Kodi Manambala Otchulidwa M’Baibulo Amaimira Chiyani? Nanga Kukhulupirira Manambala N’kogwirizana ndi Mfundo za M’Baibulo?
Yankho la m’Baibulo
Kawirikawiri manambala otchulidwa m’Baibulo saimira chilichonse, koma nthawi zina angaimire zinthu zina. Nthawi zambiri nkhani imene mukupezeka nambala inayake m’Baibulo ingatithandize kudziwa ngati nambalayo ikuimira zinthu zinazake. Taonani zitsanzo zotsatirazi zosonyeza manambala amene amaimira zinthu zapadera m’Baibulo:
1 Mgwirizano. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti otsatira ake akhale ogwirizana. Iye anati: “Onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana.”—Yohane 17:21; Mateyu 19:6.
2 Pa milandu pamafunika kukhala mboni ziwiri kuti anthu atsimikizire kuti nkhani inayake ndi yoona. (Deuteronomo 17:6) Komanso, munthu ankati akaona masomphenya kawiri, kapena nkhani inayake ikabwerezedwa kawiri, zinkatsimikizira kuti n’zoonadi. Mwachitsanzo, pamene Yosefe ankamasulira maloto a Farao, ananena kuti: “Popeza kuti inu mwalota kawiri malotowa, ndiye kuti Mulungu woona watsimikiza mtima kuchitadi zimenezi.” (Genesis 41:32) Mogwirizana ndi ulosi, “nyanga ziwiri” zingaimire ulamuliro wopangidwa ndi mafumu awiri ogwirizana. Ndipotu izi n’zimene mneneri Danieli anauzidwa ponena za ufumu wa Mediya ndi Perisiya.—Danieli 8:20, 21; Chivumbulutso 13:11.
3 Pa mlandu pakakhala mboni zitatu zotsimikizira nkhani inayake, zinkachititsa kuti anthu asakayikire ngakhale pang’ono kuti umboni wawowo ndi woona. Mofanana ndi zimenezi, mawu enaake akatchulidwa katatu, zimatsimikizira kuti mawuwo ndi oonadi.—Ezekieli 21:27; Machitidwe 10:9-16; Chivumbulutso 4:8; 8:13.
4 Nambala imeneyi imaimira mbali zonse za chinthu, monga mmene mawu akuti “m’makona anayi a dziko lapansi” akusonyezera.—Chivumbulutso 7:1; 21:16; Yesaya 11:12.
6 Panambalayi pakuperewera chinthu chimodzi kuti ikwane 7, ndipo nambala ya 7 nthawi zambiri imaimira chinthu chokwanira. Choncho 6 angaimire chinthu chosakwanira kapena chopanda ungwiro, kapenanso chinthu chinachake chokhudzana ndi adani a Mulungu.—1 Mbiri 20:6; Danieli 3:1; Chivumbulutso 13:18.
7 Kawirikawiri nambala imeneyi imagwiritsidwa ntchito poimira chinthu chokwanira. Mwachitsanzo, Mulungu analamula Aisiraeli kuti azungulire mzinda wa Yeriko kwa masiku 7 otsatizana, ndipo pa tsiku la 7, anawauza kuti azungulire mzindawo maulendo 7. (Yoswa 6:15) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza mmene nambala ya 7 anaigwiritsira ntchito. (Levitiko 4:6; 25:8; 26:18; Salimo 119:164; Chivumbulutso 1:20; 13:1; 17:10) Yesu anatchula nambala ya 7 mobwereza pamene anauza Petulo kuti azikhululukira m’bale wake “osati nthawi 7 zokha ayi, koma, Mpaka nthawi 77.” Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti tizikhululukira ena popanda malire.—Mateyu 18:21, 22.
10 Nambala imeneyi imaimira chinthu chathunthu kapena zinthu zonse.—Ekisodo 34:28; Luka 19:13; Chivumbulutso 2:10.
12 Zikuoneka kuti nambala imeneyi ikuimira gulu lokwanira limene Mulungu wakonza. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane anaona masomphenya akumwamba a mzinda womwe unali ndi “miyala yomangira maziko yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12.” (Chivumbulutso 21:14; Genesis 49:28; Chivumbulutso 4:4; 7:4-8) Komanso nambala ya 12 ikachulukitsidwa ndi nambala ina, imathanso kuimira gulu limene Mulungu wakonza.—Chivumbulutso 4:4; 7:4-8.
40 Nambalayi imagwirizana ndi nthawi imene Mulungu anapereka chiweruzo kapena chilango kwa anthu.—Genesis 7:4; Ezekieli 29:11, 12.
Kukhulupirira manambala
Zimene manambala amenewa amaimira m’Baibulo n’zosiyana ndi zimene anthu ena amakhulupirira. Anthu ena okhulupirira zamizimu amaona kuti manambala ena ali ndi matanthauzo apadera. Amakhulupiriranso kuti manambala angapo akakhala pamodzi, amatanthauza zinthu zina, ndipo akawaphatikiza amakhulupiriranso kuti amakhala ndi tanthauzo lina lapadera. Mwachitsanzo, akatswiri ena a Chiyuda amatanthauzira Malemba Achiheberi pogwiritsa ntchito manambala. Iwo amatanthauzira malembawo poona manambala amene amawafananitsa ndi zilembo. Komatu kukhulupirira manambala n’kogwirizana ndi zamizimu ndipo Mulungu sasangalala nazo.—Deuteronomo 18:10-12.