Wolembedwa na Mateyo 4:1-25

  • Mdyelekezi ayesa Yesu (1-11)

  • Yesu ayamba kulalikila ku Galileya (12-17)

  • Yesu aitana ophunzila ake oyamba (18-22)

  • Yesu alalikila, kuphunzitsa, na kucilitsa (23-25)

4  Kenako mzimu unatsogolela Yesu ku cipululu kuti akayesedwe na Mdyelekezi.  Atasala kudya kwa masiku 40 usana na usiku, anamva njala.  Kenako Woyesayo anamuyandikila n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi isanduke mitanda ya mkate.”  Koma iye anamuyankha kuti: “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale na moyo na cakudya cokha ayi, koma na mawu alionse ocokela m’kamwa mwa Yehova.’”  Kenako Mdyelekezi anamutengela ku mzinda woyela, ndipo anamukwezeka pamwamba penipeni pa* kacisi  na kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, dziponyeni pansi, cifukwa Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake za inu,’ ndipo ‘Iwo adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisagunde mwala.’”  Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amatinso: ‘Usamuyese Yehova Mulungu wako.’”  Mdyelekezi anatengelanso Yesu ku phili lalitali kwambili n’kumuonetsa maufumu onse a padziko na ulemelelo wawo.  Kenako anamuuza kuti: “Zinthu zonsezi nikupatsani mukagwada pansi na kunilambilako kamodzi kokha.” 10  Apa lomba Yesu anamuuza kuti: “Coka Satana! Cifukwa Malemba amati: ‘Yehova Mulungu wako ni amene uyenela kum’lambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’” 11  Pamenepo Mdyelekezi anamusiya, ndipo angelo anabwela na kuyamba kum’tumikila. 12  Lomba Yesu atamva kuti Yohane wamangidwa, anacoka n’kupita ku Galileya. 13  Ndiponso atacoka ku Nazareti anapita kukakhala ku Kaperenao kumbali kwa nyanja, m’madela a Zebuloni komanso Nafitali. 14  Izi zinakwanilitsa mawu amene anakambidwa kudzela mwa mneneli Yesaya akuti: 15  “Inu anthu okhala m’dziko la Zebuloni na dziko la Nafitali, m’mbali mwa msewu wopita ku nyanja, kutsidya lina la Yorodani, Galileya wa anthu a mitundu ina, 16  anthu okhala mu mdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu okhala mu mthunzi wa imfa, kuunika kunawawalila.” 17  Kucokela nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikila kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.” 18  Iye akuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya anaona amuna aŵili a pacibale, Simoni wochedwa Petulo, na Andireya m’bale wake, akuponya ukonde pa nyanja, popeza anali asodzi. 19  Ndiyeno anawauza kuti: “Nitsatileni, ndipo ine nidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20  Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatila. 21  Atacoka pamenepo, anaona amuna enanso aŵili a pacibale, Yakobo mwana wa Zebedayo na m’bale wake Yohane. Iwo anali m’bwato pamodzi na Zebedayo tate wawo akusoka maukonde awo ndipo anawaitana. 22  Nthawi yomweyo anasiya bwatolo na atate awo n’kumutsatila. 23  Kenako anazungulila m’cigawo conse ca Galileya. Iye anali kuphunzitsa m’masunagoge awo na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu, komanso kucilitsa anthu matenda a mtundu uliwonse na zofooka zilizonse. 24  Mbili yonena za iye inamveka mu Siriya yense, moti anthu anamubweletsela odwala matenda osiyana-siyana na zopweteka zina. Anamubweletselanso ogwidwa na ziŵanda, akhunyu komanso ofa ziwalo, ndipo anawacilitsa. 25  Pa cifukwa ici, makamu a anthu ocokela ku Galileya, ku Dekapoli,* ku Yerusalemu, ku Yudeya, na kutsidya lina la Yorodani anamutsatila.

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “pamwamba pa mpanda wa.”
Kapena kuti, “Cigawo ca Mizinda 10.”