale Mkhristu.
Zoona zake: Anthu amapulumuka chifukwa cha nsembe ya Khristu ndipo anthuwa amaphatikizapo amene anabadwanso omwe akalamulire ndi Khristu kumwamba komanso anthu amene adzakhale padzikoli n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu. (1 Yohane 2:1, 2; Chivumbulutso 5:9, 10) Akhristu amene ali m’gulu lachiwirili ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli.—Salimo 37:29; Mateyu 6:9, 10; Chivumbulutso 21:1-5.
Maganizo olakwika: Munthu angasankhe yekha kubadwanso kapena ayi.
Zoona zake: Aliyense ali ndi mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndiponso wopulumuka. (1 Timoteyo 2:3, 4; Yakobo 4:8) Koma Mulungu ndi amene amasankha anthu oti abadwenso kapena kuti adzozedwe ndi mzimu woyera. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kuti munthu abadwenso “sizidalira munthu wofunayo . . . koma Mulungu.” (Aroma 9:16) Mawu akuti “kubadwanso” akhoza kumasuliridwanso kuti “kubadwa kuchokera kumwamba.” Izi zikutsimikizira kuti Mulungu ndi amene amasankha anthu oti abadwenso.—Yohane 3:3.
a Anthu okhawo amene analandira mzimu woyera asanabatizidwe ndi Koneliyo ndi anthu amene anali naye basi.—Machitidwe 10:44-48.